Mika 4 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 4:1-13

Phiri la Yehova

1Mʼmasiku otsiriza,

phiri la Nyumba ya Yehova adzalikhazikitsa

kukhala lalitali kuposa mapiri ena onse.

Lidzaonekera pamwamba pa mapiri ena onse,

ndipo anthu amitundu yonse adzathamangira kumeneko.

2Mayiko ambiri adzabwera ndikunena kuti,

“Tiyeni, tikwere ku phiri la Yehova,

ku nyumba ya Mulungu wa Yakobo.

Iye adzatiphunzitsa njira zake,

ndipo tidzayenda mʼnjira zakezo.”

Malangizo adzachokera ku Ziyoni,

mawu a Yehova adzachokera ku Yerusalemu.

3Iye adzaweruza pakati pa anthu amitundu yambiri

ndipo adzathetsa kusamvana pakati pa anthu amphamvu akutali ndi apafupi omwe.

Anthuwo adzasandutsa malupanga awo kukhala makasu

ndiponso mikondo yawo kukhala zomwetera.

Mtundu wina sudzatenganso lupanga kumenyana ndi mtundu wina,

kapena kuphunziranso za nkhondo.

4Munthu aliyense adzakhala pansi pa tsinde pa mtengo wake wa mpesa

ndi pa tsinde pa mtengo wake wamkuyu,

ndipo palibe amene adzawachititse mantha,

pakuti Yehova Wamphamvuzonse wayankhula.

5Mitundu yonse ya anthu

itha kutsatira milungu yawo;

ife tidzayenda mʼnjira za Yehova

Mulungu wathu mpaka muyaya.

Cholinga cha Yehova

6“Tsiku limenelo, Yehova akuti,

“ndidzasonkhanitsa olumala;

ndidzasonkhanitsa pamodzi anthu ochotsedwa

ndiponso amene ndinawalanga.

7Anthu olumalawo ndidzawasandutsa anthu anga otsala.

Anthu amene ndinawachotsa ndidzawasandutsa mtundu wamphamvu.

Yehova adzawalamulira mʼPhiri la Yehova

kuyambira tsiku limenelo mpaka muyaya.

8Kunena za iwe, nsanja ya ziweto zanga,

iwe linga la mwana wamkazi wa Ziyoni,

ulamuliro wako wakale udzabwezeretsedwa kwa iwe;

ufumu udzabwera pa mwana wamkazi wa Yerusalemu.”

9Chifukwa chiyani tsopano ukulira mofuwula,

kodi ulibe mfumu?

Kodi phungu wako wawonongedwa,

kotero kuti ululu wako uli ngati wa mayi amene akubereka?

10Gubuduka ndi ululu, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,

ngati mayi pa nthawi yake yobereka,

pakuti tsopano muyenera kuchoka mu mzinda

ndi kugona kunja kwa mzindawo.

Udzapita ku Babuloni;

kumeneko udzapulumutsidwa,

kumeneko Yehova adzakuwombola

mʼmanja mwa adani ako.

11Koma tsopano mitundu yambiri ya anthu

yasonkhana kulimbana nawe.

Iwo akuti, “Tiyeni timudetse,

maso athu aone chiwonongeko cha Ziyoni!”

12Koma iwo sakudziwa

maganizo a Yehova;

iwo sakuzindikira cholinga chake,

Iye amene amawatuta ngati mitolo ya tirigu ku malo opunthira tirigu.

13“Imirira, puntha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni,

pakuti ndidzakupatsa nyanga zachitsulo;

ndidzakupatsa ziboda zamkuwa

ndipo udzaphwanya mitundu yambiri ya anthu.”

Phindu lawo lolipeza molakwikalo udzalipereka kwa Yehova,

chuma chawo kwa Yehova wa dziko lonse lapansi.

King James Version

Micah 4:1-13

1But in the last days it shall come to pass, that the mountain of the house of the LORD shall be established in the top of the mountains, and it shall be exalted above the hills; and people shall flow unto it. 2And many nations shall come, and say, Come, and let us go up to the mountain of the LORD, and to the house of the God of Jacob; and he will teach us of his ways, and we will walk in his paths: for the law shall go forth of Zion, and the word of the LORD from Jerusalem.

3¶ And he shall judge among many people, and rebuke strong nations afar off; and they shall beat their swords into plowshares, and their spears into pruninghooks: nation shall not lift up a sword against nation, neither shall they learn war any more.4.3 pruninghooks: or, scythes 4But they shall sit every man under his vine and under his fig tree; and none shall make them afraid: for the mouth of the LORD of hosts hath spoken it. 5For all people will walk every one in the name of his god, and we will walk in the name of the LORD our God for ever and ever. 6In that day, saith the LORD, will I assemble her that halteth, and I will gather her that is driven out, and her that I have afflicted; 7And I will make her that halted a remnant, and her that was cast far off a strong nation: and the LORD shall reign over them in mount Zion from henceforth, even for ever.

8¶ And thou, O tower of the flock, the strong hold of the daughter of Zion, unto thee shall it come, even the first dominion; the kingdom shall come to the daughter of Jerusalem. 9Now why dost thou cry out aloud? is there no king in thee? is thy counsellor perished? for pangs have taken thee as a woman in travail. 10Be in pain, and labour to bring forth, O daughter of Zion, like a woman in travail: for now shalt thou go forth out of the city, and thou shalt dwell in the field, and thou shalt go even to Babylon; there shalt thou be delivered; there the LORD shall redeem thee from the hand of thine enemies.

11¶ Now also many nations are gathered against thee, that say, Let her be defiled, and let our eye look upon Zion. 12But they know not the thoughts of the LORD, neither understand they his counsel: for he shall gather them as the sheaves into the floor. 13Arise and thresh, O daughter of Zion: for I will make thine horn iron, and I will make thy hoofs brass: and thou shalt beat in pieces many people: and I will consecrate their gain unto the LORD, and their substance unto the Lord of the whole earth.