Salimo 8
Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa gititi. Salimo la Davide.
1Inu Yehova Ambuye athu,
dzina lanu ndi la lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
Inu mwakhazikitsa ulemerero wanu
mʼmayiko onse akumwamba.
2Kuchokera mʼkamwa mwa ana ndi makanda,
Inu mwakhazikitsa mphamvu
chifukwa cha adani anu,
kukhazikitsa bata adani ndi anthu obwezera zoyipa.
3Pamene ndilingalira za mayiko anu akumwamba,
ntchito ya zala zanu,
mwezi ndi nyenyezi,
zimene mwaziyika pa malo ake,
4munthu ndani kuti Inu mumamukumbukira,
ndi mwana wa munthu kuti inu mumacheza naye?
5Inu munamupanga kukhala wocheperapo kusiyana ndi zolengedwa zakumwamba
ndipo mwamuveka ulemerero ndi ulemu.
6Inu munamuyika wolamulira ntchito ya manja anu;
munayika zinthu zonse pansi pa mapazi ake;
7nkhosa, mbuzi ndi ngʼombe pamodzi
ndi nyama zakuthengo,
8mbalame zamlengalenga
ndi nsomba zamʼnyanja
zonse zimene zimayenda pansi pa nyanja.
9Inu Yehova, Ambuye athu,
dzina lanu ndi lamphamvudi pa dziko lonse lapansi!
1Een psalm van David voor de koordirigent.
2Here, onze God,
de majesteit en glorie van uw naam
vullen de gehele aarde
en de hemelen vloeien ervan over.
3U hebt de kleine kinderen geleerd
U volmaakt te prijzen.
Hun voorbeeld zal uw vijanden
en hen die op wraak zinnen,
beschaamd doen staan
en tot zwijgen brengen!
4Als ik ʼs nachts omhoog kijk naar de hemel
en het werk van uw handen zie,
de maan en de sterren,
die U hun plaats gegeven hebt,
5wat is dan de mens,
dat U zoveel om hem geeft?
Wat is een mensenkind
dat U Zich om hem bekommert?
6En U hebt hem een plaats vlak onder Uzelf gegeven,
U hebt hem gekroond met heerlijkheid en eer.
7U hebt hem zelfs het beheer gegeven
over alles wat U hebt gemaakt,
alles staat onder zijn gezag:
8alle schapen en runderen
en andere dieren in het veld,
9de vogels in de lucht
en de vissen en andere wezens in de zee.
10O Here, onze God,
de majesteit en glorie van uw naam
vullen de hele aarde!