Miyambo 15 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 15:1-33

1Kuyankha kofatsa kumathetsa mkwiyo,

koma mawu ozaza amautsa ukali.

2Munthu wanzeru amayankhula zinthu za nzeru,

koma pakamwa pa zitsiru pamatulutsa za uchitsiru.

3Maso a Yehova ali ponseponse,

amayangʼana pa oyipa ndi abwino omwe.

4Kuyankhula kodekha kuli ngati mtengo wopatsa moyo,

koma kuyankhula kopotoka kumapweteka mtima.

5Chitsiru chimanyoza mwambo wa abambo ake,

koma wochenjera amasamala chidzudzulo.

6Munthu wolungama amakhala ndi chuma chambiri,

zimene woyipa amapindula nazo zimamugwetsa mʼmavuto.

7Pakamwa pa anthu anzeru pamafalitsa nzeru;

koma mitima ya zitsiru sitero.

8Nsembe za anthu oyipa zimamunyansa Yehova,

koma amakondwera ndi pemphero la anthu owona mtima.

9Ntchito za anthu oyipa zimamunyansa Yehova

koma amakonda amene amafunafuna chilungamo.

10Amene amasiya njira yabwino adzalangidwa koopsa.

Odana ndi chidzudzulo adzafa.

11Manda ndi chiwonongeko ndi zosabisika pamaso pa Yehova,

nanji mitima ya anthu!

12Wonyoza sakonda kudzudzulidwa;

iye sapita kwa anthu anzeru.

13Mtima wokondwa umachititsa nkhope kukhala yachimwemwe,

koma mtima wosweka umawawitsa moyo.

14Mtima wa munthu wozindikira zinthu umafunafuna nzeru,

koma pakamwa pa zitsiru pamadya uchitsiru wawo.

15Munthu woponderezedwa masiku ake onse amakhala oyipa,

koma mtima wachimwemwe umakhala pa chisangalalo nthawi zonse.

16Kuli bwino kukhala ndi zinthu pangʼono nʼkumaopa Yehova,

kusiyana ndi kukhala ndi chuma chambiri uli pamavuto.

17Kuli bwino kudyera ndiwo zamasamba pamene pali chikondi,

kusiyana ndi kudyera nyama yangʼombe yonenepa pamene pali udani.

18Munthu wopsa mtima msanga amayambitsa mikangano,

koma munthu woleza mtima amathetsa ndewu.

19Njira ya munthu waulesi ndi yowirira ndi mtengo waminga,

koma njira ya munthu wolungama ili ngati msewu waukulu.

20Mwana wanzeru amakondweretsa abambo ake,

koma mwana wopusa amanyoza amayi ake.

21Uchitsiru umakondweretsa munthu wopanda nzeru,

koma munthu womvetsa zinthu amayenda mowongoka.

22Popanda uphungu zolinga zako munthu zimalephereka,

koma pakakhala aphungu ambiri zolinga zimatheka.

23Munthu amakondwera ndi kuyankha koyenera,

ndipo mawu onena pa nthawi yake ndi okoma.

24Munthu wanzeru amatsata njira yopita ku moyo

kuti apewe malo okhala anthu akufa.

25Yehova amapasula nyumba ya munthu wonyada

koma amasamalira malo a mkazi wamasiye.

26Maganizo a anthu oyipa amamunyansa Yehova,

koma mawu a anthu oyera mtima amamusangalatsa.

27Munthu wofuna phindu mwachinyengo amavutitsa banja lake,

koma wodana ndi ziphuphu adzakhala ndi moyo.

28Munthu wolungama amaganizira za mmene ayankhire,

koma pakamwa pa munthu woyipa pamatulutsa mawu oyipa.

29Yehova amakhala kutali ndi anthu oyipa,

koma amamva pemphero la anthu olungama.

30Kuwala kwa maso kumasangalatsa mtima

ndipo uthenga wabwino umalimbitsa munthu.

31Womvera mawu a chidzudzulo amene apatsa moyo

adzakhala pakati pa anthu anzeru.

32Amene amanyoza mwambo amadzinyoza yekha,

koma womvera mawu a chidzudzulo amapeza nzeru zomvetsa zinthu.

33Kuopa Yehova kumaphunzitsa munthu nzeru,

ndipo kudzichepetsa ndi ulemu chili patsogolo ndi kudzichepetsa.