Miyambo 16 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 16:1-33

1Zolinga za mu mtima ndi za munthu,

koma kwa Yehova ndiye kumachokera yankho.

2Zochita zonse za munthu zimaoneka zabwino pamaso pake,

koma Yehova ndiye amasanthula zolinga zako.

3Pereka ntchito zako zonse mʼmanja mwa Yehova,

ndipo zolinga zako zidzachitikadi.

4Yehova amachita zonse ndi cholinga chake,

ngakhale anthu oyipa kuti aone tsiku latsoka.

5Munthu aliyense wodzikuza amamunyansa Yehova.

Koma dziwani izi: Iwo sadzakhala osalangidwa.

6Chifukwa cha chikondi chosasinthika ndi kukhulupirika, munthu amakhululukidwa machimo ake;

chifukwa cha kuopa Yehova munthu amapewa zoyipa.

7Pamene makhalidwe a munthu akondweretsa Yehova,

ngakhale adani ake amakhala naye mwa mtendere.

8Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono zozipeza mwachilungamo,

kusiyana ndi kukhala ndi zinthu zambiri zozipeza popanda chilungamo.

9Mtima wa munthu umalingalira zochita,

koma Yehova ndiye amakhazikitsa njira zake.

10Mawu a mfumu ali ngati mawu ochokera kwa Mulungu;

ndipo pakamwa pake sipalakwa poweruza mlandu.

11Miyeso ndi masikelo achilungamo zimachokera kwa Yehova;

miyala yonse yoyesera ya mʼthumba anayipanga ndi Yehova.

12Kuchita zoyipa kumanyansa mafumu,

pakuti chilungamo ndiye maziko a ufumu wake.

13Mawu owona amakondweretsa mfumu.

Iyo imakonda munthu woyankhula choonadi.

14Ukali wa mfumu ndi mthenga wa imfa,

koma munthu wanzeru amawupepesa ukaliwo.

15Kuwala kwa nkhope ya mfumu kumapatsa moyo;

ndipo kukoma mtima kwake kuli ngati mitambo ya mvula nthawi ya chilimwe.

16Nʼkwabwino kwambiri kupeza nzeru kupambana golide.

Kukhala womvetsa bwino zinthu nʼkwabwino kupambana ndi kukhala ndi siliva.

17Msewu wa munthu wowongoka mtima umapewa zoyipa;

wopenyetsetsa kumene akupita amasunga moyo wake.

18Kunyada kumafikitsa ku chiwonongeko,

ndipo munthu wodzikuza adzagwa.

19Nʼkwabwino kukhala ndi mtima wodzichepetsa pakati pa anthu oponderezedwa,

kusiyana ndi kugawana zolanda ndi anthu onyada.

20Munthu womvera malangizo zinthu zimamuyendera bwino,

ndipo wodala ndi amene amadalira Yehova.

21A mtima wanzeru amatchedwa ozindikira zinthu,

ndipo mawu ake okoma amawonjezera nzeru.

22Kumvetsa zinthu ndi kasupe wa moyo kwa iwo amene ali nako,

koma uchitsiru umabweretsa chilango kwa zitsiru.

23Mtima wanzeru umathandiza munthu kuyankhula mwa nzeru,

ndipo mawu ake amawonjezera nzeru.

24Mawu okometsera ali ngati chisa cha njuchi,

amakoma mu mtima ndipo amalimbitsa thupi.

25Pali njira ina yooneka ngati yowongoka kwa munthu

koma kumatsiriziro kwake ndi imfa.

26Njala ya munthu wantchito imamuthandiza kulimbikira;

njalayo imamukakamiza kuchitapo kanthu.

27Munthu wopanda pake amakonzekera kuchita zoyipa

ndipo mawu ake ali ngati moto wopsereza.

28Munthu woyipa mtima amayambitsa mikangano,

ndipo miseche imalekanitsa anthu okondana kwambiri.

29Munthu wandewu amakopa mnansi wake,

ndipo amamuyendetsa njira imene si yabwino.

30Amene amatsinzinira maso ake amalingalira zinthu zokhota;

amene amachita msunamo amakonzeka kuchita zoyipa.

31Imvi zili ngati chipewa chaufumu chaulemerero;

munthu amazipeza akakhala moyo wolungama.

32Munthu wosapsa mtima msanga amaposa munthu wankhondo,

munthu wowugwira mtima wake amaposa amene amalanda mzinda.

33Maere amaponyedwa pa mfunga,

koma ndiye Yehova amene amalongosola zonse.