Masalimo 88 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 88:1-18

Salimo 88

Salimo la ana a Kora. Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a nyimbo yoti: “Pa Matenda ndi pa Mazunzo.” Ndakatulo ya Hemani, wa banja la Ezara.

1Inu Yehova, Mulungu amene mumandipulumutsa,

usana ndi usiku ndimalira pamaso panu.

2Pemphero langa lifike pamaso panu;

tcherani khutu lanu kuti mumve kulira kwanga.

3Pakuti ndili ndi mavuto ambiri

ndipo moyo wanga ukuyandikira ku manda.

4Ndikuwerengedwa pamodzi ndi iwo amene akutsikira ku dzenje;

ndine munthu wopanda mphamvu.

5Ndayikidwa pambali pamodzi ndi anthu akufa,

monga ophedwa amene agona mʼmanda,

amene Inu simuwakumbukiranso,

amene achotsedwa pa chisamaliro chanu.

6Mwandiyika pansi pa dzenje penipeni,

mʼmalo akuya a mdima waukulu.

7Ukali wanu ukundipsinja kwambiri,

mwandiopseza kwambiri ndi mafunde anu onse.

Sela

8Mwandichotsa pakati pa abwenzi anga enieni

ndipo mwachititsa kuti ndikhale chonyansa kwa iwo.

Ndatsekerezedwa ndipo sindingathe kuthawa;

9maso anga ada ndi chisoni.

Ndimayitana Inu Yehova tsiku lililonse;

ndimakweza manja anga kwa Inu.

10Kodi mumaonetsa zozizwitsa zanu kwa anthu akufa?

Kodi iwo amene afa amaukanso ndi kutamanda Inu?

Sela

11Kodi chikondi chanu chimalalikidwa mʼmanda,

za kukhulupirika kwanu ku malo a chiwonongeko?

12Kodi zozizwitsa zanu zimadziwika ku malo a mdima,

kapena ntchito zanu zolungama ku dziko la anthu oyiwalika?

13Inu Yehova, Ine ndimalirira thandizo;

mmawa mapemphero anga amafika pamaso panu.

14Inu Yehova nʼchifukwa chiyani mukundikana

ndi kundibisira nkhope yanu?

15Kuyambira ubwana wanga ndakhala ndikuzunzika pafupi kufa;

ndakhala ndikuchita mantha ndipo ndine wothedwa nzeru.

16Ukali wanu wandimiza;

zoopsa zanu zandiwononga.

17Tsiku lonse zimandizungulira ngati chigumula;

zandimiza kwathunthu.

18Inu mwatenga anzanga ndi okondedwa anga kuwachotsa pamaso panga;

mdima ndiye bwenzi langa lenileni.

New Serbian Translation

Псалми 88:1-18

Псалам 88

Песма. Псалам. Потомака Корејевих. Хоровођи. Жалосно. Пева се наизменично. Поучна песма Емана Езраита.

1О, Господе, Боже мог спасења,

и дању и ноћу ја пред тобом вапим!

2Нек пред тебе дође молитва моја,

моме преклињању ти ухо приклони!

3Душа ми је препуна очаја,

Свету мртвих живот ми све ближи.

4У друштву сам оних што иду у раку,

ја сам као човек који снаге нема;

5положен сам међу мртве,

попут мртвих што леже у гробу,

као они које више не спомињеш

и што су далеко од твоје помоћи.

6Ти си ме положио у најдубљу раку,

у тамне дубине.

7Срџба твоја на мене је легла

и плаве ме сви таласи твоји. Села

8Од мене си одвојио пријатеље моје,

гадним си ме њима учинио;

сада сам спутан, напоље не могу!

9Очи су ми усахле од беде.

Призивам те сваког дана,

о, Господе, теби ширим руке своје!

10Зар ћеш чуда за мртве да чиниш?

Хоће ли покојни устати да те славе? Села

11Да ли се у гробу твоја милост разглашава,

и верност твоја у трулежу мртвих?

12Па зар се у тами зна за чуда твоја,

за праведност твоју у земљи заборава?

13А ја тебе, о, Господе, призивам у помоћ;

молитва се моја јутром подиже до тебе.

14Господе, зашто ме одбацујеш?

Зашто своје лице од мене сакриваш?

15Ојађен сам, од младости близу смрти;

очајан сам, натоварен ужасима твојим.

16Срџба твоја ме је прегазила,

страхоте ме твоје уништиле.

17Окружише ме попут воде поваздан,

наваљују једнодушно на ме.

18Вољене и блиске од мене си уклонио

и ја сада другујем са тамом.