Mateyu 13 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 13:1-58

Fanizo la Wofesa Mbewu

1Tsiku lomwelo Yesu anatuluka mʼnyumba ndipo anakhala mʼmbali mwa nyanja. 2Magulu a anthu anasonkhana mozungulira ndipo Iye analowa mʼbwato nakhala pansi ndipo anthu onse anayimirira ku mtunda. 3Pamenepo Iye anawawuza zinthu zambiri mʼmafanizo ndi kuti, “Mlimi anapita kukafesa mbewu zake. 4Akufesa, zina zinagwera mʼmbali mwa njira ndipo mbalame zinabwera ndi kuzidya. 5Zina zinagwa pamalo a miyala pamene panalibe dothi lambiri. Zinamera mofulumira chifukwa panalibe dothi lambiri. 6Koma dzuwa litakwera, mbewu zinapserera ndipo zinawuma chifukwa zinalibe mizu. 7Mbewu zina zinagwa pa minga ndipo mingayo inayanga ndi kuzirepheretsa kukula. 8Koma mbewu zina zinagwa pa nthaka yabwino ndipo zinabala zipatso 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa. 9Amene ali ndi makutu amve.”

10Ophunzira anabwera kwa Iye ndikumufunsa kuti, “Chifukwa chiyani Inu mukuyankhula kwa anthu mʼmafanizo?”

11Iye anayankha kuti, “Nzeru zakudziwa zinsinsi za ufumu wakumwamba zapatsidwa kwa inu koma osati kwa iwo. 12Aliyense amene ali nazo adzapatsidwa zowonjezera ndipo iye adzakhala nazo zambiri. Aliyense amene alibe, ngakhale zimene ali nazo adzamulanda. 13Ichi ndi chifukwa chake ndimayankhula kwa iwo mʼmafanizo:

“Ngakhale akupenya koma saona,

ngakhale akumva koma samvetsetsa kapena kuzindikira.

14Mwa iwo zimene ananenera Yesaya zikwaniritsidwa:

“ ‘Kumva mudzamva koma osamvetsetsa.

Kupenya mudzapenya koma osaona kanthu.

15Pakuti mtima wa anthu awa ndi wokanika,

mʼmakutu mwawo ndi mogontha,

ndipo atsinzina

kuti asaone kanthu.

Mwina angapenye ndi maso awo,

angamve ndi makutu awo, angamvetse ndi nzeru zawo ndi kutembenuka,

Ineyo nʼkuwachiritsa.’

16Koma maso anu ndi odala chifukwa amapenya ndi makutu anu chifukwa amamva. 17Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti aneneri ambiri ndi anthu olungama anafuna kuona zimene inu mukupenya koma sanazione ndi kumva zimene inu mukumva koma sanazimve.

Tanthauzo la Fanizo la Wofesa

18“Tamverani tsono zimene fanizo la wofesa litanthauza: 19Pamene aliyense akumva uthenga wa ufumu koma sawuzindikira, woyipayo amabwera ndi kuchotsa zimene zafesedwa mu mtima mwake. Iyi ndi mbewu yofesedwa mʼmbali mwa njira. 20Zimene zinafesedwa pa malo amiyala ndi munthu amene amamva mawu ndi kuwalandira msanga ndi chimwemwe. 21Koma popeza alibe muzu, iwo amakhala nthawi yochepa. Pamene vuto kapena zunzo libwera chifukwa cha mawu, iye amagwa mofulumira. 22Zimene zinafesedwa pakati pa minga, ndi munthu amene amamva mawu koma nkhawa za moyo uno ndi chinyengo cha chuma zimalepheretsa mawuwo kuti abale chipatso. 23Koma zimene zinafesedwa pa nthaka yabwino, ndi munthu amene amamva mawu ndipo amawazindikira. Iye amabala zipatso zokwanira 100, zina 60 ndipo zinanso makumi atatu mwa zimene zinafesedwa.”

Fanizo la Namsongole

24Yesu anawawuza fanizo lina kuti: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi munthu amene anafesa mbewu zabwino mʼmunda mwake. 25Koma aliyense akugona usiku mdani wake anabwera ndi kufesa namsongole pakati pa tirigu ndipo anachoka. 26Pamene tirigu anamera ndi kutulutsa ngala, namsongole anaonekanso.

27“Antchito ake anabwera kwa iye ndi kuti, ‘Bwana, kodi simunafese mbewu zabwino mʼmunda mwanu? Nanga namsongole wachokera kuti?’

28“Iye anayankha kuti, ‘Ndi mdani amene anachita izi.’

“Antchito anamufunsa iye kuti, ‘Kodi mufuna kuti tipite tikamuzule?’

29“Iye anakana nati, ‘Ayi. Chifukwa pamene mukuzula namsongoleyo mwina inu mungazulire pamodzi ndi tirigu. 30Zisiyeni zonse zikulire pamodzi mpaka nthawi yokolola. Pa nthawi imeneyo ndidzawuza okolola kuti: Poyamba sonkhanitsani namsongole ndi kumumanga mʼmitolo kuti atenthedwe, kenaka sonkhanitsani tirigu ndi kumuyika mʼnkhokwe yanga.’ ”

Fanizo la Mbewu ya Mpiru ndi Yisiti

31Iye anawawuza fanizo lina kuti, “Ufumu wakumwamba uli ngati mbewu ya mpiru, imene munthu anatenga ndi kudzala mʼmunda mwake. 32Ngakhale mbewuyi ndi yayingʼono mwa mbewu zanu zonse za mʼmunda, imakula ndi kukhala mtengo kotero kuti mbalame zamlengalenga zimabwera ndi kupumula mʼnthambi zake.”

33Iye anawawuzanso fanizo lina nati: “Ufumu wakumwamba ufanana ndi yisiti amene mayi anatenga ndi kusakaniza mu ufa wambiri mpaka wonse unafufuma.”

34Yesu anayankhula zinthu zonsezi kwa gulu la anthu mʼmafanizo ndipo Iye sananene kalikonse kwa iwo osagwiritsa ntchito fanizo. 35Kotero zinakwaniritsidwa zimene zinayankhulidwa ndi mneneri kuti,

“Ndidzatsekula pakamwa panga ndi mafanizo,

ndidzawulula zinthu zobisika

chiyambire kukhazikidwa kwa dziko lapansi.”

Yesu Awatanthauzira Fanizo la Namsongole

36Kenaka Iye anasiya gulu la anthu ndi kukalowa mʼnyumba. Ophunzira ake anapita kwa Iye nati, “Timasulireni fanizo la namsongole mʼmunda.”

37Iye anayankha nati, “Munthu amene anafesa mbewu yabwino ndi Mwana wa Munthu. 38Munda ndi dziko lapansi ndipo mbewu yabwino ndi ana a ufumu. Namsongole ndi ana a woyipayo. 39Ndipo amene anafesa namsongole ndi Satana. Kukolola ndiko kutha kwa dzikoli ndipo otuta ndi angelo.

40“Monga momwe namsongole azulidwa ndi kutenthedwa ndi moto, momwemonso kudzakhala pakutha kwa dziko. 41Mwana wa Munthu adzatumiza angelo ake ndipo iwo adzachotsa mu ufumu wake chilichonse chochimwitsa ndi onse amene amachita zoyipa. 42Adzawaponya mʼngʼanjo yamoto kumene kudzakhala kulira ndi kukuta mano. 43Pamenepo olungama adzawala ngati dzuwa mu ufumu wa Atate awo. Amene ali ndi makutu amve.”

Fanizo la Chuma Chobisika ndi la Ngale

44“Ufumu wakumwamba ufanana ndi chuma chobisika mʼmunda. Munthu atachipeza anachibisanso ndipo ndi chimwemwe anapita nakagulitsa zonse anali nazo, nakagula mundawo.

45“Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi wogulitsa malonda amene amafuna ngale zabwino. 46Atapeza imodzi ya mtengowapatali, iye anapita nakagulitsa chilichonse anali nacho ndi kukayigula.”

Fanizo la Khoka

47“Komanso Ufumu wakumwamba ufanana ndi khoka limene linaponyedwa mʼnyanja ndipo linakola mitundu yonse ya nsomba. 48Litadzaza, asodzi analikokera ku mtunda. Pomwepo anakhala pansi nasonkhanitsa nsomba zabwino mʼmadengu koma zoyipa anazitaya. 49Umu ndi mmene kudzakhalira pakutha kwa dziko. Angelo adzabwera ndi kulekanitsa oyipa ndi olungama. 50Ndipo oyipa adzawaponya mʼngʼanjo ya moto kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.”

51Yesu anawafunsa kuti, “Kodi mwamvetsetsa zonsezi?”

Iwo anayankha kuti, “Inde.”

52Iye anawawuza kuti, “Chifukwa chake mphunzitsi aliyense wa malamulo amene walangizidwa za ufumu wakumwamba ali ngati mwini nyumba amene amatulutsa chuma chatsopano komanso chakale.”

Amupeputsa Yesu ku Nazareti

53Yesu atatsiriza mafanizowa anachoka kumeneko. 54Atafika ku mudzi kwawo anayamba kuphunzitsa mʼmasunagoge awo ndipo iwo anadabwa nati, “Munthu uyu anayitenga kuti nzeru iyi ndi mphamvu zodabwitsazi? 55Kodi si mwana wa wopala matabwa? Kodi dzina la amayi ake si Mariya ndipo kodi abale ake si Yakobo, Yosefe, Simoni ndi Yudasi? 56Kodi alongo ake onse sali ndi ife? Tsono ndi kuti kumene anazitenga zinthu izi?” 57Ndipo iwo anakhumudwa chifukwa cha Iye.

Koma Yesu anawawuza kuti, “Mneneri sapatsidwa ulemu ku mudzi kwawo ndi ku nyumba kwawo.”

58Ndipo Iye sanachite zodabwitsa zambiri kumeneko chifukwa cha kusowa kwa chikhulupiriro kwawo.