Mika 2 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 2:1-13

Zokonzekera za Munthu ndi Zokonzekera za Mulungu

1Tsoka kwa amene amakonzekera chiwembu,

kwa amene amakonzekera kuchita zoyipa usiku pa mabedi awo!

Kukacha mmawa amakachitadi

chifukwa ali ndi mphamvu zochitira zimenezo.

2Amasirira minda ndi kuyilanda,

amasirira nyumba ndi kuzilanda.

Amatenga nyumba ya munthu mwachinyengo,

munthu mnzawo kumulanda cholowa chake.

3Nʼchifukwa chake Yehova akuti,

“Ine ndikukonzekera kubweretsa tsoka pa anthu awa,

tsoka limene simudzatha kudzipulumutsa nokha.

Inu simudzayendanso monyada,

pakuti idzakhala nthawi ya masautso.

4Tsiku limenelo anthu adzakuchitani chipongwe;

adzakunyogodolani ndi nyimbo iyi yamaliro:

‘Tawonongeka kotheratu;

dziko la anthu anga lagawidwa.

Iye wandilanda!

Wapereka minda yathu kwa anthu otiwukira.’ ”

5Nʼchifukwa chake simudzakhala ndi munthu mu msonkhano wa Yehova

kuti agawe dziko pochita maere.

Aneneri Onyenga

6Aneneri awo amanena kuti, “Usanenere!

Usanenere ndi pangʼono pomwe zimenezi;

ife sitidzachititsidwa manyazi.”

7Inu nyumba ya Yakobo, monga zimenezi ndi zoyenera kuzinena:

“Kodi Mzimu wa Yehova wakwiya?

Kodi Iye amachita zinthu zotere?”

“Kodi mawu ake sabweretsa zabwino

kwa amene amayenda molungama?

8Posachedwapa anthu anga andiwukira

ngati mdani.

Mumawavula mkanjo wamtengowapatali

anthu amene amadutsa mosaopa kanthu,

monga anthu amene akubwera ku nkhondo.

9Mumatulutsa akazi a anthu anga

mʼnyumba zawo zabwino.

Mumalanda ana awo madalitso anga

kosatha.

10Nyamukani, chokani!

Pakuti ano si malo anu opumulirapo,

chifukwa ayipitsidwa,

awonongedwa, sangatheke kuwakonzanso.

11Ngati munthu wabodza ndi wachinyengo abwera nʼkunena kuti,

‘Ine ndidzanenera ndipo mudzakhala ndi vinyo ndi mowa wambiri,

woteroyo adzakhala mneneri amene anthu awa angamukonde!’

Alonjeza Chipulumutso

12“Inu banja la Yakobo, ndidzakusonkhanitsani nonse;

ndidzawasonkhanitsa pamodzi otsala a ku Israeli.

Ndidzawabweretsa pamodzi ngati nkhosa mʼkhola,

ngati ziweto pa msipu wake;

malowo adzadzaza ndi chinamtindi cha anthu.

13Amene adzawapulumutse adzayenda patsogolo pawo;

iwo adzathyola chipata ndipo adzatuluka.

Mfumu yawo idzawatsogolera,

Yehova adzakhala patsogolo pawo.”