Masalimo 80 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 80:1-19

Salimo 80

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Kakombo wa Pangano.” Salimo la Asafu.

1Tcherani khutu Inu mʼbusa wa Israeli,

Inu amene mumatsogolera Yosefe monga nkhosa;

Inu amene mumakhala pa mpando waufumu pakati pa akerubi, walani

2kwa Efereimu, Benjamini ndi Manase.

Utsani mphamvu yanu;

bwerani ndi kutipulumutsa.

3Tibwezereni mwakale Inu Mulungu;

nkhope yanu itiwalire

kuti tipulumutsidwe.

4Inu Mulungu Wamphamvuzonse,

mpaka liti mkwiyo wanu udzanyeka

kutsutsana ndi mapemphero a anthu anu?

5Mwawadyetsa buledi wa misozi;

mwachitisa iwo kumwa misozi yodzaza mbale.

6Mwachititsa kuti tikhale gwero la mikangano pakati pa anansi athu,

ndipo adani athu akutinyoza.

7Tibwezereni mwakale Inu Mulungu Wamphamvuzonse,

nkhope yanu itiwalire

kuti tipulumutsidwe.

8Munatulutsa mpesa kuchoka ku Igupto;

munathamangitsa anthu a mitundu ina ndi kuwudzala mpesawo.

9Munawulimira munda wamphesawo,

ndipo unamera ndi kudzaza dziko.

10Mapiri anaphimbidwa ndi mthunzi wake,

mikungudza yamphamvu ndi nthambi zake.

11Unatambalitsa nthambi zake mpaka ku nyanja,

mphukira zake mpaka ku mtsinje.

12Chifukwa chiyani mwagwetsa makoma ake

kuti onse amene akudutsa athyole mphesa zake?

13Nguluwe zochokera mʼnkhalango zikuwononga

ndipo zirombo za mthengo zimawudya.

14Bweraninso kwa ife Inu Mulungu Wamphamvuzonse!

Yangʼanani pansi muli kumwambako ndipo muone!

Uyangʼanireni mpesa umenewu,

15muzu umene dzanja lanu lamanja ladzala,

mwana amene inu munamukuza nokha.

16Mpesa wanu wadulidwa ndi kutenthedwa ndi moto;

pakudzudzula kwanu anthu anu awonongeka.

17Dzanja lanu likhale pa munthu amene ali ku dzanja lanu lamanja,

mwana wa munthu amene mwalera nokha.

18Ndipo ife sitidzatembenukira kumbali kuchoka kwa Inu;

titsitsimutseni ndipo tidzayitana pa dzina lanu.

19Tibwezereni mwakale Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse

nkhope yanu itiwalire

kuti tipulumutsidwe.