Mateyu 21 – CCL & HHH

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 21:1-46

Yesu Alowa mu Yerusalemu

1Akuyandikira ku Yerusalemu anafika ku Betifage pa phiri la Olivi, Yesu anatumiza ophunzira awiri, 2nawawuza kuti, “Pitani ku mudzi uli patsogolo panu, ndipo mukakangolowa mʼmenemo mukapeza bulu womangidwa ali ndi mwana pa mbali pake. Mukawamasule ndipo mubwere nawo kwa Ine. 3Wina akakayankhula, mukamuwuze kuti Ambuye akuwafuna, ndipo adzawatumiza nthawi yomweyo.”

4Izi zinachitika kukwaniritsa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri:

5“Uza mwana wamkazi wa Ziyoni,

taona, mfumu yako ikubwera kwa iwe,

yofatsa ndi yokwera pa bulu,

pa kamwana ka bulu, mwana wa nyama yonyamula katundu.”

6Ophunzirawo anapita nachita monga Yesu anawalamulira. 7Anabweretsa bulu ndi mwana wake, nayala zovala zawo pa abuluwo, ndipo Yesu anakwerapo. 8Gulu lalikulu la anthu linayala zovala zawo mu msewu pamene ena anadula nthambi zamitengo ndi kuziyala mu msewumo. 9Magulu amene anali patsogolo pake ndi amene amamutsatira anafuwula kuti,

“Hosana Mwana wa Davide!”

“Wodala Iye amene abwera mʼdzina la Ambuye!”

“Hosana mmwambamwamba!”

10Yesu atalowa mu Yerusalemu, mzinda wonse unatekeseka ndipo anthu anafunsa kuti, “Ndani ameneyu?”

11Magulu a anthu anayankha kuti, “Uyu ndi Yesu, mneneri wochokera ku Nazareti.”

Yesu mʼNyumba ya Mulungu

12Yesu analowa mʼdera lina la Nyumba ya Mulungu ndipo anatulutsa kunja anthu onse amene ankachita malonda. Anagubuduza matebulo a osinthira ndalama ndi mipando ya ogulitsa nkhunda. 13Iye anawawuza kuti, “Zinalembedwa kuti Nyumba yanga idzatchedwa Nyumba ya mapemphero koma inu mwayisandutsa phanga la anthu achifwamba.”

14Anthu osaona ndi olumala anabwera kwa Iye mʼNyumba ya Mulungu ndipo anawachiritsa. 15Koma akulu a ansembe ndi aphunzitsi amalamulo ataona zodabwitsa zimene anachita, komanso ana akufuwula mʼNyumbayo kuti, “Hosana kwa Mwana wa Davide,” anapsa mtima.

16Anamufunsa kuti, “Kodi mukumva zimene anawa akunena?”

Yesu anayankha nati, “Inde. Kodi simunawerenge kuti,

“Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda

mwatuluka mayamiko?”

17Ndipo anawasiya natuluka mu mzindawo ndi kupita ku Betaniya, kumene anakagona.

Yesu Atemberera Mtengo wa Mkuyu

18Mmamawa, pamene amabwera ku mzinda, anamva njala. 19Ataona mtengo wamkuyu mʼmbali mwa msewu, anapitapo koma sanapeze kanthu koma masamba okhaokha. Pamenepo anati kwa mtengowo, “Usadzabalenso chipatso!” Nthawi yomweyo mtengowo unafota.

20Ophunzira ataona zimenezi, anadabwa nafunsa kuti, “Kodi mtengo wamkuyuwu wauma msanga bwanji?”

21Yesu anayankha kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro ndipo simukayika, simudzangochita zokha zachitika kwa mkuyuzi, koma mudzatha kuwuza phiri ili kuti, ‘Pita, kadziponye wekha mʼnyanja,’ ndipo zidzachitikadi. 22Ngati mukhulupirira, mudzalandira chilichonse chimene muchipempha mʼpemphero.”

Amufunsa Yesu za Ulamuliro Wake

23Yesu analowa mʼNyumba ya Mulungu, ndipo pamene ankaphunzitsa, akulu a ansembe ndi akuluakulu anabwera kwa Iye namufunsa kuti, “Muchita izi ndi ulamuliro wanji ndipo anakupatsani ndani ulamuliro umenewu?”

24Yesu anayankha kuti, “Inenso ndikufunsani funso limodzi, mukandiyankha, Inenso ndikukuwuzani ndi ulamuliro wa yani umene ndikuchitira izi. 25Ubatizo wa Yohane unachokera kuti? Kumwamba kapena kwa anthu?”

Anakambirana pakati pawo ndipo anati, “Tikati, ‘Kuchokera kumwamba,’ Iye adzafunsa kuti, ‘Bwanji simunakhulupirire?’ 26Koma tikati, ‘Kuchokera kwa anthu,’ ife tikuopa anthuwa, pakuti onse amakhulupirira kuti Yohane anali mneneri.”

27Choncho anamuwuza Yesu kuti, “Sitikudziwa.”

Pamenepo Iye anati, “Inenso sindikuwuzani kuti ndi ulamuliro wa yani umene ndichitira izi.”

Fanizo la Ana Amuna Awiri

28“Kodi muganiza bwanji? Panali munthu wina anali ndi ana aamuna awiri. Anapita kwa woyamba nati, ‘Mwanawe pita kagwire ntchito lero mʼmunda wamphesa.’

29“Iye anayankha kuti, ‘Sindipita,’ koma pambuyo pake anasintha maganizo napita.

30“Kenaka abambowo anapita kwa mwana winayo nanena chimodzimodzi. Iye anayankha kuti, ‘Ndipita abambo,’ koma sanapite.

31“Ndani wa awiriwa anachita chimene abambo ake amafuna?”

Anamuyankha nati, “Woyambayo.”

Yesu anawawuza kuti, “Ndikuwuzani zoonadi, kuti amisonkho ndi adama akulowa mu ufumu wa Mulungu inu musanalowemo.” 32Pakuti Yohane anabwera kwa inu kuti akuonetseni njira yachilungamo, koma inu simunakhulupirire iye, koma amisonkho ndi adama anamukhulupirira. Koma ngakhale munaona izi, simunatembenuke mtima ndi kumukhulupirira iye.

Fanizo la Alimi

33“Tamverani fanizo lina: Panali mwini munda amene anadzala mphesa. Anamanga mpanda kuzungulira mundawo, nakumba moponderamo mphesa ndipo anamanga nsanja. Kenaka anabwereketsa munda wamphesawo kwa alimi ena napita pa ulendo. 34Pamene nthawi yokolola inakwana, anatumiza antchito ake kwa matenanti aja kuti akatenge zipatso zake.

35“Alimi aja anagwira antchito ake; namenya mmodzi, napha wina, ndi kumuponya miyala wachitatuyo. 36Kenaka anatumiza antchito ena oposa oyambawo ndipo matenantiwo anawachitira chimodzimodzi. 37Pomalizira anatumiza mwana wake. Anati adzamuchitira ulemu mwana wanga.

38“Koma alimiwo ataona mwanayo anati kwa wina ndi mnzake, ‘Uyu ndiye olowa mʼmalo mwa abambo ake. Tiyeni timuphe ndipo titenge cholowa chake.’ 39Pamenepo anamutenga namuponyera kunja kwa munda wamphesa namupha.

40“Tsono akabwera mwini munda wamphesa adzachita nawo chiyani matenantiwo?”

41Iwo anayankha kuti, “Adzawapha moyipa alimi oyipawo ndipo adzabwereketsa mundawo kwa alimi ena amene adzamupatsa gawo lake la mbewu pa nthawi yokolola.”

42Yesu anawawuza kuti, “Kodi simunawerenge mʼmalemba kuti:

“ ‘Mwala umene omanga nyumba anawukana,

womwewo wasanduka mwala wofunika kwambiri wa pa ngodya.

Ambuye wachita izi,

ndipo ndi zodabwitsa mʼmaso mwathu.’

43“Nʼchifukwa chake ndi kukuwuzani kuti ufumu wa Mulungu udzalandidwa kwa inu ndipo udzapatsidwa kwa anthu amene adzabereka chipatso chake. 44Amene agwa pa mwalawu adzadukaduka, ndipo amene udzamugwere udzamuthudzula.”

45Akulu a ansembe ndi Afarisi atamva mafanizo a Yesu, anadziwa kuti ankanena iwo. 46Pamenepo anafuna njira yoti amugwirire, koma anaopa gulu la anthu chifukwa anthu onse ankakhulupirira kuti Iye anali mneneri.

Habrit Hakhadasha/Haderekh

הבשורה על-פי מתי 21:1-46

1כשהתקרבו ישוע ותלמידיו לירושלים ועברו ליד בית־פגי, שעל הר הזיתים, שלח ישוע שניים מתלמידיו אל הכפר ואמר: 2”כשתיכנסו אל הכפר תראו אתון קשורה ולידה עיר. התירו אותם והביאו אלי. 3אם מישהו ישאל אתכם מה אתם עושים, אמרו פשוט: ’האדון זקוק להם‘. והוא יניח לכם מיד.“

4דבר זה בא לקיים את הנבואה:21‏.4 כא 4 זכריה ט 9

5”אמרו לבת ציון, הנה מלכך יבוא לך,

עני ורוכב על חמור ועל עַיִר בן־אתנות.“

6שני התלמידים הלכו אל הכפר ועשו כדברי ישוע. 7הם הביאו אליו את העיר ואת האתון, ריפדו את גבם במעיליהם והושיבו עליהם את ישוע. 8רבים מההמון השליכו את מעיליהם על הדרך לפני ישוע, ואחרים כרתו ענפים מהעצים ושטחו אותם לפניו. 9ההמונים החלו להידחק מלפניו ומאחוריו וקראו:

”הושע־נא לבן־דוד!“

”ברוך הבא בשם ה׳!“ 21‏.9 כא 9 תהלים קיח 26‏-25

”הושע־נא במרומים!“

10כשנכנס ישוע לתוך ירושלים, העיר כולה התרגשה מאוד. ”מי האיש הזה?“ שאלו האנשים.

11וההמון השיב: ”זהו ישוע – הנביא מנצרת שבגליל!“

12ישוע הלך לבית־המקדש, גירש את כל הסוחרים והקונים, הפך את השולחנות של מחליפי הכספים ואת הדוכנים של סוחרי היונים.

13”בכתבי־הקודש כתוב:21‏.13 כא 13 ישעיה נו 7 ’ביתי בית־תפלה ייקרא‘, “ קרא ישוע, ”ואילו אתם הפכתם אותו למאורת גנבים!“ 14העיוורים ובעלי המום שהיו בבית־המקדש ניגשו אליו, והוא ריפא אותם שם. 15אולם כשראו ראשי הכוהנים והסופרים את הניסים והנפלאות שחולל ישוע, וכששמעו את הילדים הקטנים קוראים במקדש: ”הושע־נא לבן־דוד!“ הם התרגזו מאוד ושאלו אותו: 16”האם אתה שומע את מה שהילדים האלה אומרים?“

”כן“, ענה ישוע. ”האם מעולם לא קראתם בכתבי־הקודש:21‏.16 כא 16 תהלים ח 3 ’מפי עוללים ויונקים יסדת עֹז‘!“

17ישוע עזב אותם והלך לבית־עניה – שם נשאר ללון באותו לילה.

18כשחזר בבוקר לירושלים היה רעב. 19הוא ראה עץ תאנה בצד הדרך, אבל כשניגש לחפש תאנים מצא עלים בלבד. ”לעולם לא תישאי פרי!“ אמר ישוע לתאנה, ומיד התייבש העץ.

20התלמידים נדהמו ושאלו: ”כיצד יבשה התאנה לפתע?“

21וישוע ענה: ”אני אומר לכם: אם באמת תאמינו ולא תטילו ספק, תוכלו גם אתם לעשות דברים כאלה ואף גדולים מאלה. אפילו תוכלו לומר להר הזה: ’זוז, הזרק לים!‘ והוא ישמע בקולכם. 22תוכלו לקבל כל דבר שתבקשו בתפילה – אם רק תאמינו.“

23כשחזר ישוע לבית־המקדש ולימד את העם, באו אליו ראשי הכוהנים וזקני העם, ודרשו לדעת באיזו רשות הוא עושה את כל הדברים האלה.

24”אני אענה לשאלתכם אם אתם תענו לשאלתי“, השיב להם ישוע.

25”האם יוחנן המטביל נשלח על־ידי אלוהים או לא?“

הם התייעצו ביניהם: ”אם נאמר שאלוהים שלח את יוחנן, הוא ישאל אותנו מדוע לא האמנו בו. 26ואם נאמר שאלוהים לא שלח את יוחנן, העם יתנפל עלינו, כי כולם חושבים שיוחנן היה נביא.“ 27לבסוף השיבו: ”איננו יודעים.“ אמר להם ישוע: ”אם כך, גם אני לא אענה לשאלתכם. 28אולם מה דעתכם: לאב אחד היו שני בנים. ’בני, לך היום לעבוד בכרם‘, ביקש האב מבנו הבכור. 29’אינני רוצה‘, השיב הבן, אבל אחר כך שינה את דעתו והלך לעבוד בכרם. 30הלך האב אל הבן הצעיר וחזר על בקשתו. ’טוב, אבא אני אלך‘, השיב הבן הצעיר, אולם לא הלך לכרם. 31מי מהשניים שמע בקול אביו?“

”הבן הבכור, כמובן“, השיבו.

”אני אומר לכם שהמוכסים והזונות יכנסו למלכות השמים לפניכם“, הסביר להם ישוע את המשל. 32”כי יוחנן המטביל אמר לכם לחזור בתשובה ולהאמין באלוהים, ואתם לא שבתם; בעוד שפושעים וזונות כן שבו בתשובה. גם לאחר שראיתם כיצד הם שבו, לא נהגתם כמוהם ולא האמנתם לדברי יוחנן.

33”הקשיבו עתה למשל הבא: בעל־אדמה נטע כרם, בנה גדר סביבו, הקים מגדל שמירה, הפקיד את הכרם בידי כורמים שכירים ונסע לארץ רחוקה.

34”בעת הבציר שלח בעל־הכרם אחדים מאנשיו אל הכורמים, כדי לאסוף את חלקו ביבול הענבים.

35”אולם הכורמים הכו את האחד, סקלו באבנים את השני והרגו את השלישי.

36”בעל־הכרם שלח קבוצה גדולה יותר של אנשים כדי לאסוף את היבול, אך גורלם היה כגורל קודמיהם. 37לבסוף שלח האיש את בנו, כי חשב שיכבדו אותו ויפחדו מפניו.

38”אולם כשראו הכורמים את הבן מרחוק, אמרו זה לזה: ’הנה בא יורש הכרם; הבה נהרוג אותו, וכך נזכה אנחנו בירושה!‘ 39הם גירשו את הבן מהכרם והרגו אותו.

40”כשישוב בעל־הכרם, מה לדעתכם יעשה לאותם כורמים?“

41השיבו המנהיגים: ”הוא יוציא להורג את השכירים הרעים, וייתן את הכרם לפועלים נאמנים יותר, אשר יתנו לו בזמן את היבול המגיע לו.“

42ישוע המשיך ואמר: ”האם מעולם לא קראתם בכתובים:21‏.42 כא 42 תהלים קיח 23

’אבן מאסו הבונים היתה לראש פינה,

מאת ה׳ היתה זאת; היא נפלאת בעינינו‘?

43”אני מתכוון לומר שאלוהים ייקח מכם את המלכות, וייתן אותה לעם אשר ייתן לו את חלקו ביבול. 44מי שייפול על האבן הזאת יתנפץ לרסיסים, ומי שתיפול עליו האבן ישחק לאבק.“

45כשהבינו ראשי הכוהנים והפרושים שישוע התכוון אליהם – כלומר, שהם היו הכורמים במשל – 46הם רצו לתפוס אותו, אבל פחדו לעשות דבר מפני ההמון אשר האמין כי ישוע הוא נביא.