Mateyu 17 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 17:1-27

Maonekedwe Aulemerero a Yesu pa Phiri

1Patapita masiku asanu ndi limodzi Yesu anatenga Petro, Yakobo, ndi Yohane mʼbale wa Yakobo pa okha ndipo anakwera nawo pa phiri lalitali. 2Pamenepo Iye anasinthika maonekedwe ake pamaso pawo. Nkhope yake inawala ngati dzuwa ndipo zovala zake zinayera kuti mbuu. 3Nthawi yomweyo Mose ndi Eliya anaonekera kwa iwo akuyankhulana ndi Yesu.

4Petro anati kwa Yesu, “Ambuye ndi bwino kuti ife tikhale pano. Ngati mufuna ndidzamanga misasa itatu umodzi wanu, wina wa Mose ndi wina wa Eliya.”

5Iye akuyankhulabe, mtambo owala unawaphimba, ndipo mawu ochokera mu mtambo anati, “Uyu ndiye Mwana wanga amene ndimukonda ndipo ndikondwera naye kwambiri. Mumumvere Iye!”

6Ophunzira atamva zimenezi, anachita mantha nagwa pansi chafufumimba. 7Ndipo Yesu anabwera nawakhudza nati, “Dzukani, musaope.” 8Atayangʼana, sanaone wina aliyense kupatula Yesu yekha.

9Akutsika ku phiriko, Yesu anawalamula kuti, “Musawuze wina aliyense zimene mwaona, mpaka Mwana wa Munthu ataukitsidwa kwa akufa.”

10Ophunzira anamufunsa Iye kuti, “Nanga nʼchifukwa chiyani aphunzitsi amalamulo amati Eliya ayenera kukhala woyamba kubwera?”

11Yesu anayankha kuti, “Kunena zoona, Eliya adzayenera kubwera ndipo adzakonza zinthu zonse. 12Koma Ine ndikuwuzani inu kuti Eliya anabwera kale koma iwo sanamuzindikire ndipo anachita naye chilichonse chimene anafuna. Momwemonso iwo adzazunza Mwana wa Munthu.” 13Pamenepo ophunzira anazindikira kuti amawawuza za Yohane Mʼbatizi.

Yesu Achiritsa Wodwala Matenda Akugwa

14Atafika ku gulu la anthu, munthu wina anamuyandikira Yesu ndi kugwada pamaso pake. 15Iye anati, “Ambuye, muchitireni chifundo mwana wanga akudwala matenda akugwa ndipo akuvutika kwambiri. Kawirikawiri iye amagwa pa moto kapena mʼmadzi. 16Ine ndinabwera naye kwa ophunzira anu koma alephera kumuchiritsa.”

17Yesu anayankha nati, “Haa, mʼbado wosakhulupirira ndi wokhota maganizo! Kodi ndidzakhala nanu mpaka liti? Ndidzapirira nanu mpaka liti? Bwera nayeni kwa Ine mnyamatayo.” 18Yesu anadzudzula chiwandacho ndipo chinatuluka mwa mnyamatayo ndipo anachira nthawi yomweyo.

19Pamenepo ophunzira anabwera kwa Yesu mwamseri ndi kumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani ife tinalephera kutulutsa chiwandacho?”

20Iye anayankha kuti, “Chifukwa inu muli ndi chikhulupiriro chachingʼono. Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti ngati muli ndi chikhulupiriro monga kambewu ka mpiru, mukhoza kunena ndi phiri ili kuti, ‘Choka apa nupite apo,’ ndipo lidzachoka. Palibe kanthu kamene kadzakukanikani. 21Chiwanda cha mtundu uwu sichingachoke chabe koma ndi pemphero ndi kusala kudya.”

Yesu Anena za Imfa yake Kachiwiri

22Atasonkhana pamodzi ku Galileya, Iye anawawuza kuti, “Mwana wa Munthu akupita kukaperekedwa mʼmanja mwa anthu. 23Iwo adzamupha koma pa tsiku lachitatu adzaukitsidwa.” Ndipo ophunzira anadzazidwa ndi chisoni.

Yesu Apereka Msonkho

24Yesu ndi ophunzira ake atafika ku Kaperenawo, wolandira msonkho wa ku Nyumba ya Mulungu anabwera kwa Petro namufunsa kuti, “Kodi aphunzitsi anu sapereka msonkho wa Nyumba ya Mulungu?”

25Iye anayankha kuti, “Inde amapereka.”

Petro atalowa mʼnyumba, Yesu ndiye anayamba kuyankhula. Ndipo anamufunsa kuti, “Ukuganiza bwanji Simoni, kodi mafumu a dziko lapansi amalandira msonkho kuchokera kwa ana awo kapena kwa ena?”

26Petro anayankha kuti, “Kuchokera kwa ena.”

Yesu ananena kwa iye kuti, “Ndiye kuti ana sapereka.” 27Koma kuti ife tisawakhumudwitse pita ku nyanja kaponye mbedza yako. Katenge nsomba imene ukayambe kuyikola; kayitsekule kukamwa ndipo ukapezamo ndalama. Katenge ndalamayo ndi kukapereka msonkho wanga ndi wanu.

New Russian Translation

Матфея 17:1-27

Преображение

(Мк. 9:2-13; Лк. 9:28-36)

1Через шесть дней Иисус взял с Собой Петра, Иакова, его брата Иоанна и привел их одних на высокую гору. 2И на глазах учеников вдруг Его облик изменился: лицо Его засияло, как солнце, а одежда стала белой, как свет. 3И вот они увидели Моисея и Илию, беседующих с Ним. 4Петр сказал:

– Господи, нам здесь так хорошо! Если Ты хочешь, я сделаю три шалаша: один Тебе, один Моисею и один Илии.

5Пока он говорил, светлое облако накрыло их, и из облака прозвучал голос:

– Это Мой любимый Сын, в Котором Моя радость. Слушайте Его!

6Услышав эти слова, ученики в ужасе пали на лица свои. 7Иисус подошел и прикоснулся к ним:

– Встаньте, не бойтесь.

8Они подняли взгляд и уже никого, кроме Иисуса, не увидели. 9Когда они спускались с горы, Иисус сказал им:

– Никому не говорите о том, что вы видели здесь, до тех пор, пока Сын Человеческий не воскреснет из мертвых.

10Ученики спросили Его:

– Почему же учители Закона говорят, что вначале, перед Мессией, должен прийти Илия?

11Иисус ответил:

– Илия действительно должен прийти и все приготовить17:11 См. Мал. 4:5-6.. 12Но, говорю вам, что Илия уже пришел17:12 См. Лк. 1:13-17., только его не узнали и поступили с ним по своему произволу. Так же и Сыну Человеческому предстоит пострадать от их рук.

13Тогда ученики поняли, что Он говорил об Иоанне Крестителе.

Исцеление мальчика, одержимого нечистым духом

(Мк. 9:14-29; Лк. 9:37-42)

14Когда они подошли к месту, где собралась толпа, один мужчина пал перед Иисусом на колени 15со словами:

– Господи, сжалься над моим сыном, у него судороги, и он сильно мучается, часто бросается то в огонь, то в воду. 16Я привел его к Твоим ученикам, но они не смогли исцелить его.

17Иисус в ответ сказал:

– О неверующее и испорченное поколение! Сколько Мне еще быть с вами? Сколько Мне еще терпеть вас? Приведите мальчика ко Мне.

18Иисус приказал демону выйти, и тот вышел из мальчика; в тот же миг ребенок стал совершенно здоров. 19Потом, оставшись с Иисусом наедине, ученики спросили:

– Почему же мы не смогли изгнать его?

20Иисус ответил:

– Потому что у вас мало веры. Говорю вам истину: если бы ваша вера была с горчичное зерно, то вы могли бы этой горе сказать: «Передвинься отсюда туда», и она бы передвинулась; для вас не было бы ничего невозможного. 21Этот же вид демонов изгоняется только молитвой и постом17:21 В некоторых рукописях отсутствуют эти слова..

Иисус снова предсказывает Свою смерть и воскресение

(Мк. 9:30-32; Лк. 9:43-45)

22Во время пребывания в Галилее Иисус сказал ученикам:

– Сын Человеческий будет предан в руки людей, 23которые убьют Его, но на третий день Он воскреснет.

Учеников это сильно опечалило.

Налог на храм

24Когда они вернулись в Капернаум, к Петру подошли сборщики налога на нужды храма и спросили:

– А ваш Учитель платит налог на храм?

25– Платит, – ответил он.

Петр вошел в дом и еще не успел ничего сказать, как Иисус спросил:

– Симон, как тебе кажется, с кого земные цари взимают пошлины или дань, со своих сыновей или с чужеземцев?

26– С чужеземцев, – ответил Петр.

– Значит, сыновья17:26 То есть граждане. свободны, – заключил Иисус. – 27Но чтобы нам никого не обидеть, пойди к озеру, забрось удочку, вытащи первую рыбу, что попадется на крючок, открой ей рот, и там ты найдешь монету достоинством в четыре драхмы. Возьми ее и заплати за Меня и за себя.