Masalimo 76 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 76:1-12

Salimo 76

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Pa zoyimbira za zingwe. Salimo la Asafu.

1Mulungu amadziwika mu Yuda;

dzina lake ndi lotchuka mu Israeli.

2Tenti yake ili mu Salemu,

malo ake okhalamo mu Ziyoni.

3Kumeneko Iye anathyola mivi yowuluka,

zishango ndi malupanga, zida zankhondo.

Sela

4Wolemekezeka ndinu,

wamphamvu kuposa mapiri amene ali ndi nyama zambiri.

5Anthu owuma mtima amagona atalandidwa chuma,

Iwowo amagona tulo tawo totsiriza;

palibe mmodzi wamphamvu

amene angatukule manja ake.

6Pa kudzudzula kwanu, Inu Mulungu wa Yakobo,

kavalo pamodzi ndi galeta zimakhala chete zitagona pansi.

7Inu nokha ndiye muyenera kuopedwa.

Angathe kuyima pamaso panu ndani mukakwiya?

8Kuchokera kumwamba Inu munalengeza chiweruzo,

ndipo dziko linaopa ndi kukhala chete,

9pamene Inu Mulungu munadzuka kuti muweruze,

kupulumutsa onse osautsidwa mʼdziko.

Sela

10Zoonadi, ukali wanu pa anthu umakubweretserani matamando

ndipo opulumuka ku ukali wanu mumawasunga pafupi nanu.

11Chitani malumbiro kwa Yehova Mulungu wanu ndipo muwakwaniritse;

anthu onse omuzungulira abweretse mphatso

kwa Iye amene ayenera kuopedwa.

12Iye amaswa mzimu wa olamulira;

amaopedwa ndi mafumu a dziko lapansi.