Masalimo 81 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 81:1-16

Salimo 81

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a gititi. Salimo la Asafu.

1Imbani mwachimwemwe kwa Mulungu mphamvu yathu;

Fuwulani mokweza kwa Mulungu wa Yakobo!

2Yambani nyimbo, imbani tambolini

imbani pangwe wolira bwino ndi zeze.

3Imbani lipenga la nyanga ya nkhosa yayimuna pa mwezi watsopano,

ndi pamene mwezi waoneka wonse, pa tsiku la phwando;

4ili ndi lamulo kwa Israeli,

langizo la Mulungu wa Yakobo.

5Iye anapereka lamulolo kwa zidzukulu za Yosefe

pamene anatuluka kulimbana ndi Igupto,

kumene tinamva chiyankhulo chimene sitinachidziwe.

6Iye akunena kuti, “Ine ndinachotsa zolemetsa pa mapewa awo;

Manja awo anamasulidwa mʼdengu.

7Pa mavuto anu munayitana ndipo ndinakulanditsani,

ndinakuyankhani kuchokera mʼmitambo ya mabingu;

ndinakuyesani pa madzi a ku Meriba.

Sela

8“Imvani anthu anga, ndipo ndidzakuchenjezani

ngati mungathe kumvetsera, Inu Israeli!

9Musadzakhale ndi mulungu wachilendo pakati panu;

musadzagwadire mulungu wina.

10Ine ndine Yehova Mulungu wanu,

amene ndinakutulutsani mʼdziko la Igupto.

Yasamani kukamwa kwanu ndipo ndidzakudyetsani.

11“Koma anthu anga sanandimvere;

Israeli sanandigonjere.

12Kotero ndinawasiya ndi mitima yawo yosamverayo

kuti atsate zimene ankafuna.

13“Anthu anga akanangondimvera,

Israeli akanatsatira njira zanga,

14nʼkanafulumira motani kuti ndigonjetse adani awo

ndi kutembenuza mkono wanga kulimbana ndi amaliwongo!

15Iwo amene amadana ndi Yehova akanakhwinyata pamaso pake,

ndipo chilango chawo chinakakhala mpaka kalekale.

16Koma inu mukanadyetsedwa tirigu wabwino kwambiri;

ndikanakukhutitsani ndi uchi wochokera pa thanthwe.”

New Russian Translation

Псалтирь 81:1-8

Псалом 81

1Псалом Асафа.

Бог возглавляет великое собрание81:1 Великое собрание – или: «собрание Бога».,

среди богов81:1 Или: «судей». Это слово на языке оригинала может означать «боги», «ангелы» и «судьи». Также в ст. 6. произносит суд:

2«Как долго еще вы будете судить несправедливо

и оказывать предпочтение нечестивым? Пауза

3Защищайте дело слабого и сироты,

угнетенному и бедному явите справедливость.

4Избавляйте слабого и нищего,

спасайте их от нечестивых.

5Их знание – ничто, их понимание бессмысленно.

Они ходят во тьме.

Содрогаются все основания земли.

6Я сказал: „Вы – боги,

все вы – сыны Всевышнего“

7но вы умрете, как все люди,

и вы падете, как любой из властителей».

8Восстань, Боже, и суди землю,

потому что Ты наследуешь все народы!