Masalimo 96 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 96:1-13

Salimo 96

1Imbirani Yehova nyimbo yatsopano;

Imbirani Yehova dziko lonse lapansi.

2Imbirani Yehova, tamandani dzina lake;

lalikirani chipulumutso chake tsiku ndi tsiku.

3Lengezani ulemerero wake pakati pa mayiko,

ntchito zake zodabwitsa pakati pa mitundu yonse ya anthu.

4Pakuti wamkulu ndi Yehova ndipo ndi woyenera kwambiri kumutamanda;

ayenera kuopedwa kupambana milungu yonse.

5Pakuti milungu yonse ya anthu a mitundu ina ndi mafano,

koma Yehova analenga mayiko akumwamba.

6Ulemu ndi ufumu zili pamaso pake,

mphamvu ndi ulemerero zili mʼmalo ake opatulika.

7Perekani kwa Yehova, inu mabanja a anthu a mitundu ina,

perekani kwa Yehova ulemerero ndi mphamvu.

8Perekani kwa Yehova ulemerero woyenera dzina lake;

bweretsani chopereka ndipo mulowe mʼmabwalo ake.

9Lambirani Yehova mu ulemerero wa chiyero chake;

njenjemerani pamaso pake, dziko lonse lapansi.

10Nenani pakati pa mitundu ya anthu, “Yehova akulamulira.”

Dziko lonse lakhazikika molimba, silingasunthidwe;

Iye adzaweruza mitundu ya anthu molungama.

11Mayiko akumwamba asangalale, dziko lapansi likondwere;

nyanja ikokome, ndi zonse zili mʼmenemo;

12minda ikondwere pamodzi ndi chilichonse chili mʼmenemo.

Pamenepo mitengo yonse ya mʼnkhalango idzayimba ndi chimwemwe;

13idzayimba pamaso pa Yehova,

pakuti Iye akubwera kudzaweruza dziko lapansi;

adzaweruza dziko lonse mwachilungamo

ndi mitundu ya anthu onse mʼchoonadi.