Masalimo 7 – CCL & NSP

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 7:1-17

Salimo 7

Sigioni wa Davide, amene anayimbira Yehova zokhudza Kusi, wa fuko la Benjamini.

1Inu Yehova Mulungu wanga, Ine ndikuthawira kwa Inu;

pulumutseni ndi kundilanditsa kwa onse amene akundithamangitsa,

2mwina angandikadzule ngati mkango,

ndi kundingʼamba popanda wondipulumutsa.

3Inu Yehova Mulungu wanga,

ngati ndachita izi ndipo ndapezeka wolakwa,

4ngati ndachita zoyipa kwa iye amene ndili naye pa mtendere,

kapena popanda chifukwa ndalanda mdani wanga,

5pamenepo lolani adani anga andithamangitse ndi kundipitirira,

lolani kuti moyo wanga aupondereze pansi

ndipo mundigoneke pa fumbi.

Sela

6Nyamukani Yehova, mu mkwiyo wanu;

nyamukani kutsutsana ndi mkwiyo wa adani anga.

Dzukani Mulungu wanga, lamulirani chilungamo chanu.

7Lolani gulu la anthu a mitundu ina lisonkhane mokuzungulirani.

Alamulireni muli kumwambako;

8Yehova aweruzeni anthu a mitundu inayo.

Ndiweruzeni Yehova, monga mwa chilungamo changa,

monga mwa moyo wanga wangwiro, Inu Wammwambamwamba.

9Inu Mulungu wolungama,

amene mumasanthula maganizo ndi mitima,

thetsani chiwawa cha anthu oyipa

ndipo wolungama akhale motetezedwa.

10Chishango changa ndi Mulungu Wammwambamwamba,

amene amapulumutsa olungama mtima.

11Mulungu amaweruza molungama,

Mulungu amene amaonetsa ukali wake tsiku ndi tsiku.

12Ngati munthu satembenuka,

Mulungu adzanola lupanga lake,

Iye adzawerama ndi kukoka uta.

13Mulungu wakonza zida zake zoopsa;

Iye wakonzekera mivi yake yoyaka moto.

14Taonani, munthu woyipa amalingalira zoyipa zokhazokha nthawi zonse.

Zochita zake ndi zosokoneza ndi zovutitsa anthu ena.

15Iye amene akumba dzenje ndi kulizamitsa

amagwera mʼdzenje limene wakumbalo.

16Mavuto amene amayambitsa amamubwerera mwini;

chiwawa chake chimatsikira pa mutu wake womwe.

17Ine ndidzayamika Yehova chifukwa cha chilungamo chake;

ndipo ndidzayimba nyimbo zamatamando pa dzina la Yehova Wammwambamwamba.

New Serbian Translation

Псалми 7:1-17

Псалам 7

Тужбалица Давидова, коју је испевао Господу због речи Хуша, Венијаминовца.

1Господе, Боже мој,

у теби је моје уточиште,

спаси ме, избави,

од свих који ме гоне,

2да ми душу као лав не раздеру,

растргну ме, а спаса ни од кога.

3Господе, Боже мој, ако сам ово учинио,

ако сам руке своје неправдом окаљао,

4ако сам пријатељу злом узвратио,

а противника без разлога пљачкао,

5нека ме непријатељ гони и сустигне,

нека живот мој на земљу згази,

а славу моју у прашину баци. Села

6У свом гневу устани, Господе,

дигни се на бес мојих душмана,

пробуди се, у помоћ ми дођи,

јер ти си свој суд заказао.

7Нека се збор народа скупи око тебе,

па над њима владај са висина.

8Господ суди народима,

суди ми, Господе, по праведности

и непорочности мојој.

9Бог је праведан,

он испитује и срца и нутрину;

нека дође крај злу опаких,

а праведнога ти учврсти.

10Бог је мој штит,

он спасава исправног у срцу.

11Бог је праведни судија,

сваког дана Бог гнев свој излива.

12А за оног ко се не покаје,

он ће свој мач наоштрити,

и лук свој запети, уперити;

13таквом спрема оружје смртно,

стреле своје прави запаљиве.

14Ето, опаки је злом бременит,

зачиње невољу, а рађа превару.

15Копа јаму, издуби је,

и пада у јаму коју је начинио.

16Невоља његова нека му се на главу врати,

насиље његово нека му на теме падне.

17Хвалићу Господа ради његове праведности,

славићу песмом име Господа Свевишњег!