Mateyu 22 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 22:1-46

Fanizo la Phwando la Ukwati

1Yesu anayankhula nawonso mʼmafanizo, nati, 2“Ufumu wakumwamba uli ngati mfumu imene inakonzera phwando mwana wake wamwamuna. 3Anatumiza antchito ake kwa amene anayitanidwa kuphwando koma anakana kubwera.

4“Kenaka anatumiza antchito ena nati, ‘Awuzeni oyitanidwa kuti phwando lakonzedwa: ndapha ngʼombe yayimuna ndi nyama zina zonenepa ndipo zonse zakonzedwa. Bwerani ku phwando laukwati.’

5“Koma iwo sanalabadire ndipo anachoka; wina anapita ku munda wake ndi wina ku malonda ake. 6Ndipo otsalawo anagwira antchito ake, nawazunza ndi kuwapha. 7Mfumu inakwiya. Inatumiza asilikali ake ndipo anawononga opha anzawowo ndi kutentha mzinda wawo.

8“Pamenepo anati kwa antchito ake, ‘Phwando laukwati lakonzedwa, koma amene ndinawayitana sanali oyenera. 9Pitani ku mphambano za misewu ndipo kayitaneni aliyense amene mukamupeze kuti abwere ku phwando.’ 10Pamenepo antchitowo anapita ku misewu nakasonkhanitsa anthu onse amene anakawapeza, abwino ndi oyipa omwe, ndipo nyumba ya madyerero inadzaza ndi oyitanidwa.

11“Koma pamene mfumu inabwera kudzaona oyitanidwawo, inaona munthu amene sanavale zovala zaukwati. 12Inamufunsa kuti, ‘Bwenzi walowa bwanji muno wopanda zovala zaukwati?’ Munthuyo anakhala chete.

13“Pamenepo mfumuyo inawuza otumikira kuti, ‘Mʼmangeni manja ndi miyendo, ndipo muponyeni kunja, ku mdima kumene kudzakhale kulira ndi kukuta mano.’

14“Popeza oyitanidwa ndi ambiri koma osankhidwa ndi ochepa.”

Za Kupereka Msonkho

15Kenaka Afarisi anatuluka nakakonza njira zomupezera zifukwa Yesu mʼmawu ake. 16Anatumiza ophunzira awo kwa Iye pamodzi ndi Aherodia. Anati, “Aphunzitsi, tidziwa kuti ndinu wangwiro ndi kuti mumaphunzitsa mawu a Mulungu monga mwa choonadi. Simutekeseka ndi anthu, popeza simusamala kuti kodi ndi ndani? 17Tiwuzeni tsono maganizo anu ndi otani, kodi nʼkololedwa kupereka msonkho kwa Kaisara kapena ayi?”

18Koma Yesu podziwa maganizo awo oyipa anati, “Inu achiphamaso, bwanji mufuna kundipezera chifukwa? 19Onetseni ndalama imene mumapereka msonkho.” Iwo anabweretsa dinari, 20ndipo anawafunsa kuti, “Kodi chithunzi ichi ndi malemba awa ndi za ndani?”

21Iwo anayankha kuti, “Ndi za Kaisara.”

Pamenepo anawawuza kuti, “Perekani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.”

22Atamva izi, anadabwa, ndipo anamusiya Iye, nachoka.

Ukwati ndi za Kuuka kwa Akufa

23Tsiku lomwelo Asaduki amene amati kulibe za kuukanso, anabwera kwa Iye ndi funso. 24Iwo anati, “Aphunzitsi, Mose anatiwuza kuti munthu akamwalira wosasiya ana, mʼbale wake akuyenera kukwatira mkazi wamasiyeyo kuti amuberekere ana mʼbale wakeyo. 25Tsopano panali abale asanu ndi awiri pakati pathu. Woyambayo anakwatira ndipo anamwalira, ndipo popeza analibe ana, mʼbale wake analowa chokolo. 26Izi zinachitikiranso mʼbale wa chiwiri ndi wachitatu mpaka wachisanu ndi chiwiri. 27Pa mapeto pake mkaziyo anamwaliranso. 28Tsopano, kodi akadzaukitsidwa adzakhala mkazi wa ndani mwa asanu ndi awiriwa popeza aliyense anamukwatirapo?”

29Yesu anayankha kuti, “Inu mukulakwitsa chifukwa simukudziwa malemba kapena mphamvu ya Mulungu. 30Anthu akadzaukitsidwa, sadzakwatira kapena kukwatiwa; adzakhala ngati angelo kumwamba. 31Koma za kuukitsidwa kwa akufa, kodi simunawerenge zimene Mulungu ananena kwa inu kuti, 32‘Ine ndine Mulungu wa Abrahamu, Mulungu wa Isake ndi Mulungu wa Yakobo?’ Iyeyo si Mulungu wa akufa koma wa amoyo.”

33Magulu a anthu atamva zimenezi, anazizwa ndi chiphunzitso chake.

Lamulo Lalikulu Koposa

34Pakumva kuti Yesu anawakhalitsa chete Asaduki, Afarisi anasonkhana pamodzi. 35Mmodzi wa iwo, katswiri wa malamulo anamuyesa Iye ndi funso ndipo anati, 36“Aphunzitsi, kodi lamulo lalikulu koposa mu malamulo ndi liti?” 37Yesu anayankha kuti, “Uzikonda Yehova Mulungu wako ndi mtima wako wonse ndi moyo wako wonse ndi nzeru zako zonse. 38Ili ndi lamulo loyamba ndi loposa onse. 39Ndipo lachiwiri ndi lofanana nalo: ‘Konda mnansi wako monga iwe mwini.’ 40Malamulo onse ndi aneneri zakhazikika pa malamulo awiriwa.”

Kodi Khristu ndi Mwana wa Ndani?

41Afarisi atasonkhana pamodzi, Yesu anawafunsa kuti, 42“Kodi mukuganiza bwanji za Khristu? Ndi Mwana wa ndani?”

Iwo anayankha kuti, “Mwana wa Davide.”

43Iye anawawuza kuti, “Nanga zikutheka bwanji kuti Davide poyankhula mwa Mzimu Woyera amatchula Iye ‘Ambuye?’ Pakuti akuti,

44“Ambuye anati kwa Ambuye wanga:

‘Khala pa dzanja langa lamanja

mpaka ndiyike adani ako

pansi pa mapazi ako.’

45Ngati tsono Davide amamutchula ‘Ambuye,’ zingatheke bwanji kukhala mwana wake?” 46Panalibe wina anatha kuyankha, ndipo kuchokera pamenepo, panalibe wina anayerekeza kumufunsa funso.

King James Version

Matthew 22:1-46

1And Jesus answered and spake unto them again by parables, and said, 2The kingdom of heaven is like unto a certain king, which made a marriage for his son, 3And sent forth his servants to call them that were bidden to the wedding: and they would not come. 4Again, he sent forth other servants, saying, Tell them which are bidden, Behold, I have prepared my dinner: my oxen and my fatlings are killed, and all things are ready: come unto the marriage. 5But they made light of it, and went their ways, one to his farm, another to his merchandise: 6And the remnant took his servants, and entreated them spitefully, and slew them. 7But when the king heard thereof, he was wroth: and he sent forth his armies, and destroyed those murderers, and burned up their city. 8Then saith he to his servants, The wedding is ready, but they which were bidden were not worthy. 9Go ye therefore into the highways, and as many as ye shall find, bid to the marriage. 10So those servants went out into the highways, and gathered together all as many as they found, both bad and good: and the wedding was furnished with guests.

11¶ And when the king came in to see the guests, he saw there a man which had not on a wedding garment: 12And he saith unto him, Friend, how camest thou in hither not having a wedding garment? And he was speechless. 13Then said the king to the servants, Bind him hand and foot, and take him away, and cast him into outer darkness; there shall be weeping and gnashing of teeth. 14For many are called, but few are chosen.

15¶ Then went the Pharisees, and took counsel how they might entangle him in his talk. 16And they sent out unto him their disciples with the Herodians, saying, Master, we know that thou art true, and teachest the way of God in truth, neither carest thou for any man: for thou regardest not the person of men. 17Tell us therefore, What thinkest thou? Is it lawful to give tribute unto Caesar, or not? 18But Jesus perceived their wickedness, and said, Why tempt ye me, ye hypocrites? 19Shew me the tribute money. And they brought unto him a penny. 20And he saith unto them, Whose is this image and superscription? 21They say unto him, Cæsar’s. Then saith he unto them, Render therefore unto Cæsar the things which are Cæsar’s; and unto God the things that are God’s. 22When they had heard these words, they marvelled, and left him, and went their way.

23¶ The same day came to him the Sadducees, which say that there is no resurrection, and asked him, 24Saying, Master, Moses said, If a man die, having no children, his brother shall marry his wife, and raise up seed unto his brother. 25Now there were with us seven brethren: and the first, when he had married a wife, deceased, and, having no issue, left his wife unto his brother: 26Likewise the second also, and the third, unto the seventh. 27And last of all the woman died also. 28Therefore in the resurrection whose wife shall she be of the seven? for they all had her. 29Jesus answered and said unto them, Ye do err, not knowing the scriptures, nor the power of God. 30For in the resurrection they neither marry, nor are given in marriage, but are as the angels of God in heaven. 31But as touching the resurrection of the dead, have ye not read that which was spoken unto you by God, saying, 32I am the God of Abraham, and the God of Isaac, and the God of Jacob? God is not the God of the dead, but of the living. 33And when the multitude heard this, they were astonished at his doctrine.

34¶ But when the Pharisees had heard that he had put the Sadducees to silence, they were gathered together. 35Then one of them, which was a lawyer, asked him a question, tempting him, and saying, 36Master, which is the great commandment in the law? 37Jesus said unto him, Thou shalt love the Lord thy God with all thy heart, and with all thy soul, and with all thy mind. 38This is the first and great commandment. 39And the second is like unto it, Thou shalt love thy neighbour as thyself. 40On these two commandments hang all the law and the prophets.

41¶ While the Pharisees were gathered together, Jesus asked them, 42Saying, What think ye of Christ? whose son is he? They say unto him, The Son of David. 43He saith unto them, How then doth David in spirit call him Lord, saying, 44The LORD said unto my Lord, Sit thou on my right hand, till I make thine enemies thy footstool? 45If David then call him Lord, how is he his son? 46And no man was able to answer him a word, neither durst any man from that day forth ask him any more questions.