Masalimo 95 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 95:1-11

Salimo 95

1Bwerani, tiyeni timuyimbire Yehova mwachimwemwe,

tiyeni tifuwule kwa Thanthwe la chipulumutso chathu

2Tiyeni tibwere pamaso pake ndi chiyamiko

ndipo mupembedzeni Iyeyo ndi zida zoyimbira ndi nyimbo.

3Pakuti Yehova ndi Mulungu wamkulu,

mfumu yayikulu pamwamba pa milungu yonse.

4Mʼmanja mwake muli maziko ozama a dziko lapansi,

ndipo msonga za mapiri ndi zake.

5Nyanja ndi yake, pakuti anayilenga ndi Iye,

ndipo manja ake anawumba mtunda wowuma.

6Bwerani, tiyeni tiwerame pomulambira,

tiyeni tigwade pamaso pa Yehova Mlengi wathu;

7pakuti Iye ndiye Mulungu wathu

ndipo ife ndife anthu a pabusa pake,

ndi nkhosa za mʼdzanja lake.

Lero ngati inu mumva mawu ake,

8musawumitse mitima yanu monga momwe munachitira pa Meriba,

monga munachitira tsiku lija pa Masa mʼchipululu.

9Kumene makolo anu anandiyesa ndi kundiputa,

ngakhale anaona zimene Ine ndinazichita.

10Kwa zaka makumi anayi ndinali wokwiya ndi mʼbado umenewo;

ndipo ndinati, “Iwo ndi anthu amene mitima yawo imasochera

ndipo sanadziwe njira zanga.”

11Choncho ndili chikwiyire, ndinalumbira kuti,

“Iwowa sadzalowa ku malo anga a mpumulo.”