Miyambo 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 2:1-22

Ubwino Wanzeru

1Mwana wanga, ngati ulandira mawu anga

ndi kusunga malamulo anga mu mtima mwako,

2ndiponso kutchera khutu lako ku nzeru

ndi kuyikapo mtima pa kumvetsa zinthu;

3ngati upempha kuti uzindikire zinthu

inde kupempha ndi mtima wonse kuti ukhale womvetsa zinthu,

4ngati ufunafuna nzeruyo ngati siliva

ndi kuyisakasaka ngati chuma chobisika,

5ndiye udzamvetsa bwino tanthauzo la kuopa Yehova;

ndipo udzapezanso tanthauzo la kumudziwa Yehova.

6Pakuti Yehova ndiye amapereka nzeru,

ndipo mʼkamwa mwake mumachokera chidziwitso ndi kumvetsa zinthu.

7Anthu olungama zinthu zimawayendera bwino chifukwa Yehova amakhala nawo.

Paja Yehova ndiye chishango cha amene amayenda mwangwiro,

8pakuti ndiye mlonda wa njira zolungama.

Iye amasamala mayendedwe a anthu ake okhulupirika.

9Choncho udzamvetsa tanthauzo la ungwiro, chilungamo,

kusakondera ndi njira iliyonse yabwino.

10Pakuti nzeru idzalowa mu mtima mwako,

kudziwa zinthu kudzakusangalatsa.

11Kuganizira bwino za mʼtsogolo kudzakusunga;

kumvetsa zinthu bwino kudzakuteteza.

12Nzeru idzakupulumutsa ku mayendedwe oyipa,

kwa anthu amabodza,

13amene amasiya njira zolungama

namayenda mʼnjira zamdima,

14amene amakondwera pochita zoyipa

namasangalala ndi kuyipa kwa ntchito zawo zonyansa.

15Amenewa ndi anthu a njira zawo zokhotakhota,

ndipo makhalidwe awo ndi achinyengo.

16Nzeruyo idzakupulumutsanso kwa mkazi wachigololo;

kwa mkazi wachilendo woyankhula moshashalika,

17amene wasiya mwamuna wa chitsikana wake

ndi kuyiwala pangano limene anachita pamaso pa Mulungu wake.

18Pakuti nyumba yake imatsetserekera ku imfa;

njira zake zimamufikitsa ku manda.

19Opita kwa iye palibe ndi mmodzi yemwe amabwerera

kapena kupezanso njira zamoyo.

20Choncho iwe uziyenda mʼnjira za anthu abwino,

uzitsata njira za anthu ochita chilungamo.

21Pakuti anthu olungama ndiwo ati adzakhale mʼdziko

ndipo anthu angwiro ndiwo ati adzakhazikike mʼmenemo;

22Koma anthu oyipa adzachotsedwa mʼdzikomo,

ndipo anthu onyenga adzachotsedwamo.