Miyambo 27 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 27:1-27

1Usamanyadire za mawa,

pakuti sudziwa zimene zidzachitike pa tsikulo.

2Munthu wina akutamande, koma osati wekha;

mlendo akakutamanda, ndiponi koma osati ndi pakamwa pako.

3Mwala ndi wolemera ndipo mchenganso ndi wolemera kwambiri,

koma makani a chitsiru ndi oposa zonsezo kulemera kwake.

4Mkwiyo umadzetsa nkhanza ndipo kupsa mtima kumachititsa zoopsa.

Koma nsanje imachita zoopsa zopambana.

5Kudzudzula munthu poyera nʼkwabwino

kuposa chikondi chobisika.

6Munthu amene amakukonda ngakhale akupweteke zili bwino,

koma mdani wako amakupsompsona mwachinyengo.

7Iye amene wakhuta amayipidwa ndi chisa cha uchi,

koma kwa munthu wanjala ngakhale chimene chili chowawa chimamukomera.

8Munthu amene wasochera ku nyumba kwake,

ali monga mbalame imene yasochera pa chisa chake.

9Mafuta ndi zonunkhira zimasangalatsa mtima,

ndipo kukoma mtima kwa bwenzi kwagona pa malangizo ake.

10Usasiye bwenzi lako ndiponso bwenzi la abambo ako,

ndipo usapite ku nyumba ya mʼbale wako pamene wakumana ndi mavuto;

mnzako wokhala naye pafupi amaposa mʼbale wako wokhala kutali.

11Mwana wanga, khala wanzeru, ndipo ukondweretse mtima wanga;

pamenepo ine ndidzatha kuyankha aliyense amene amandinyoza.

12Munthu wochenjera akaona choopsa amabisala,

koma munthu wopusa amangopitirira ndipo amakumana ndi mavuto.

13Utenge chovala cha munthu amene waperekera mlendo chikole;

ngati chigwiriro chifukwa waperekera chikole mlendo wosadziwika.

14Ngati munthu apatsa mnzake moni mofuwula mmamawa kwambiri,

anthu adzamuyesa kuti akutemberera.

15Mkazi wolongolola ali ngati

mvula yamvumbi.

16Kumuletsa mkazi wotereyu zimenezi zili ngati kuletsa mphepo

kapena kufumbata mafuta mʼdzanja.

17Chitsulo chimanoledwa ndi chitsulo chinzake,

chomwechonso munthu amanoledwa ndi munthu mnzake.

18Amene amasamalira mtengo wamkuyu adzadya zipatso zake,

ndipo iye amene amasamalira mbuye wake adzalandira ulemu.

19Monga momwe nkhope imaonekera mʼmadzi,

chomwechonso mtima wa munthu umadziwika ndi ntchito zake.

20Manda sakhuta,

nawonso maso a munthu sakhuta.

21Siliva amasungunulira mu uvuni ndipo golide mʼngʼanjo,

chomwechonso munthu amadziwika ndi zomwe akudzitamandira nazo.

22Ngakhale utakonola chitsiru mu mtondo

ndi musi ngati chimanga,

uchitsiru wakewo sudzachoka.

23Uzidziwe bwino nkhosa zako momwe zilili.

Kodi usamalire bwino ziweto zako?

24Paja chuma sichikhala mpaka muyaya,

ndipo ufumu sukhala mpaka mibado yonse.

25Pamene udzu watha, msipu nʼkumera;

ndipo atatuta udzu wa ku mapiri,

26ana ankhosa adzakupatsani chovala

ndipo pogulitsa mbuzi mudzapeza ndalama yogulira munda.

27Mudzakhala ndi mkaka wambuzi wambiri

kuti muzidya inuyo ndi banja lanu

ndi kudyetsa antchito anu aakazi.