Mateyu 19 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 19:1-30

Za Kuthetsa Ukwati

1Yesu atatsiriza kunena zinthu zimenezi, anachoka ku Galileya ndi kupita ku chigawo cha Yudeya mbali ina ya mtsinje wa Yorodani. 2Magulu akulu a anthu anamutsatira Iye, ndipo iwo anachiritsidwa pomwepo.

3Afarisi ena anabwera kwa Iye kudzamuyesa. Anamufunsa Iye nati, “Kodi ndikololedwa kuti mwamuna amuleke mkazi wake pa chifukwa china chilichonse?”

4Iye anayankha kuti, “Kodi simunawerenge kuti pachiyambi Mulungu analenga iwo, ‘mwamuna ndi mkazi?’ 5Ndipo anati, ‘Pa chifukwa ichi mwamuna adzasiya abambo ake ndi amayi ake nakaphatikana ndi mkazi wake, ndipo awiriwo adzakhala thupi limodzi.’ 6Motero salinso awiri ayi koma mmodzi. Nʼchifukwa chake chimene Mulungu wachimanga pamodzi munthu wina asachilekanitse.”

7Ndipo iwo anamufunsa nati, “Nanga nʼchifukwa chiyani Mose analamula kuti mwamuna azipatsa mkazi wake kalata ya chisudzulo ndi kumuchotsa?”

8Yesu anayankha kuti, “Mose anakulolezani kuti muzisudzula akazi anu chifukwa cha kuwuma mitima kwanu. Koma sizinali chotere kuyambira pachiyambi. 9Ine ndikuwuzani kuti aliyense amene asudzula mkazi wake, osati chifukwa cha chiwerewere nakakwatira mkazi wina, achita chigololo.”

10Ophunzira ake anati kwa Iye, “Ngati umu ndi mmene zilili pa mwamuna ndi mkazi, kuli bwino kusakwatira.”

11Yesu anayankha kuti, “Si aliyense amene angavomere chiphunzitso ichi, koma kwa okhawo amene achimvetsetsa. 12Pakuti ena ndi akuti sangakwatire chifukwa anabadwa motero, ena ali motero chifukwa chofulidwa ndi anthu ndipo ena anawukana ukwati chifukwa cha ufumu wakumwamba. Iye amene angalandire ichi alandire.”

Yesu Adalitsa Ana

13Pamenepo anabwera nawo ana kwa Yesu kuti awasanjike manja ndi kuwapempherera. Koma ophunzira ake anadzudzula amene anabweretsa anawo.

14Yesu anati, “Lolani ana abwere kwa Ine, ndipo musawaletse pakuti ufumu wakumwamba ndi wa iwo onga anawa.” 15Atasanjika manja ake pa anawo, anachokapo.

Mnyamata Wolemera ndi Ufumu wa Mulungu

16Taonani mnyamata wina anabwera kwa Yesu namufunsa kuti, “Aphunzitsi, ndi chinthu chiti chabwino chimene ndiyenera kuchita kuti ndipeze moyo wosatha?”

17Yesu anayankha kuti, “Ukundifunsiranji Ine za chinthu chimene ndi chabwino? Pali mmodzi yekha amene ndi wabwino. Ngati ukufuna kulowa mʼmoyo wosatha mvera malamulo.”

18Mnyamatayo anamufunsa kuti, “Ndi ati?”

Yesu anayankha kuti, “Usaphe, usachite chigololo, usabe, usapereke umboni onama, 19lemekeza abambo ako ndi amayi ako ndipo konda mnansi wako monga iwe mwini.”

20Mnyamatayo anati, “Zonsezi ndimazisunga, nanga chatsala ndi chiyani?”

21Yesu anayankha kuti, “Ngati ukufuna kukhala wangwiro, pita kagulitse katundu wako ndi kupereka kwa osauka, ndipo udzakhala ndi chuma kumwamba. Ukakachita zimenezi, ukabwere udzanditsate Ine.”

22Mnyamatayo atamva zimenezi, anachoka mokhumudwa, chifukwa anali ndi chuma chambiri.

23Pamenepo Yesu anati kwa ophunzira ake, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti nʼkovuta kuti olemera akalowe mu ufumu wakumwamba. 24Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”

25Ophunzira atamva zimenezi, anadabwa kwambiri ndipo anamufunsa kuti, “Nanga angapulumuke ndani?”

26Yesu anawayangʼana iwo nati, “Ndi anthu, izi nʼzosatheka, koma ndi Mulungu zinthu zonse zimatheka.”

27Petro anamuyankha Iye kuti, “Ife tinasiya zonse ndi kukutsatirani Inu! Nanga tsono ife tidzalandira chiyani?”

28Yesu anawawuza kuti, “Zoonadi, ndikuwuzani kuti pa nthawi yokonzanso zinthu zonse, pamene Mwana wa Munthu adzakhala pa mpando wake waufumu mu ulemerero wake kumwamba, inu amene mwanditsata Ine mudzakhalanso pa mipando khumi ndi iwiri yaufumu, kuweruza mafuko khumi ndi awiri a Israeli. 29Ndipo aliyense amene wasiya nyumba, kapena abale, kapena alongo, kapena bambo kapena mayi kapena mkazi, kapena ana, kapena minda chifukwa cha Ine adzalandira madalitso ochuluka ndi kulandiranso moyo wosatha. 30Koma ambiri amene ali oyambirira adzakhala omalizira, ndipo ambiri amene ndi omalizira adzakhala oyambirira.”

King James Version

Matthew 19:1-30

1And it came to pass, that when Jesus had finished these sayings, he departed from Galilee, and came into the coasts of Judaea beyond Jordan; 2And great multitudes followed him; and he healed them there.

3¶ The Pharisees also came unto him, tempting him, and saying unto him, Is it lawful for a man to put away his wife for every cause? 4And he answered and said unto them, Have ye not read, that he which made them at the beginning made them male and female, 5And said, For this cause shall a man leave father and mother, and shall cleave to his wife: and they twain shall be one flesh? 6Wherefore they are no more twain, but one flesh. What therefore God hath joined together, let not man put asunder. 7They say unto him, Why did Moses then command to give a writing of divorcement, and to put her away? 8He saith unto them, Moses because of the hardness of your hearts suffered you to put away your wives: but from the beginning it was not so. 9And I say unto you, Whosoever shall put away his wife, except it be for fornication, and shall marry another, committeth adultery: and whoso marrieth her which is put away doth commit adultery.

10¶ His disciples say unto him, If the case of the man be so with his wife, it is not good to marry. 11But he said unto them, All men cannot receive this saying, save they to whom it is given. 12For there are some eunuchs, which were so born from their mother’s womb: and there are some eunuchs, which were made eunuchs of men: and there be eunuchs, which have made themselves eunuchs for the kingdom of heaven’s sake. He that is able to receive it, let him receive it.

13¶ Then were there brought unto him little children, that he should put his hands on them, and pray: and the disciples rebuked them. 14But Jesus said, Suffer little children, and forbid them not, to come unto me: for of such is the kingdom of heaven. 15And he laid his hands on them, and departed thence.

16¶ And, behold, one came and said unto him, Good Master, what good thing shall I do, that I may have eternal life? 17And he said unto him, Why callest thou me good? there is none good but one, that is, God: but if thou wilt enter into life, keep the commandments. 18He saith unto him, Which? Jesus said, Thou shalt do no murder, Thou shalt not commit adultery, Thou shalt not steal, Thou shalt not bear false witness, 19Honour thy father and thy mother: and, Thou shalt love thy neighbour as thyself. 20The young man saith unto him, All these things have I kept from my youth up: what lack I yet? 21Jesus said unto him, If thou wilt be perfect, go and sell that thou hast, and give to the poor, and thou shalt have treasure in heaven: and come and follow me. 22But when the young man heard that saying, he went away sorrowful: for he had great possessions.

23¶ Then said Jesus unto his disciples, Verily I say unto you, That a rich man shall hardly enter into the kingdom of heaven. 24And again I say unto you, It is easier for a camel to go through the eye of a needle, than for a rich man to enter into the kingdom of God. 25When his disciples heard it, they were exceedingly amazed, saying, Who then can be saved? 26But Jesus beheld them, and said unto them, With men this is impossible; but with God all things are possible.

27¶ Then answered Peter and said unto him, Behold, we have forsaken all, and followed thee; what shall we have therefore? 28And Jesus said unto them, Verily I say unto you, That ye which have followed me, in the regeneration when the Son of man shall sit in the throne of his glory, ye also shall sit upon twelve thrones, judging the twelve tribes of Israel. 29And every one that hath forsaken houses, or brethren, or sisters, or father, or mother, or wife, or children, or lands, for my name’s sake, shall receive an hundredfold, and shall inherit everlasting life. 30But many that are first shall be last; and the last shall be first.