Mika 5 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 5:1-15

Wolamulira Wochokera ku Betelehemu

1Iwe mzinda wa anthu ankhondo, sonkhanitsa anthu ako ankhondo,

pakuti anthu atizungulira kuti alimbane nafe.

Adzakantha ndi ndodo pa chibwano

cha wolamulira wa Israeli.

2“Koma iwe Betelehemu Efurata,

ngakhale uli wonyozeka pakati pa mafuko a Yuda,

mwa iwe mudzatuluka

munthu amene adzalamulira Israeli,

amene chiyambi chake nʼchakalekale,

nʼchamasiku amakedzana.”

3Nʼchifukwa chake Israeli adzasiyidwa

mpaka pa nthawi imene mayi amene ali woyembekezera adzachire.

Ndipo abale ake onse otsalira adzabwerera

kudzakhala pamodzi ndi Aisraeli.

4Iye adzalimbika, ndipo adzaweta nkhosa zake

mwa mphamvu ya Yehova,

mu ulemerero wa dzina la Yehova Mulungu wake.

Ndipo iwo adzakhala mu mtendere,

pakuti ukulu wake udzakhala ponseponse pa dziko lapansi.

5Ndipo Iye adzakhala mtendere wawo.

Chipulumutso ndi Chiwonongeko

Asiriya akadzalowa mʼdziko lathu

ndi kuyamba kuthira nkhondo malo athu otetezedwa,

tidzawadzutsira abusa asanu ndi awiri,

ngakhalenso atsogoleri asanu ndi atatu.

6Iwo adzagonjetsa dziko la Asiriya ndi lupanga,

dziko la Nimurodi adzalilamulira mwankhondo.

Adzatipulumutsa kwa Asiriya

akadzafika mʼmalire a mʼdziko lathu

kudzatithira nkhondo.

7Otsalira a Yakobo adzakhala

pakati pa mitundu yambiri ya anthu

ngati mame ochokera kwa Yehova,

ngati mvumbi pa udzu,

omwe sulamulidwa ndi munthu

kapena kudikira lamulo la anthu.

8Otsala a Yakobo adzakhala pakati pa mitundu ya anthu,

mʼgulu la anthu a mitundu yambiri,

ngati mkango pakati pa nyama za mʼnkhalango.

Ngati mwana wa mkango pakati pa gulu la nkhosa,

amene pozidutsa amazidya ndi kuzikhadzula,

ndipo palibe angathe kuzilanditsa.

9Mudzagonjetsa adani anu,

ndipo adani anu onse adzawonongeka.

10Yehova akuti,

“Tsiku limenelo ndidzawononga akavalo anu onse

ndi kuphwasula magaleta anu.

11Ndidzawononga mizinda ya mʼdziko mwanu

ndi kugwetsa malinga anu onse.

12Ndidzawononga ufiti wanu

ndipo sikudzakhalanso anthu owombeza mawula.

13Ndidzawononga mafano anu osema

pamodzi ndi miyala yanu yopatulika imene ili pakati panu;

simudzagwadiranso zinthu zopanga

ndi manja anu.

14Ndidzazula mitengo ya mafano a Asera imene ili pakati panu,

ndipo ndidzawononga mizinda yanu.

15Ndidzayilanga mwaukali ndi mokwiya

mitundu imene sinandimvere Ine.”