Masalimo 72 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 72:1-20

Salimo 72

Salimo la Solomoni.

1Patsani mwana wa mfumu nzeru zanu zoweruzira mwa chilungamo,

Inu Mulungu mupatseni mwana wa mfumu chilungamo chanu.

2Iye adzaweruza anthu anu mwachilungamo,

anthu anu ozunzika mosakondera.

3Mapiri adzabweretsa chuma kwa anthu anu,

timapiri tidzabweretsa zipatso zachilungamo.

4Iye adzateteza ozunzika pakati pa anthu

ndi kupulumutsa ana a anthu osowa;

adzaphwanya ozunza anzawo.

5Adzakhala ndi moyo pa mibado yonse,

nthawi zonse pamene dzuwa ndi mwezi zikuwala.

6Iye adzakhala kugwa kwa mvula pa minda yolimidwa

ngati mivumbi yothirira dziko lapansi.

7Mʼmasiku a munthu wolungama adzakhazikika;

chuma chidzachuluka mpaka mwezi utaleka kuwala.

8Iye adzalamulira kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja ina

ndiponso kuchokera ku mtsinje mpaka ku malekezero a dziko lapansi.

9Mafuko a mʼchipululu adzawerama pamaso pake

ndipo adani ake adzanyambita fumbi.

10Mafumu a ku Tarisisi ndi a ku zilumba zakutali

adzabweretsa mitulo kwa iye,

mafumu a ku Seba ndi Seba

adzapereka mphatso kwa iyeyo.

11Mafumu onse adzamuweramira

ndipo mitundu yonse idzamutumikira.

12Pakuti iye adzawombola wosowa amene akulira,

wozunzika amene alibe wina womuthandiza.

13Iye adzachitira chifundo anthu ofowoka ndi anthu osowa

ndi kupulumutsa osowa ku imfa.

14Iye adzalanditsa iwo ku mazunzo ndi chiwawa

pakuti magazi awo ndi amtengo wapatali pamaso pake.

15Iye akhale ndi moyo wautali;

golide ochokera ku Seba apatsidwe kwa iye.

Anthu amupempherere nthawi zonse

ndi kumudalitsa tsiku lonse.

16Mulole kuti tirigu achuluke mʼdziko lonse;

pamwamba pa mapiri pakhale tirigu.

Zipatso zake zichuluke ngati za ku Lebanoni;

zichuluke ngati udzu wakuthengo

17Dzina lake likhazikike kwamuyaya,

lipitirire kukhala monga momwe limakhalira dzuwa.

Mitundu yonse idzadalitsika kudzera mwa iye

ndipo iwo adzamutcha iye wodala.

18Matamando akhale kwa Yehova Mulungu, Mulungu wa Israeli

amene Iye yekha amachita ntchito zodabwitsa.

19Matamando akhale ku dzina lake laulemerero kwamuyaya

dziko lonse lapansi lidzaze ndi ulemerero wake.

Ameni ndi Ameni.

20Uku ndiko kumaliza kwa mapemphero a Davide mwana wa Yese.