Masalimo 71 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 71:1-24

Salimo 71

1Mwa Inu Yehova ine ndathawiramo;

musalole kuti ndichititsidwe manyazi.

2Mundilanditse ndi kundipulumutsa mwa chilungamo chanu,

mutchere khutu lanu ndi kundipulumutsa.

3Mukhale thanthwe langa lothawirapo,

kumene ine nditha kupita nthawi zonse;

lamulani kuti ndipulumuke,

pakuti Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa.

4Landitseni Inu Mulungu wanga, kuchoka mʼdzanja la oyipa,

kuchoka mʼdzanja la oyipa ndi anthu ankhanza.

5Pakuti Inu mwakhala chiyembekezo changa, Inu Ambuye Wamphamvuzonse,

chilimbikitso changa kuyambira ndili mwana.

6Kuyambira pamene ndinabadwa, ndakhala ndikudalira Inu;

Inu munanditulutsa mʼmimba mwa amayi anga,

ndipo ndidzakupembedzani nthawi zonse.

7Ine ndakhala chinthu chodabwitsa kwa anthu ambiri

koma Inu ndinu wonditchinjiriza wamphamvu.

8Pakamwa panga padzaza ndi matamando anu,

kulengeza ulemerero wanu tsiku lonse.

9Musanditaye pamene ndakalamba;

musandisiye pamene mphamvu zanga zatha.

10Pakuti adani anga ayankhula motsutsana nane;

iwo amene amadikira kuti andiphe amapangana pamodzi.

11Iwo amati, “Mulungu wamusiya;

mutsatireni ndi kumugwira,

pakuti palibe amene adzamupulumutse.”

12Musakhale kutali ndi ine Inu Mulungu,

bwerani msanga, Inu Mulungu wanga; thandizeni.

13Ondineneza anga awonongeke mwa manyazi,

iwo amene akufuna kundipweteka

avale chitonzo ndi manyazi.

14Koma ine ndidzakhala ndi chiyembekezo mwa Inu nthawi zonse,

ndidzakutamandani mowirikizawirikiza.

15Pakamwa panga padzafotokoza za chilungamo chanu,

za chipulumutso chanu tsiku lonse,

ngakhale sindikudziwa muyeso wake.

16Ndidzabwera ndi kulengeza za machitidwe amphamvu zanu Inu Ambuye Wamphamvuzonse.

Ndidzalengeza chilungamo chanu, chanu chokha.

17Kuyambira ubwana wanga, Inu Mulungu mwakhala mukundiphunzitsa,

ndipo mpaka lero ine ndikulengeza za ntchito zanu zodabwitsa

18Ngakhale pamene ndakalamba ndipo imvi zili mbuu

musanditaye Inu Mulungu,

mpaka nditalengeza mphamvu zanu

kwa mibado yonse yakutsogolo.

19Mphamvu zanu ndi kulungama kwanu zimafika mpaka kumwambamwamba.

Ndani wofanana nanu Inu Mulungu,

amene mwachita zazikulu?

20Ngakhale mwandionetsa mavuto

ambiri owawa,

mudzabwezeretsanso moyo wanga;

kuchokera kunsi kwa dziko lapansi,

mudzandiukitsanso.

21Inu mudzachulukitsa ulemu wanga

ndi kunditonthozanso.

22Ndidzakutamandani ndi zeze

chifukwa cha kukhulupirika kwanu Mulungu,

ndidzayimba matamando kwa Inu ndi pangwe,

Inu Woyera wa Israeli.

23Milomo yanga idzafuwula ndi chimwemwe

pamene ndidzayimba matamando kwa Inu

amene mwandiwombola.

24Lilime langa lidzafotokoza za ntchito zanu zachilungamo

tsiku lonse,

pakuti iwo amene amafuna kundipweteka

achititsidwa manyazi ndi kusokonezedwa.