Mika 7 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 7:1-20

Chipsinjo cha Israeli

1Tsoka ine!

Ndili ngati munthu wokunkha zipatso nthawi yachilimwe,

pa nthawi yokolola mphesa;

palibe phava lamphesa loti nʼkudya,

palibe nkhuyu zoyambirira zimene ndimazilakalaka kwambiri.

2Anthu opembedza atha mʼdziko;

palibe wolungama ndi mmodzi yemwe amene watsala.

Anthu onse akubisalirana kuti aphane;

aliyense akusaka mʼbale wake ndi khoka.

3Manja awo onse ndi aluso pochita zoyipa;

wolamulira amafuna mphatso,

woweruza amalandira ziphuphu,

anthu amphamvu amalamula kuti zichitike zimene akuzifuna,

onse amagwirizana zochita.

4Munthu wabwino kwambiri pakati pawo ali ngati mtengo waminga,

munthu wolungama kwambiri pakati pawo ndi woyipa kuposa mpanda waminga.

Tsiku limene alonda ako ananena lafika,

tsiku limene Mulungu akukuchezera.

Tsopano ndi nthawi ya chisokonezo chawo.

5Usadalire mnansi;

usakhulupirire bwenzi.

Usamale zoyankhula zako

ngakhale kwa mkazi amene wamukumbatira.

6Pakuti mwana wamwamuna akunyoza abambo ake,

mwana wamkazi akuwukira amayi ake,

mtengwa akukangana ndi apongozi ake,

adani a munthu ndi amene amakhala nawo mʼbanja mwake momwe.

7Koma ine ndikudikira Yehova mwachiyembekezo,

ndikudikira Mulungu Mpulumutsi wanga;

Mulungu wanga adzamvetsera.

Kuuka kwa Israeli

8Iwe mdani wanga, usandiseke!

Ngakhale ndagwa, ndidzauka.

Ngakhale ndikukhala mu mdima,

Yehova ndiye kuwunika kwanga.

9Ndidzapirira mkwiyo wa Yehova,

chifukwa ndinamuchimwira,

mpaka ataweruza mlandu wanga

ndi kukhazikitsa chilungamo changa.

Iye adzanditulutsa ndi kundilowetsa mʼkuwunika;

ndidzaona chilungamo chake.

10Ndipo mdani wanga adzaona zimenezi

nadzagwidwa ndi manyazi,

iye amene anandifunsa kuti,

“Ali kuti Yehova Mulungu wako?”

Ndidzaona kugonjetsedwa kwake ndi maso anga;

ngakhale tsopano adzaponderezedwa

ngati matope mʼmisewu.

11Idzafika nthawi yomanganso makoma anu,

nthawi yokulitsanso malire anu.

12Nthawi imeneyo anthu adzabwera kwa inu

kuchokera ku Asiriya ndi mizinda ya ku Igupto,

ngakhale kuchokera ku Igupto mpaka ku Yufurate

ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso

kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.

13Dziko lapansi lidzasanduka chipululu

chifukwa cha anthu okhala mʼdzikomo, potsatira zochita za anthuwo.

Pemphero ndi Matamando

14Wetani anthu anu ndi ndodo yanu yowateteza,

nkhosa zimene ndi cholowa chanu,

zimene zili zokha mʼnkhalango,

mʼdziko la chonde.

Muzilole kuti zidye mu Basani ndi mu Giliyadi

monga masiku akale.

15“Ndidzawaonetsa zodabwitsa zanga,

ngati masiku amene ndinawatulutsa mʼdziko la Igupto.”

16Mitundu ya anthu idzaona zimenezi ndipo idzachita manyazi,

ngakhale ali ndi mphamvu zotani.

Adzagwira pakamwa pawo

ndipo makutu awo adzagontha.

17Adzabwira fumbi ngati njoka,

ngati zolengedwa zomwe zimakwawa pansi.

Adzabwera akunjenjemera kuchokera mʼmaenje awo;

mwamantha adzatembenukira kwa Yehova Mulungu wathu

ndipo adzachita nanu mantha.

18Kodi alipo Mulungu wofanana nanu,

amene amakhululukira tchimo ndi kuyiwala zolakwa

za anthu otsala amene ndi cholowa chake?

Inu simusunga mkwiyo mpaka muyaya

koma kwanu nʼkuonetsa chikondi chosasinthika.

19Inu mudzatichitiranso chifundo;

mudzapondereza pansi machimo athu

ndi kuponyera zolakwa zathu zonse pansi pa nyanja.

20Mudzakhala wokhulupirika kwa Yakobo,

ndi kuonetsa chifundo chanu kwa Abrahamu,

monga munalonjeza molumbira kwa makolo athu

masiku amakedzana.