Miyambo 11 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Miyambo 11:1-31

1Muyeso wachinyengo Yehova umamunyansa,

koma amakondwera ndi muyeso woyenera.

2Kunyada kukalowa, pamafikanso manyazi,

koma pamene pali kudzichepetsa pameneponso pali nzeru.

3Ungwiro wa anthu olungama umawatsogolera,

koma anthu osakhulupirika amawonongeka ndi chinyengo chawo.

4Chuma sichithandiza pa tsiku lawukali wa Mulungu,

koma chilungamo chimapulumutsa ku imfa.

5Chilungamo cha anthu angwiro chimawongolera moyo wawo,

koma ntchito zoyipa zimagwetsa mwini wake yemweyo.

6Chilungamo cha anthu oyera mtima chimawapulumutsa,

koma anthu onyenga adzagwidwa ndi zilakolako zawo zomwe.

7Pamene munthu woyipa wafa, chiyembekezo chake chimathanso.

Chiyembekezo cha munthu wosalungama chimawonongeka.

8Munthu wolungama amapulumutsidwa ku mavuto,

koma mʼmalo mwake amagwa mʼmavutomo ndi anthu oyipa.

9Munthu wosapembedza amawononga mnansi wake ndi pakamwa pake,

koma munthu wolungama amapulumuka chifukwa cha kudziwa zinthu.

10Anthu olungama zinthu zikamawayendera bwino, mzinda wonse umakondwera,

ndipo oyipa akamawonongeka anthu amafuwula mwachimwemwe.

11Mzinda umakwezeka chifukwa cha madalitso a anthu oyera mtima,

koma umawonongedwa chifukwa cha pakamwa pa anthu oyipa.

12Munthu wonyoza mnzake ndi wopanda nzeru,

koma munthu wanzeru zomvetsa zinthu amakhala chete.

13Amene amanka nachita ukazitape amawulula zinsinsi;

koma munthu wokhulupirika amasunga pakamwa pake.

14Pakasoweka uphungu mtundu wa anthu umagwa;

koma pakakhala aphungu ambiri pamakhalanso chipulumutso.

15Woperekera mlendo chikole adzapeza mavuto,

koma wodana ndi za chikole amakhala pa mtendere.

16Mkazi wodekha amalandira ulemu,

koma amuna ankhanza amangopata chuma.

17Munthu wachifundo amadzipindulira zabwino

koma munthu wankhanza amadzibweretsera mavuto.

18Munthu woyipa amalandira malipiro wopanda phindu,

koma wochita chilungamo amakolola mphotho yeniyeni.

19Munthu wochita za chilungamo amapeza moyo,

koma wothamangira zoyipa adzafa.

20Yehova amanyansidwa ndi anthu a mtima wokhotakhota

koma amakondwera ndi anthu a makhalidwe angwiro.

21Zoonadi, anthu oyipa adzalangidwa,

koma anthu olungama adzapulumuka.

22Monga imaonekera mphete yagolide ikakhala pa mphuno ya nkhumba,

ndi momwenso amaonekera mkazi wokongola wamʼkamwa.

23Zokhumba za anthu olungama zimathera pa zabwino zokhazokha,

koma chiyembekezo cha anthu oyipa chimathera mu ukali wa Mulungu.

24Munthu wina amapatsako anzake zinthu mwaufulu nʼkumangolemererabe;

wina amamana chomwe akanatha kupereka, koma kumanka nasawukabe.

25Munthu wopereka mowolowamanja adzalemera;

iye amene amathandiza ena iyenso adzathandizidwa.

26Anthu amatemberera womana anzake chakudya,

koma madalitso amakhala pamutu pa munthu amene amagulitsa chakudyacho.

27Iye amene amafunafuna zabwino mwakhama amapeza zabwinozo,

koma wofunafuna zoyipa zidzamupeza.

28Aliyense amene amadalira chuma chake adzafota,

koma wolungama adzaphukira ngati tsamba lobiriwira.

29Wovutitsa a mʼnyumba mwake adzalowa mʼmavuto,

ndipo chitsiru chidzakhala kapolo wa munthu wa nzeru.

30Chipatso cha ntchito zabwino ndi moyo,

ndipo kusatsata malamulo kumawonongetsa moyo.

31Ngati anthu olungama amalandira mphotho zawo pa dziko lapansi,

kuli bwanji anthu osapembedza ndi ochimwa!