Masalimo 94 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 94:1-23

Salimo 94

1Inu Yehova, ndinu Mulungu wobwezera chilango,

Inu Mulungu amene mumabwezera chilango, wonetsani kuwala kwanu.

2Nyamukani, Inu woweruza wa dziko lapansi;

bwezerani kwa odzikuza zowayenera.

3Kodi mpaka liti anthu oyipa Inu Yehova,

mpaka liti anthu oyipa adzalumpha ndi chimwemwe?

4Amakhuthula mawu onyada;

onse ochita zoyipa ndi odzaza ndi kudzikuza.

5Amaphwanya anthu anu, Inu Yehova;

amapondereza cholowa chanu.

6Amaphanso amayi a masiye ndi alendo okhala nawo mʼdziko;

amapha ana amasiye.

7Iwo amati, “Yehova sakuona;

Mulungu wa Yakobo salabadirako.”

8Samalani, inu anthu opanda nzeru pakati pa anthu;

zitsiru inu, kodi mudzakhala liti anzeru?

9Kodi Iye amene anapanga khutu sangathe kumva?

Kodi Iye amene anapanga diso sangathe kuona?

10Kodi Iye amene amalangiza mitundu ya anthu sangathenso kulanga?

Kodi Iye amene amaphunzitsa munthu angasowe nzeru?

11Yehova amadziwa maganizo a munthu;

Iye amadziwa kuti maganizowo ndi achabechabe.

12Wodala munthu amene Inu Yehova mumamulangiza,

munthu amene mumamuphunzitsa kuchokera mulamulo lanu;

13mumamupumitsa pa nthawi ya mavuto,

mpaka woyipa atakumbiridwa dzenje.

14Pakuti Yehova sadzawakana anthu ake;

Iye sadzasiya cholowa chake.

15Chiweruzo chidzakhazikikanso pa chilungamo,

ndipo onse olungama mtima adzachitsata.

16Ndani adzadzuka chifukwa cha ine kulimbana ndi anthu oyipa?

Ndani adzayimirira mʼmalo mwanga kulimbana ndi anthu ochita zoyipa?

17Yehova akanapanda kundithandiza,

bwenzi nditakakhala msanga ku malo achete a imfa.

18Ndikanena kuti, “Phazi langa likuterereka,”

chikondi chanu, Inu Yehova, chimandichirikiza.

19Pamene nkhawa inakula mʼkati mwanga,

chitonthozo chanu chinabweretsa chimwemwe mʼmoyo mwanga.

20Kodi mpando waufumu woyipa ungathe kugwirizana nanu

umene umabweretsa masautso chifukwa cha malamulo ake?

21Iwo amasonkhana pamodzi kulimbana ndi wolungama

ndi kugamula kuti wosalakwa aphedwe.

22Koma Yehova wakhala linga langa,

ndipo Mulungu ndiye thanthwe limene ndimathawirako.

23Iye adzawabwezera chifukwa cha machimo awo

ndi kuwawononga chifukwa cha kuyipa kwawo;

Yehova Mulungu wathu adzawawononga.

New Serbian Translation

Псалми 94:1-23

Псалам 94

1О, Боже освете!

Севни, Господе, Боже осветниче!

2Устани, судијо земље,

па узврати бахатима истом мером.

3Докле ће зликовци, о, Господе,

докле ће зликовци да ликују?

4Брбљивци су, бахати хвалисавци

сви ти што опако раде.

5Они сатиру твој народ, Господе,

и наследство твоје тлаче.

6Убијају удовицу, дошљака

и сирочад кољу.

7И још кажу: „Господ не види,

не опажа Бог Јаковљев!“

8Размислите, ви свирепи људи! Будале!

Кад ћете се опаметити?

9Не чује ли онај што је творац уха?

Не види ли онај што је творац ока?

10Зар народе он да не кори?

Зар да не покара онај који људе знању учи?

11Господ зна да су мисли човекове безвредне.

12Благо ономе кога ти учиш, Господе,

кога поучаваш о Закону своме;

13да буде спокојан у данима патње,

док се за зликовца јама не ископа.

14Јер Господ не оставља свој народ

и наследства свога он се не одриче.

15Јер праведност се суду враћа

и следе је сва срца честита.

16Ко ће мене да заступа против зликоваца?

Ко ће против злочинаца уз мене да стане?

17Да ми Господ није био помоћ,

убрзо би душа моја у гробу ћутала.

18Када кажем – „Моја нога клеца!“ –

нек ме твоја милост окрепи, Господе!

19Када су у мени самом многобројне бриге,

утехе ми твоје разгаљују душу.

20Зар окрутни владари да ти буду савезници,

и они који крше заповести?

21Уроту праве против душе праведника,

крв невиних осуде ко криву.

22Господ ми је заклон на висини!

Мој је Бог стена уточишта!

23Он ће њима да узврати за злобу њихову,

збрисаће их због зала њихових;

збрисаће их, Господ, Бог наш.