Mika 6 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 6:1-16

Mlandu wa Yehova ndi Israeli

1Tamverani zimene Yehova akunena:

“Nyamukani, fotokozani mlandu wanu pamaso pa mapiri;

zitunda zimve zimene inu muti muyankhule.

2Imvani mlandu wa Yehova, inu mapiri;

tamverani, maziko amuyaya a dziko lapansi.

Pakuti Yehova ali ndi mlandu ndi anthu ake;

Iye akutsutsa Aisraeli.

3“Anthu anga, kodi ndakuchitirani chiyani?

Kodi ndakutopetsani bwanji? Ndiyankheni.

4Ine ndinakutulutsani ku dziko la Igupto

ndi kukuwombolani ku nyumba ya ukapolo.

Ndinatuma Mose kuti akutsogolereni,

pamodzi ndi Aaroni ndi Miriamu.

5Anthu anga, kumbukirani

zimene Balaki mfumu ya ku Mowabu inafuna kukuchitirani

ndiponso zimene Balaamu mwana wa Beori anayankha.

Kumbukirani zomwe zinachitika pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala,

kuti mudziwe machitidwe olungama a Yehova.”

6Kodi ndidzatenga chiyani kupita nacho pamaso pa Yehova

ndi kukagwada pamaso pa Mulungu wakumwamba?

Kodi ndidzabwera pamaso pake ndi nsembe yopsereza,

ndi ana angʼombe a chaka chimodzi?

7Kodi Yehova adzakondwera ndi nkhosa zazimuna 1,000,

kapena ndi mitsinje yosalekeza ya mafuta?

Kodi ndipereke nsembe mwana wanga woyamba kubadwa chifukwa cha zolakwa zanga?

Chipatso cha thupi langa chifukwa cha tchimo la moyo wanga?

8Munthu iwe, Yehova wakuonetsa kale chimene chili chabwino.

Tsono kodi Yehova akuyembekezera chiyani kwa iwe?

Uzichita zolungama ndi kukonda chifundo

ndiponso kuyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Kulakwa kwa Israeli ndi Chilango chake

9Tamverani! Yehova akuyitana anthu okhala mu mzinda

ndi nzeru kuopa dzina lanu.

“Mverani mfumu ndi Iye amene anayikhazikitsa.

10Inu anthu oyipa, kodi Ine nʼkuyiwala

chuma chanu chimene munachipeza mwachinyengo,

ndiponso muyeso wanu woperewera umene ndi wotembereredwa?

11Kodi ndimutenge ngati wosalakwa munthu amene ali ndi sikelo yachinyengo,

ndiponso miyeso yabodza mʼthumba lake?

12Anthu ake olemera amachita zachiwawa;

anthu ake ndi abodza

ndipo pakamwa pawo pamayankhula zachinyengo.

13Choncho, ndayamba kukuwonongani,

kukusakazani chifukwa cha machimo anu.

14Mudzadya, koma simudzakhuta;

mudzakhalabe ndi njala.

Mudzasunga zinthu, koma sizidzasungika,

chifukwa zimene mudzasunga zidzawonongedwa ndi lupanga.

15Mudzadzala, koma simudzakolola.

Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzawagwiritsa ntchito.

Mudzaponda mphesa, koma simudzamwa vinyo wake.

16Inu mwatsatira malangizo a Omuri

ndiponso machitidwe onse a banja la Ahabu,

ndi khalidwe lawo lonse.

Choncho Ine ndidzakuperekani kuti muwonongedwe

ndiponso anthu anu kuti azunguzike mitu;

mudzanyozedwa ndi anthu a mitundu ina.”