Mateyu 4 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 4:1-25

Yesu Ayesedwa Mʼchipululu

1Pambuyo pake Yesu anatsogozedwa ndi Mzimu Woyera kupita ku chipululu kukayesedwa ndi mdierekezi. 2Ndipo atasala kudya masiku makumi anayi usana ndi usiku, anamva njala. 3Woyesayo anadza kwa Iye nati, “Ngati ndinu mwana wa Mulungu, sandutsani miyala iyi kuti ikhale buledi.”

4Yesu anayankha kuti, “Zalembedwa, ‘Munthu sadzakhala ndi moyo ndi chakudya chokha, koma ndi mawu aliwonse ochokera mʼkamwa mwa Mulungu.’ ”

5Pamenepo mdierekezi anapita naye ku mzinda woyera namuyimiritsa pamwamba penipeni pa Nyumba ya Mulungu. 6Ndipo anati, “Ngati ndinu Mwana wa Mulungu, dziponyeni nokha pansi. Pakuti kwalembedwa:

“ ‘Adzalamulira angelo ake za iwe,

ndipo adzakunyamula ndi manja awo

kuti phazi lako lisagunde pa mwala.’ ”

7Yesu anamuyankha kuti, “Kwalembedwanso: ‘Musamuyese Yehova Mulungu wanu.’ ”

8Kenaka mdierekezi anamutengera Yesu ku phiri lalitali kwambiri namuonetsa maufumu onse a dziko lapansi ndi ulemerero wawo. 9Ndipo anati kwa Iye, “Zonsezi ndidzakupatsani ngati mutandiweramira ndi kundipembedza ine.”

10Yesu anati kwa iye, “Choka Satana! Zalembedwa, ‘Pembedza Yehova Mulungu wako ndi kumutumikira Iye yekha.’ ”

11Pamenepo mdierekezi anamusiya ndipo angelo anamutumikira Iye.

Yesu Ayamba Kulalikira

12Yesu atamva kuti Yohane anamutsekera mʼndende, anabwerera ku Galileya. 13Ndipo atachoka ku Nazareti anapita ku Kaperenawo ndi kukhala mʼmbali mwa nyanja, mʼdera la Zebuloni ndi Nafutali; 14pokwaniritsa zimene zinanenedwa kudzera mwa mneneri Yesaya kuti,

15“Dziko la Zebuloni ndi dziko la Nafutali,

njira ya ku nyanja, kutsidya lija la Yorodani,

Galileya wa anthu a mitundu ina,

16anthu okhala mu mdima

awona kuwala kwakukulu;

ndi kwa iwo okhala mʼdziko la mthunzi wa imfa

kuwunika kwawafikira.”

17Kuyambira nthawi imeneyo, Yesu anayamba kulalikira nati, “Tembenukani mtima ufumu wakumwamba wayandikira.”

Yesu Ayitana Ophunzira ake Oyamba

18Pamene Yesu ankayenda mʼmbali mwa nyanja ya Galileya, anaona abale awiri, Simoni wotchedwa Petro ndi mʼbale wake Andreya akuponya khoka mʼnyanja popeza anali asodzi. 19Yesu anati, “Bwerani, tsateni Ine ndipo ndidzakusandutsani asodzi a anthu.” 20Nthawi yomweyo anasiya makoka awo namutsata Iye.

21Atapita patsogolo, anaona abale ena awiri, Yakobo ndi mʼbale wake Yohane ana a Zebedayo. Iwowa anali mʼbwato ndi abambo awo, Zebedayo, akukonza makoka awo ndipo Yesu anawayitana. 22Nthawi yomweyo anasiya bwato ndi abambo awo namutsata Iye.

Yesu Achiritsa Odwala

23Yesu anayendayenda mu Galileya kuphunzitsa mʼmasunagoge awo, nalalikira Uthenga Wabwino wa ufumu ndi kuchiritsa matenda onse pakati pa anthu. 24Mbiri yake yonse inawanda ku Siriya konse ndipo anthu anabweretsa kwa Iye onse amene anali odwala nthenda zosiyanasiyana, womva maululu aakulu, ogwidwa ndi ziwanda, odwala matenda akugwa ndi olumala ndipo Iye anawachiritsa. 25Magulu ambiri a anthu anachokera ku Galileya, Dekapoli, Yerusalemu, Yudeya ndi ku madera a kutsidya la mtsinje wa Yorodani namutsata Iye.