Mateyu 14 – CCL & CCB

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 14:1-36

Kuphedwa kwa Yohane Mʼbatizi

1Pa nthawi imeneyo Mfumu Herode anamva za mbiri ya Yesu. 2Ndipo iye anati kwa antchito ake, “Uyu ndi Yohane Mʼbatizi; iye wauka kwa akufa! Ichi ndi chifukwa chake mphamvu zodabwitsa zikugwira ntchito mwa iye.”

3Pakuti Herode anamugwira Yohane ndi kumumanga ndipo anamuyika mʼndende chifukwa cha Herodia mkazi wa mʼbale wake Filipo. 4Chifukwa Yohane anakhala akunena kwa iye kuti, “Sichololedwa kwa inu kutenga mkaziyo.” 5Herode anafuna kupha Yohane koma iye anaopa anthu chifukwa anamuyesa iye mneneri.

6Pa tsiku lokumbukira kubadwa kwa Herode, mwana wamkazi wa Herodia anavina pamaso pa anthu ndipo anasangalatsa kwambiri. 7Kotero Herode analonjeza ndi lumbiro kumupatsa chilichonse chimene mwanayo angamupemphe. 8Ndipo atamupangira amayi ake anati, “Mundipatse pomwe pano mutu wa Yohane Mʼbatizi mʼmbale.” 9Mfumuyo inamva chisoni koma chifukwa cha lumbiro lake ndi alendo amene anali pa phwando lake analamulira kuti chofuna chake chipatsidwe; 10ndipo anakadula mutu wa Yohane mʼndende. 11Mutu wake anawubweretsa mʼmbale ndi kumupatsa mtsikanayo amene anawutengera kwa amayi ake. 12Ophunzira a Yohane anabwera nadzatenga mtembo wake ndi kukawuyika mʼmanda. Pomwepo iwo anapita kukamuwuza Yesu.

Yesu Adyetsa Anthu 5,000

13Yesu atamva zimene zinachitika, anachoka pa bwato mwachinsinsi kupita kumalo a yekha. Magulu a anthu atamva izi anamutsatira Iye poyenda pansi kuchokera ku mizinda. 14Yesu atafika ku mtunda, ndi kuona gulu lalikulu la anthu, Iye anamva nawo chifundo ndipo anachiritsa odwala awo.

15Kutayamba mdima, ophunzira anabwera kwa Iye nati, “Kuno ndi kutchire ndipo kwayamba kale kuda. Awuzeni anthu azipita kuti afike ku midzi ndi kukadzigulira zakudya.”

16Yesu anawayankha kuti, “Sikofunika kuti azipita. Inuyo muwapatse kanthu kuti adye.”

17Iwo anayankha kuti, “Tili ndi malofu asanu okha a buledi ndi nsomba ziwiri.”

18Koma Iye anati, “Bweretsani kwa Ine.” 19Analamula anthu kuti akhale pansi pa udzu ndipo anatenga buledi musanu ndi nsomba ziwiri nayangʼana kumwamba, nayamika nagawa bulediyo. Kenaka anapereka bulediyo kwa ophunzira ake ndipo ophunzirawo anagawira anthu. 20Onse anadya nakhuta ndipo ophunzira anatola zotsalira ndi kudzaza madengu khumi ndi awiri. 21Chiwerengero cha amene anadya kupatulako amayi ndi ana chinali pafupifupi amuna 5,000.

Yesu Ayenda pa Nyanja

22Nthawi yomweyo anawawuza ophunzira ake kuti alowe mʼbwato ndi kuti atsogole kupita kutsidya lina pamene Iye ankawuza anthu kuti azipita kwawo. 23Atatha kuwawuza kuti azipita kwawo, Iye anakwera ku phiri yekha kukapemphera. Pamene kumada anali kumeneko yekha. 24Pamenepo nʼkuti bwato litapita patali pangʼono kuchokera ku mtunda ndipo linavutika ndi mafunde chifukwa mphepo inkawomba mokumana nalo.

25Pa ora lachinayi usiku, Yesu anabwera kwa iwo akuyendabe pa nyanja. 26Ophunzira atamuona akuyenda pa nyanja, anaopa nati, “Ndi mzukwa!” Ndipo analira chifukwa cha mantha.

27Koma Yesu nthawi yomweyo anawawuza kuti, “Limbani mtima! Ndine, musaope.”

28Petro anayankha nati, “Ambuye ngati ndinu, mundiwuze ndibwere kuli inuko pa madzipo.”

29Iye anati, “Bwera.”

Pamenepo Petro anatuluka mʼbwato ndipo anayenda pa madzi kupita kwa Yesu. 30Koma ataona mphepo, iye anachita mantha ndipo anayamba kumira, nafuwula nati, “Ambuye ndipulumutseni!”

31Ndipo mofulumira Yesu anatambasula dzanja lake namugwira iye, nati, “Iwe wachikhulupiriro chochepa, bwanji unakayika?”

32Ndipo atalowa mʼbwato mphepo inaleka. 33Pamenepo amene anali mʼbwato anamulambira Iye, nati, “Zoonadi, Inu ndinu Mwana wa Mulungu.”

34Atawoloka, anafika ku Genesareti. 35Anthu akumeneko atamuzindikira Yesu, iwo anatumiza mawu kwa onse ozungulira deralo. Anthu anabwera ndi odwala awo onse kwa Iye. 36Ndipo anamupempha alole kuti akhudze mphonje ya mkanjo wake, ndipo onse amene anamukhudza anachiritsidwa.

Chinese Contemporary Bible (Simplified)

马太福音 14:1-36

施洗者约翰之死

1分封王希律听见耶稣的名声, 2就对臣仆说:“这个人是施洗者约翰!他从死里复活了,所以能够行这些神迹。”

3原来希律为他兄弟腓力的妻子希罗底的缘故,拘捕了约翰,把他捆绑起来关在监里。 4因为约翰曾多次对他说:“你娶这个妇人是不对的。” 5他想杀掉约翰,但怕触怒百姓,因为他们都认为约翰是先知。

6希律的生日那天,希罗底的女儿出来在众人面前跳舞。希律非常高兴, 7就起誓答应她无论要什么都可以。 8她受了母亲的指使,说:“请把施洗者约翰的头放在盘子里送给我。” 9希律感到为难,但既然在众宾客面前起了誓,只好下令给她。 10他派人到监里砍了约翰的头, 11放在盘子里送给她,她转送给她母亲。 12约翰的门徒把尸体领回安葬后,就去告诉耶稣。

13耶稣听见这个消息,就独自坐船退到一处偏僻的地方。众人得知后,就从各城步行来跟随祂。

耶稣使五千人吃饱

14耶稣上了岸,看见一大群人,心里怜悯他们,就治好了他们当中的病人。 15黄昏时,门徒过来对耶稣说:“这里是荒郊野外,天又晚了,请遣散众人,好让他们到村庄去自己买些吃的。”

16耶稣回答说:“他们不用离开,你们给他们吃的吧。”

17门徒答道:“我们这里只有五个饼和两条鱼。”

18耶稣说:“拿来给我。”

19于是,祂叫众人坐在草地上,然后拿起那五个饼和两条鱼,举目望着天祝谢后,就掰开饼递给门徒,让他们分给众人。 20大家都吃饱了,把剩下的零碎收拾起来,竟装满了十二个篮子。 21当时吃饭的,除了妇女和小孩,约有五千男人。

耶稣在水上行走

22随后,耶稣催门徒上船,叫他们先渡到湖对岸,祂则遣散众人。 23待众人都离开了,祂就独自上山去祷告,在那里一直待到晚上。

24那时,门徒的船离岸已远,遇到逆风,船身被波浪撞击得摇摆不定。 25天将破晓的时候,耶稣从水面上向门徒走去。 26门徒看见有人在湖面上走,都吓坏了,说:“是幽灵!”他们害怕得又喊又叫。

27耶稣立刻对他们说:“放心吧!是我,不要怕。”

28彼得说:“主啊!如果真的是你,就叫我从水面上走到你那里。”

29耶稣说:“好,你来吧!”

于是,彼得就从船上下去,走在湖面上,要去耶稣那里。 30他看到风浪很大,就害怕起来,身体开始往下沉,便大喊:“主啊,救我!”

31耶稣马上伸手拉住他,说:“你信心太小了!为什么怀疑呢?”

32他们上了船,风浪就平静了。 33船上的人都敬拜祂,说:“你真是上帝的儿子。”

34他们渡到湖对岸,来到革尼撒勒35当地的人认出是耶稣,就派人去把附近所有的病人都带到祂面前, 36求耶稣让他们摸一摸祂衣裳的穗边,所有摸过的病人都好了。