Mateyu 10 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Mateyu 10:1-42

Yesu Atuma Ophunzira Ake

1Yesu anayitana ophunzira ake khumi ndi awiri ndipo anawapatsa ulamuliro otulutsa mizimu yoyipa ndi kuchiritsa nthenda iliyonse ndi zofowoka zilizonse.

2Mayina a atumwi khumi ndi awiriwo ndi awa: woyamba, Simoni (wotchedwa Petro) ndi mʼbale wake Andreya; Yakobo mwana wa Zebedayo ndi mʼbale wake Yohane, 3Filipo ndi Bartumeyu, Tomasi ndi Mateyu wolandira msonkho, Yakobo mwana wa Alufeyo ndi Tadeyo; 4Simoni Mzerote ndi Yudasi Isikarioti, amene anamupereka Iye.

5Yesu anatuma khumi ndi awiriwo ndi kuwalamula kuti, “Musapite kwa anthu a mitundu ina kapena kulowa mʼmudzi uliwonse wa Asamariya. 6Koma pitani kwa nkhosa zotayika za banja la Israeli. 7Pamene mukupita, muzikalalikira uthenga uwu: ‘Ufumu wakumwamba wayandikira.’ 8Chiritsani odwala, ukitsani akufa, chiritsani akhate, tulutsani ziwanda. Munalandira kwaulere, perekani kwaulere.

9“Musatenge ndalama zagolide kapena zasiliva kapena zakopala mʼzikwama mwanu; 10musatenge thumba la paulendo, kapena malaya awiri kapena nsapato kapena ndodo; pakuti wantchito ayenera kulandira chakudya chake. 11Mukalowa mu mzinda ndi mʼmudzi uliwonse, funafunani munthu woyenera ndipo mukhale mʼnyumba mwake kufikira mutachoka. 12Pamene mulowa mʼnyumba mupereke moni. 13Mtendere wanu ukhale pa a mʼnyumbayo ngati ndi oyenera. Koma ngati siwoyenera, mtendere wanu ubwerere kwa inu. 14Ngati wina aliyense sakakulandirani kapena sakamvera mawu anu, musase fumbi la kumapazi anu pamene mutuluka mʼnyumbayo kapena mu mzindawo. 15Zoonadi, Ine ndikuwuzani kuti pa tsiku lachiweruziro, mlandu wa Sodomu ndi Gomora udzachepa kusiyana ndi wa mzindawo.

16“Taonani ndikukutumizani inu monga nkhosa pakati pa mimbulu. Chifukwa chake khalani ochenjera ngati njoka ndi woona mtima ngati nkhunda. 17Chenjerani ndi anthu pakuti adzakuperekani ku mabwalo amilandu nadzakukwapulani mʼmasunagoge mwawo. 18Chifukwa cha Ine, mudzaperekedwa kwa olamulira ndi kwa mafumu kuti mukhale mboni kwa iwo ndi kwa a mitundu ina. 19Koma pamene akumangani, inu musadandaule kuti mukanena bwanji kapena mukanena chiyani. Mudzapatsidwa pa nthawi imeneyo zoti munene, 20pakuti sindinu mudzanena, koma Mzimu Woyera wa Atate anu, adzayankhula mwa inu.

21“Mʼbale adzapereka mʼbale kuti aphedwe ndi abambo mwana wawo: ndipo ana adzawukira makolo awo ndi kuwapereka kuti aphedwe. 22Anthu onse adzada inu chifukwa cha Ine, koma iye amene apirira mpaka kumapeto, adzapulumuka. 23Pamene akuzunzani pamalo ena thawirani kwina. Pakuti ndikuwuzani zoonadi kuti simudzamaliza mizinda yonse ya Israeli Mwana wa Munthu asanabwere.

24“Wophunzira saposa mphunzitsi wake ndipo wantchito saposa bwana wake. 25Nʼkoyenera kuti wophunzira akhale ngati mphunzitsi wake, ndi wantchito akhale ngati bwana wake. Ngati mwini banja atchedwa Belezebabu, koposa kotani a mʼnyumba mwake!

26“Chifukwa chake musaope iwo. Pakuti palibe chinthu chobisika chimene sichidzavundukulidwa, ndi chobisika chimene sichidzadziwika. 27Chimene ndikuwuzani Ine mu mdima, muchiyankhule poyera; chimene akunongʼonezani mʼkhutu, muchilalikire muli pa denga. 28Musamaope amene amapha thupi koma sangathe kuchotsa moyo. Koma muziopa Iye amene akhoza kupha mzimu ndi kuwononga thupi mu gehena. 29Kodi suja amagulitsa mbalame ziwiri ndi ndalama imodzi? Koma palibe imodzi ya izo imene idzagwa pansi wopanda chifuniro cha Atate anu. 30Ndipo ngakhale tsitsi la mʼmutu mwanu linawerengedwa kale. 31Potero musaope; inu ndinu a mtengo woposa mbalame zambiri.

32“Aliyense amene avomereza Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzavomereza pamaso pa Atate anga akumwamba. 33Koma iye amene andikana Ine pamaso pa anthu, Inenso ndidzamukana pamaso pa Atate anga akumwamba.

34“Musaganize kuti Ine ndabweretsa mtendere pa dziko lapansi. Sindinabwere kudzapereka mtendere koma lupanga. 35Pakuti Ine ndabwera kudzalekanitsa

“ ‘Munthu ndi abambo ake,

mwana wamkazi ndi amayi ake,

mtengwa kulekanitsidwa ndi apongozi ake,

36adani a munthu adzakhala a mʼbanja mwake momwe.’

37“Aliyense amene akonda abambo kapena amayi ake koposa Ine sayenera kukhala wanga; aliyense amene akonda mwana wake wamwamuna kapena wamkazi koposa Ine sayenera kukhala wanga. 38Aliyense amene satenga mtanda wake ndi kunditsata Ine sayenera kukhala wanga. 39Aliyense amene asunga moyo wake adzawutaya koma aliyense amene ataya moyo chifukwa cha Ine adzawupeza.

40“Iye amene alandira inu alandira Ine, ndipo amene alandira Ine alandiranso amene anandituma Ine. 41Aliyense amene alandira mneneri chifukwa chakuti ndi mneneri alandira mphotho ya mneneri, ndipo aliyense amene alandira munthu wolungama chifukwa chakuti ndi munthu wolungama, adzalandira mphotho ya wolungama. 42Ngati aliyense apereka madzi ozizira a mʼchikho kwa mmodzi wa angʼonoangʼono awa chifukwa cha kuti ndi ophunzira anga, ndikuwuzani zoona, ndithudi sadzataya mphotho yake.”