Masalimo 97 – CCL & NIRV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 97:1-12

Salimo 97

1Yehova akulamulira, dziko lapansi lisangalale;

magombe akutali akondwere.

2Mitambo ndi mdima waukulu zamuzungulira;

chilungamo ndi kuweruza molungama ndiwo maziko a mpando wake waufumu.

3Moto umapita patsogolo pake

ndi kunyeketsa amaliwongo kumbali zonse.

4Zingʼaningʼani zake zimawalitsa dziko lonse;

dziko lapansi limaona ndipo limanjenjemera.

5Mapiri amasungunuka ngati phula pamaso pa Yehova,

pamaso pa Ambuye a dziko lonse lapansi.

6Mayiko akumwamba amalengeza za chilungamo chake,

ndipo mitundu yonse ya anthu imaona ulemerero wake.

7Onse amene amalambira mafano osema amachititsidwa manyazi,

iwo amene amanyadira mafano;

mulambireni, inu milungu yonse!

8Ziyoni akumva ndipo akukondwera,

midzi ya Yuda ikusangalala

chifukwa cha maweruzo anu Yehova.

9Pakuti Inu Yehova ndi Wammwambamwamba pa dziko lonse lapansi;

ndinu wokwezeka kupambana milungu yonse.

10Iwo amene amakonda Yehova adane ndi zoyipa

pakuti Iye amayangʼanira miyoyo ya amene amamukhulupirira

ndipo amawapulumutsa mʼdzanja la anthu oyipa

11Kuwala kumafika pa anthu olungama,

ndi chimwemwe kwa olungama mtima.

12Kondwerani mwa Yehova Inu olungama

ndipo tamandani dzina lake loyera.

New International Reader’s Version

Psalm 97:1-12

Psalm 97

1The Lord rules. Let the earth be glad.

Let countries that are far away be full of joy.

2Clouds and thick darkness surround him.

His rule is built on what is right and fair.

3The Lord sends fire ahead of him.

It burns up his enemies all around him.

4His lightning lights up the world.

The earth sees it and trembles.

5The mountains melt like wax when the Lord is near.

He is the Lord of the whole earth.

6The heavens announce that what he does is right.

All people everywhere see his glory.

7All who worship statues of gods or brag about them are put to shame.

All you gods, worship the Lord!

8Zion hears about it and is filled with joy.

Lord, the villages of Judah are glad

because of how you judge.

9Lord, you are the Most High God.

You rule over the whole earth.

You are honored much more than all gods.

10Let those who love the Lord hate evil.

He guards the lives of those who are faithful to him.

He saves them from the power of sinful people.

11Good things come to those who do what is right.

Joy comes to those whose hearts are honest.

12You who are godly, be glad because of what the Lord has done.

Praise him, because his name is holy.