Miyambo 17 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 17:1-28

1Nʼkwabwino kudya mkute koma pali mtendere,

kuposa kuchita madyerero mʼnyumba mʼmene muli mikangano.

2Kapolo wanzeru adzalamulira mwana wochititsa manyazi,

ndipo kapoloyo adzagawana nawo cholowa ngati mmodzi mwa abale.

3Siliva amamuyesa mʼngʼanjo ndipo golide amamuyesa mʼngʼanjo,

koma Yehova amayesa mitima.

4Munthu woyipa amamvera malangizo oyipa;

munthu wabodza amatchera khutu mawu osakaza.

5Iye amene amalalatira mʼmphawi amanyoza mlengi wake;

amene amakondwerera tsoka la mnzake sadzakhala osalangidwa.

6Zidzukulu ndiye ulemu wa anthu okalamba,

ndipo makolo ndiye ulemerero wa ana.

7Kuyankhula bwino sikuyenerana ndi chitsiru,

nanji kuyankhula bodza kungayenerane kodi ndi mfumu?

8Chiphuphu chili ngati mankhwala amwayi kwa wochiperekayo;

kulikonse kumene amapita zinthu zimamuyendera.

9Iye amene amakhululukira zolakwa za wina, amafunitsitsa chikondi;

wobwerezabwereza nkhani amapha chibwenzi.

10Munthu wanzeru amamva kamodzi kokha,

munthu wopanda nzeru ndi samvamkunkhu.

11Munthu woyipa maganizo ake ali pa kuwukira basi;

ndipo bwana adzamutumizira wamthenga wankhanza.

12Nʼkwabwino kukumana ndi chimbalangondo cholandidwa ana ake

kusiyana ndi kukumana ndi chitsiru mu uchitsiru wake.

13Ngati munthu abwezera choyipa kusinthana ndi zabwino,

ndiye choyipa sichidzachoka mʼnyumba mwake.

14Chiyambi cha mikangano chili ngati kukhamulira madzi,

choncho uzichokapo mkangano usanayambe.

15Kumasula munthu wolakwa kapena kumanga munthu wosalakwa,

zonse ziwirizi Yehova zimamunyansa.

16Ndalama zogulira nzeru zili ndi phindu lanji mʼmanja mwa chitsiru

poti iyeyo mutu wake sumayenda bwino?

17Bwenzi lako limakukonda nthawi zonse,

ndipo mʼbale wako anabadwa kuti azikuthandiza pamavuto.

18Munthu wopanda nzeru amavomereza zopereka chikole

ndipo iyeyo amasanduka chikole cha mnansi wake.

19Wokonda zolakwa amakonda mkangano,

ndipo wokonda kuyankhula zonyada amadziyitanira chiwonongeko.

20Munthu wamtima woyipa zinthu sizimuyendera bwino;

ndipo woyankhula zachinyengo amagwa mʼmavuto.

21Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake,

abambo a chitsiru sakhala ndi chimwemwe.

22Mtima wosangalala uli ngati mankhwala abwino,

koma mtima wokhumudwa umafowoketsa mafupa.

23Munthu woyipa amalandira chiphuphu chamseri

kuti apotoze chiweruzo cholungama.

24Munthu wozindikira zinthu, maso ake amakhala pa nzeru,

koma chitsiru chimwazamwaza maso ake pa dziko lonse lapansi.

25Mwana wopusa amamvetsa chisoni abambo ake

ndipo amapweteketsa mtima amayi ake.

26Sibwino kulipitsa munthu wosalakwa,

kapena kulanga anthu osalakwa.

27Munthu wosunga pakamwa ndiye wodziwa zinthu,

ndipo wodekha mtima ndiye womvetsa bwino zinthu.

28Ngakhale chitsiru chimakhala ngati chanzeru chikakhala chete;

ndipo chikatseka pakamwa chimakhala ngati munthu wochenjera.