Masalimo 89 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 89:1-52

Salimo 89

Ndakatulo ya Etani, wa banja la Ezara.

1Ndidzayimba za chikondi chachikulu cha Yehova kwamuyaya;

ndi pakamwa panga ndidzachititsa kuti kukhulupirika kwanu kudziwike ku mibado yonse.

2Ndidzalalikira kuti chikondi chanu chidzakhazikika mpaka muyaya,

kuti Inu munakhazikitsa kukhulupirika kwanu kumwamba kwenikweniko.

3Inu munati, “Ndachita pangano ndi wosankhidwa wanga,

ndalumbira kwa Davide mtumiki wanga kuti,

4‘Ndidzakhazikitsa zidzukulu zako mpaka muyaya.

Ndidzachititsa kuti mpando wako waufumu ukhazikike ku mibado yonse,’ ”

Sela.

5Mayiko akumwamba amatamanda zozizwitsa zanu Yehova,

kukhulupirika kwanunso, mu msonkhano wa oyera mtima anu.

6Pakuti ndani mu mlengalenga angalingane ndi Yehova?

Ndani wofanana ndi Yehova pakati pa zolengedwa zakumwamba?

7Mu msonkhano wa oyera mtima Mulungu amaopedwa kwambiri;

Iye ndiye wochititsa mantha kupambana onse amene amuzungulira.

8Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, ndani wofanana nanu?

Yehova ndinu wamphamvu ndipo kukhulupirika kwanu kwakuzungulirani.

9Mumalamula nyanja ya mafunde awukali;

pamene mafunde ake awundana Inu mumawakhalitsa bata.

10Munaphwanya Rahabe monga munthu wophedwa;

ndi dzanja lanu lamphamvu munabalalitsa adani anu.

11Mayiko akumwamba ndi anu ndiponso dziko lapansi ndi lanu;

munapanga dziko lonse ndi zonse zili mʼmenemo.

12Munalenga Kumpoto ndi Kummwera;

Tabori ndi Herimoni akuyimba ndi chimwemwe pa dzina lanu.

13Mkono wanu ndi wamphamvu;

dzanja lanu ndi lamphamvu, dzanja lanu lamanja ndi lopambana.

14Chilungamo ndi chiweruzo cholungama ndiye maziko a mpando wanu waufumu;

chikondi ndi kukhulupirika zimayenda patsogolo panu.

15Ndi odala amene aphunzira kuyamika Inu,

amene amayenda mʼkuwunika kwa nkhope yanu Yehova.

16Amakondwera mʼdzina lanu tsiku lonse lathunthu;

amasangalala koposa mʼchilungamo chanu.

17Pakuti Inu ndiye ulemerero wawo ndi mphamvu yawo

ndipo mwa kukoma mtima kwanu Inu mumakweza nyanga yathu.

18Ndithudi, chishango chathu ndi cha Yehova,

Mfumu yathu kwa Woyerayo wa Israeli.

19Kale munayankhula mʼmasomphenya,

kwa anthu anu okhulupirika munati,

“Ndapatsa mphamvu wankhondo;

ndakweza mnyamata wochokera pakati pa anthu.

20Ndamupeza mtumiki wanga Davide;

ndamudzoza ndi mafuta opatulika.

21Dzanja langa lidzamuchirikiza;

zoonadi, mkono wanga udzamupatsa mphamvu.

22Adani sadzamulamula kuti apereke msonkho;

anthu oyipa sadzamusautsa.

23Ndidzaphwanya adani ake pamaso pake

ndi kukantha otsutsana naye.

24Chikondi changa chokhulupirika chidzakhala naye,

ndipo kudzera mʼdzina langa nyanga yake idzakwezedwa.

25Ndidzayika dzanja lake pa nyanja,

dzanja lake lamanja pa mitsinje.

26Iyeyo adzafuwula kwa Ine kuti, ‘Ndinu Atate anga,

Mulungu wanga, Thanthwe ndi Chipulumutso changa.’

27Ndidzamuyika kuti akhale mwana wanga woyamba kubadwa;

wokwezedwa kwambiri pakati pa mafumu a dziko lapansi.

28Ndidzamusungira chifundo changa kwamuyaya,

ndipo pangano langa ndi iye silidzatha.

29Ine ndidzakhazikitsa zidzukulu zake mpaka muyaya,

mpando wake waufumu ngati masiku a miyamba.

30“Ngati ana ake adzataya lamulo langa

ndi kusatsatira malangizo anga,

31ngati adzaswa malamulo anga

ndi kulephera kusunga ziphunzitso zanga,

32Ine ndidzalanga tchimo lawo ndi ndodo,

mphulupulu zawo powakwapula.

33Koma sindidzachotsa chikondi changa pa iye,

kapena kukhala wosakhulupirika kwa iyeyo.

34Sindidzaswa pangano langa

kapena kusintha zimene milomo yanga yayankhula.

35Ndinalumbira kamodzi mwa kuyera kwanga

ndipo sindidzanama kwa Davide,

36kuti zidzukulu zake zidzakhale kwamuyaya

ndipo mpando wake waufumu udzakhazikika pamaso panga ngati dzuwa;

37udzakhazikika kwamuyaya monga mwezi,

mboni yokhulupirika mʼmitambo.

Sela

38“Koma tsopano Inu mwamukana, mwamutaya,

mwamukwiyira kwambiri wodzozedwa wanu.

39Mwakana pangano ndi mtumiki wanu

ndipo mwadetsa mʼfumbi chipewa chake chaufumu.

40Inu mwagumula makoma ake onse

ndipo mwasandutsa bwinja malinga ake.

41Onse amene amadutsa amalanda zinthu zake;

iye wakhala chotonzedwa cha anansi ake.

42Mwakweza dzanja lamanja la adani ake;

mwachititsa kuti adani ake akondwere.

43Mwabunthitsa lupanga lake,

simunamuthandize pa nkhondo.

44Inu mwathetsa kukongola kwa ulemerero wake

ndipo mwagwetsa pansi mpando wake waufumu.

45Mwachepetsa masiku a unyamata wake;

mwamuphimba ndi chofunda chochititsa manyazi.

Sela

46“Mpaka liti Yehova? Kodi mudzadzibisa mpaka kalekale?

Mpaka liti ukali wanu udzayaka ngati moto?

47Kumbukirani kuti masiku a moyo wanga ndi ochepa

pakuti munalenga kwachabe anthu onse!

48Kodi ndi munthu uti angakhale ndi moyo ndi kusaona imfa?

Kapena kudzipulumutsa yekha ku mphamvu ya manda?

Sela

49Inu Ambuye kodi chili kuti chikondi chanu chachikulu choyamba chija,

chimene mwa kukhulupirika kwanu munalumbira kwa Davide?

50Kumbukirani, Ambuye momwe mtumiki wanu wanyozedwera,

momwe ndakhalira ndi kusunga mu mtima mwanga mawu a pangano a anthu a mitundu yonse,

51mawu achipongwe amene adani anu akhala akunyoza, Inu Yehova,

ndi mawu amene akhala akunyoza mayendedwe onse a wodzozedwa wanu.

52“Matamando akhale kwa Yehova mpaka muyaya!”

Ameni ndi Ameni.

New Russian Translation

Псалтирь 89:1-17

Книга 4

Псалом 89

1Молитва Моисея, человека Божьего.

2Владыка, Ты – наше прибежище

из поколения в поколение.

3Прежде чем родились горы

и Ты образовал землю и вселенную,

от века и до века Ты – Бог.

4Ты возвращаешь человека в тление

и говоришь: «Вернитесь, сыны человеческие».

5Тысяча лет в глазах Твоих,

как день вчерашний, что минул, как стража в ночи.

6Как наводнением уносишь людей;

они проходят, как сон.

Они – как трава, что утром взошла:

утром она цветет и зеленеет,

а вечером вянет и засыхает.

7Мы исчезаем от Твоего гнева,

мы в смятении от Твоей ярости.

8Ты поставил наши беззакония перед Собой

и наши тайные грехи – перед светом Своего лица.

9Наши дни проходят в Твоем гневе;

мы завершаем свои годы со стоном.

10Наших дней – лет семьдесят,

а для более сильных – восемьдесят,

и большая часть их – беда и несчастье;

они проходят быстро, и мы улетаем.

11Кто познал силу Твоего гнева?

Ярость Твоя столь же велика,

сколь велик страх перед Тобой.

12Научи нас вести счет нашим дням,

чтобы мы обрели сердце мудрое.

13Возвратись, Господи! Как долго это будет длиться?

Сжалься над Своими рабами!

14Насыщай нас по утрам милостью Своей,

чтобы мы радовались и веселились все наши дни.

15Возвесели нас за дни, когда Ты наказывал нас,

и за годы, в которые мы испытывали бедствие89:15 Или: зло..

16Да откроется взору рабов Твоих дело Твое,

и слава Твоя – их детям.

17И да пребудет на нас благоволение Владыки, нашего Бога.

Укрепи дело наших рук для нас,

укрепи дело наших рук.