Mateyu 5 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 5:1-48

Chiphunzitso cha pa Phiri

1Iye ataona anthu ambiri, anakwera pa phiri nakhala pansi. Ndipo ophunzira ake anabwera kwa Iye, 2ndipo anayamba kuwaphunzitsa kuti,

3“Odala ndi amene ali osauka mu mzimu,

chifukwa ufumu wakumwamba ndi wawo.

4Odala ndi amene ali achisoni,

chifukwa adzatonthozedwa.

5Odala ndi amene ali ofatsa,

chifukwa adzalandira dziko lapansi.

6Odala ndi amene akumva njala ndi ludzu la chilungamo,

chifukwa adzakhutitsidwa.

7Odala ndi amene ali ndi chifundo,

chifukwa adzawachitira chifundo.

8Odala ndi amene ali oyera mtima,

chifukwa adzaona Mulungu.

9Ndi odala amene amabweretsa mtendere,

chifukwa adzatchedwa ana a Mulungu.

10Odala ndi amene akuzunzidwa chifukwa cha chilungamo,

pakuti ufumu wakumwamba ndi wawo.”

11“Inu ndinu odala anthu akamakunyozani, kukuzunzani, kukunenerani zoyipa zilizonse ndi kukunamizirani chifukwa cha Ine. 12Sangalalani, kondwerani chifukwa mphotho yanu ndi yayikulu kumwamba, chifukwa moterenso ndi mmene anazunzira aneneri inu musanabadwe.

Mchere ndi Kuwunika

13“Inu ndinu mchere wa dziko lapansi. Koma ngati mcherewo usukuluka, adzawukometsanso ndi chiyani? Ulibenso ntchito koma kungowutaya kunja, anthu nawuponda.

14“Inu ndinu kuwunika kwa dziko lapansi. Mzinda wa pa phiri sungathe kubisika. 15Anthu sayatsa nyale ndikuyivundikira ndi mbiya, mʼmalo mwake amayika poonekera ndipo imawunikira onse mʼnyumbamo. 16Momwemonso kuwunika kwanu kuwale pamaso pa anthu kuti aone ntchito zanu zabwino ndi kulemekeza Atate anu akumwamba.

Kukwaniritsa Malamulo

17“Musaganize kuti ndinadza kudzathetsa malamulo kapena zonena za aneneri; sindinabwere kudzathetsa koma kukwaniritsa. 18Ine ndikukuwuzani zoonadi kuti, kufikira kutha kwa thambo ndi dziko lapansi, chilichonse chimene chinalembedwa mʼmalamulo, ngakhale kalemba kakangʼonongʼono, chidzakwaniritsidwa. 19Chifukwa chake aliyense amene aphwanya limodzi la malamulowa ngakhale lalingʼonongʼono ndi kuphunzitsa ena kuti achite chimodzimodzi, adzakhala wotsirizira mu ufumu wakumwamba, koma aliyense amene achita ndi kuphunzitsa malamulo awa adzakhala wamkulu mu ufumu wakumwamba. 20Chifukwa chake ndikuwuzani kuti ngati chilungamo chanu sichiposa cha Afarisi ndi aphunzitsi amalamulo, zoonadi, simudzalowa mu ufumu wakumwamba.

Zokhudza Kupha

21“Munamva kuti kunanenedwa kwa anthu kale kuti, ‘Usaphe ndipo kuti aliyense amene apha munthu adzaweruzidwa.’ 22Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense wokwiyira mʼbale wake adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene wonena mʼbale wake kuti, ‘Ndiwe wopanda phindu,’ adzapezeka wolakwa ku bwalo la milandu lalikulu. Ndipo aliyense amene anganene mnzake ‘wopandapake’ adzatengeredwa ku bwalo la milandu. Ndiponso aliyense amene angamunene mnzake kuti, ‘Chitsiru iwe,’ adzaponyedwa ku gehena.

23“Nʼchifukwa chake, pamene ukupereka chopereka chako pa guwa lansembe ndipo nthawi yomweyo ukumbukira kuti mʼbale wako ali nawe chifukwa, 24usiye choperekacho pa guwa lansembepo, choyamba pita kayanjane ndi mʼbale wako; ukatero bwera kudzapereka chopereka chakocho.

25“Fulumira kuyanjana ndi mnzako amene unamulakwira nthawi ya milandu isanafike chifukwa angakupereke kwa oweruza amene angakupereke kwa mlonda ndipo mlondayo angakutsekere mʼndende. 26Zoonadi, Ine ndikukuwuza kuti sudzatuluka mʼndende mpaka utalipira zonse.

Zokhudza Chigololo

27“Munamva kuti kunanenedwa kuti, ‘Usachite chigololo.’ 28Koma Ine ndikuwuzani kuti aliyense woyangʼana mkazi momusirira wachita naye kale chigololo mu mtima mwake. 29Ngati diso lako lakumanja likuchimwitsa, ulichotse ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena. 30Ndipo ngati dzanja lako lamanja likuchimwitsa, ulidule ndi kulitaya. Pakuti nʼkwabwino kwa iwe kutaya chiwalo chimodzi cha thupi lako, kusiyana ndi kuti thupi lonse liponyedwe mʼgehena.

Zokhudza Kusudzula Mkazi

31“Ananena kuti, ‘Aliyense wosudzula mkazi wake ayenera amupatse kalata ya chisudzulo.’ 32Koma Ine ndikukuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake pa chifukwa china chilichonse osati chifukwa cha chiwerewere, akumuchititsa mkaziyo chigololo ndipo aliyense wokwatira mkaziyo, akuchitanso chigololo.

Malonjezo

33“Munamvanso kuti kunanenedwa kwa anthu akale kuti, ‘Musaphwanye lonjezo; koma sungani malonjezo anu amene mwachita kwa Yehova.’ 34Koma ndikuwuzani kuti musalumbire ndi pangʼono pomwe kutchula kumwamba chifukwa kuli mpando waufumu wa Mulungu. 35Kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa ndi chopondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa ndi mzinda wa mfumu yayikulu. 36Ndipo musalumbire ndi mutu wanu chifukwa simungathe kuyeretsa ngakhale kudetsa tsitsi limodzi. 37Koma ‘Inde’ wanu akhaledi ‘Inde’ kapena ‘Ayi’ wanu akhaledi ‘Ayi,’ chilichonse choposera apa, chichokera kwa woyipayo.

Za Kubwezera Choyipa

38“Munamva kuti, ‘Diso kulipira diso ndi dzino kulipira dzino.’ 39Koma ndikuwuzani kuti musamukanize munthu woyipa, akakumenya patsaya mupatseni tsaya linalo. 40Ndipo ngati wina afuna kukuzenga mlandu kuti akulande malaya ako, umupatsenso mkanjo wako. 41Ngati wina akukakamiza kuti uyende naye mtunda umodzi, iwe uyende naye mitunda iwiri. 42Wina akakupempha kanthu umupatse, ndipo wofuna kubwereka usamukanize.

Kukonda Adani

43“Munamva kuti, ‘Konda mnansi wako ndi kudana ndi mdani wako.’ 44Koma Ine ndikuwuzani kuti, ‘Kondani adani anu ndi kuwapempherera okuzunzani 45kuti mukhale ana a Atate anu akumwamba, amene awalitsa dzuwa lake pa oyipa ndi pa abwino, nagwetsa mvula pa olungama ndi pa osalungama.’ 46Ngati mukonda amene akukondani inu, mudzapeza mphotho yanji? Kodi ngakhale amisonkho sachita chimodzimodzi? 47Ndipo ngati inu mupatsa moni abale anu okhaokha mukuchita chiyani choposa ena? Kodi ngakhale akunja sachita chimodzimodzi? 48Nʼchifukwa chake, inu khalani angwiro monga Atate anu akumwamba ali wangwiro.”

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马太福音 5:1-48

八福

1耶稣看见这些人群,就上了山,刚坐下,门徒便走到祂跟前, 2祂就开口教导他们,说:

3“心灵贫穷的人有福了,

因为天国是他们的。

4哀痛的人有福了,

因为他们必得安慰。

5谦和的人有福了,

因为他们必承受土地。

6爱慕公义如饥似渴的人有福了,

因为他们必得饱足。

7心存怜悯的人有福了,

因为他们必蒙上帝的怜悯。

8心灵纯洁的人有福了,

因为他们必看见上帝。

9使人和睦的人有福了,

因为他们必被称为上帝的儿女。

10为义受迫害的人有福了,

因为天国是他们的。

11“人们因为我的缘故侮辱、迫害、肆意毁谤你们,你们就有福了。 12要欢喜快乐,因为你们在天上有很大的奖赏。他们也曾这样迫害以前的先知。

盐和光

13“你们是世上的盐。如果盐失去咸味,怎能使它再变咸呢?它将毫无用处,只有被丢在外面任人践踏。 14你们是世上的光,如同建在山上的城一样无法隐藏。 15人点亮了灯,不会把它放在斗底下,而是放在灯台上,好照亮全家。 16同样,你们的光也应当照在人面前,好让他们看见你们的好行为,便赞美你们天上的父。

成全律法

17“不要以为我是来废除律法和先知书,我不是来废除,乃是来成全。 18我实在告诉你们,就是到天地都消失了,律法的一点一划都不会废除,全都要成就。 19所以,谁违背这些诫命中最小的一条,并教导别人违背,谁在天国将被称为最小的。但谁遵守这些诫命,并教导别人遵守,谁在天国将被称为大的。 20我告诉你们,除非你们的义胜过律法教师和法利赛人的义,否则断不能进天国。

论仇恨

21“你们听过吩咐古人的话,‘不可杀人,杀人的要受审判。’ 22但我告诉你们,凡无缘无故5:22 有古卷无“无缘无故”。向弟兄发怒的,要受审判;凡骂弟兄是白痴的,要受公会5:22 公会”是当时犹太人的最高司法机构,处理宗教、道德和伦理等事务。的审判;凡骂弟兄是笨蛋的,难逃地狱的火。

23“所以,你在祭坛前献祭的时候,要是想起有弟兄和你有过节, 24就该把祭物留在祭坛前,先去跟他和好,然后再来献祭。

25“趁着你和告你的人还在去法庭的路上,你要赶紧与对方和解。不然,他会把你交给审判官,审判官会把你交给差役关进监牢。 26我实在告诉你,要是有一分钱没有还清,你绝不能从那里出来。

论通奸

27“你们听过这样的话,‘不可通奸。’ 28但我告诉你们,凡看见妇女就动淫念的,他在心里已经犯了通奸罪。 29如果你的右眼使你犯罪,就把它剜掉!宁可失去身体的一部分,也比整个人下地狱好。 30如果你的右手使你犯罪,就把它砍掉!宁可失去身体的一部分,也比整个人下地狱好。

论休妻

31“还有话说,‘人若休妻,必须给她休书’。 32但我告诉你们,除非是妻子不贞,否则,休妻就是使妻子犯通奸罪,娶被休女子的人也犯了通奸罪。

论起誓

33“你们也听过吩咐古人的话,‘不可违背誓言,总要向主遵守所起的誓。’ 34但我告诉你们,不可起誓。不可指着天起誓,因为天是上帝的宝座。 35不可指着地起誓,因为地是上帝的脚凳。不可指着圣城耶路撒冷起誓,因为那是大君王的城。 36也不可指着自己的头起誓,因为你不能使一根头发变黑或变白。 37你们说话,是就说是,不是就说不是,多说的便是来自那恶者5:37 那恶者即魔鬼,又名撒旦。

论爱仇敌

38“你们听过这样的话,‘以眼还眼,以牙还牙。’ 39但我告诉你们,不要跟恶人作对。有人打你的右脸,连左脸也转过来让他打。 40有人想控告你,要夺取你的内衣,连外衣也给他。 41有人强迫你走一里路,你就跟他走二里路。 42有求你的,就给他;有向你借的,不可拒绝他。

43“你们听过这样的话,‘要爱邻居,恨仇敌。’ 44但我告诉你们,要爱仇敌,为迫害你们的人祷告。 45这样,你们才是天父的孩子。因为祂让阳光照好人也照坏人,降雨给义人也给恶人。 46如果你们只爱那些爱你们的人,有什么值得嘉奖的呢?就是税吏也会这样做。 47如果你们只问候自己的弟兄,有什么特别呢?就是外族人也会这样做。 48所以,你们要纯全,正如你们的天父是纯全的。