Mika 1 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mika 1:1-16

1Yehova anayankhula ndi Mika wa ku Moreseti pa nthawi ya ulamuliro wa Yotamu, Ahazi ndi Hezekiya, mafumu a ku Yuda. Awa ndi masomphenya amene iye anaona onena za Samariya ndi Yerusalemu.

2Tamverani, inu anthu a mitundu yonse,

mvetsera iwe dziko lapansi ndi okhala mʼmenemo,

pakuti Ambuye Yehova achitira umboni wokutsutsani,

Ambuye akuyankhula ali mʼnyumba yake yopatulika.

Chiweruzo cha Samariya ndi Yerusalemu

3Taonani! Yehova akubwera kuchokera ku malo ake;

Iye akutsika ndipo akuponda pa malo okwera a dziko lapansi.

4Mapiri akusungunuka pansi pake,

ndipo zigwa zikugawikana

ngati phula pa moto,

ngati madzi ochokera mʼphiri.

5Zonsezi ndi chifukwa cha cholakwa cha Yakobo,

chifukwa cha machimo a nyumba ya Israeli.

Kodi cholakwa cha Yakobo nʼchiyani?

Kodi si Samariya?

Kodi malo achipembedzo a Yuda ndi ati?

Kodi si Yerusalemu?

6“Choncho Ine ndidzasandutsa Samariya kukhala bwinja,

malo odzalamo mphesa.

Miyala yake ndidzayitaya ku chigwa

ndipo ndidzafukula maziko ake.

7Mafano ake onse ndidzawaphwanyaphwanya;

mphatso zake zonse ndidzazitentha ndi moto;

ndidzawononga zifanizo zonse za milungu yake.

Popeza analandira mphatso zake kuchokera ku malipiro a akazi achiwerewere,

mphatsozonso zidzagwiritsidwa ntchito ndi ena ngati malipiro a akazi achiwerewere.”

Kulira ndi Kumva Chisoni

8Chifukwa cha zimenezi ine ndidzalira momvetsa chisoni;

ndidzayenda wopanda nsapato ndi wamaliseche.

Ndidzafuwula ngati nkhandwe

ndi kulira ngati kadzidzi.

9Pakuti chilonda cha Samariya nʼchosachizika;

chafika ku Yuda.

Chafika pa chipata chenicheni cha anthu anga,

mpaka mu Yerusalemu mwenimwenimo.

10Musanene zimenezi ku Gati;

musalire nʼkomwe.

Mugubuduzike mu fumbi

ku Beti-Leafura.

11Inu anthu okhala ku Safiro,

muzipita ku ukapolo muli amaliseche ndi amanyazi.

Iwo amene akukhala ku Zanaani

sadzatuluka.

Beti-Ezeli akulira mwachisoni;

chitetezo chake chakuchokerani.

12Anthu amene amakhala ku Maroti akubuwula ndi ululu,

akuyembekezera thandizo,

chifukwa Yehova wabweretsa tsoka,

lafika mpaka pa chipata cha Yerusalemu.

13Inu anthu okhala ku Lakisi

mangani akavalo ku magaleta.

Inu amene munayamba kuchimwitsa

mwana wamkazi wa Ziyoni,

pakuti zolakwa za Israeli

zinapezeka pakati panu.

14Chifukwa chake perekani mphatso zolawirana

ndi a ku Moreseti Gati.

Mzinda wa Akizibu udzaonetsa kunama

kwa mafumu a Israeli.

15Ndidzabweretsa mgonjetsi kudzalimbana ndi inu

okhala mu Maresa.

Ulemerero wa Israeli udzafika

ku Adulamu.

16Metani mipala mitu yanu kuonetsa kuti mukulirira

ana anu amene mumawakonda;

mudzichititse dazi ngati dembo,

pakuti anawo adzatengedwa pakati panu kupita ku ukapolo.

New Serbian Translation

Књига пророка Михеја 1:1-16

1Ово је Господња реч која је дошла Михеју Морашћанину, виђење за Самарију и Јерусалим у време Јотама, Ахаза и Језекије, царева Јуде.

2Чујте, о, народи сви!

Послушај, земљо, сви ви што је испуњавате!

Нека Господ Бог против вас сведок буде,

Господ из храма светости своје.

Суд над Самаријом и Јерусалимом

3Јер, гле, излази Господ из свог места,

сићи ће да гази висине земаљске.

4Под њим ће се топити планине,

распукнуће се долине

као восак пред огњем,

биће као када вода низ стрмину тече.

5Све је то због Јаковљевог преступа

и због греха куће израиљске.

А који је Јаковљев преступ?

Зар то није Самарија?

И које су узвишице Јудине?

Зар то није Јерусалим?

6„Самарију ћу да претворим у хрпу камења насред ледине,

у поље за засад винограда.

Камење ћу њено да изручим у долину,

оголићу њене темеље.

7Биће сатрвени сви њени кипови

и у ватри изгореће сви њени добици.

Уништићу све њене идоле

јер их је накупила од добити блудничке,

па ће опет бити блудничка добит.“

Плач и жаљење

8Жалићу ја због овог, вапићу,

ићи ћу бос и го.

Завијаћу нарицаљку као шакал

и кликтаћу као женка ноја.

9Јер нема лека за њену рану

која дође све до Јуде,

рашири се све до врата мог народа у Јерусалиму.

10Не јављајте Гату,

не јецајте, не плачите.

У Вет-Афри у прашини ваљајте се.

11Бежи, становнице сафирска,

гола и осрамоћена.

Неће изаћи становница сананска

јер због нарицаљке Вет-Езела

тамо нећете заклон наћи.

12Добро чека забринута становница маротска,

јер је сишло од Господа зло на врата Јерусалима.

13У бојна кола упрегни коње,

становнице Лахиса,

јер си почетак греха ћерко сионска.

У теби су се нашли преступи Израиља.

14Зато ћеш дати дарове Моресет-Гату,

а куће ахзивске изневериће цареве Израиља.

15Ипак ћу ти довести освајача,

становнице мариска,

а до Одолама ће доћи слава Израиља.

16Оћелави и косу ошишај

за децом својом милом.

Рашири ћелу своју као лешинар,

јер ће од тебе отићи у изгнанство.