Masalimo 69 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 69:1-36

Salimo 69

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide. Potsata mayimbidwe a “Akakombo.”

1Pulumutseni Inu Mulungu,

pakuti madzi afika mʼkhosi

2Ine ndikumira mʼthope lozama

mʼmene mulibe popondapo.

Ndalowa mʼmadzi ozama;

mafunde andimiza.

3Ndafowoka ndikupempha chithandizo;

kummero kwanga kwawuma gwaa,

mʼmaso mwanga mwada

kuyembekezera Mulungu wanga.

4Iwo amene amadana nane popanda chifukwa

ndi ochuluka kuposa tsitsi la kumutu kwanga;

ambiri ndi adani anga popanda chifukwa,

iwo amene akufunafuna kundiwononga.

Ndikukakamizidwa kubwezera

zomwe sindinabe.

5Mukudziwa uchitsiru wanga, Inu Mulungu,

kulakwa kwanga sikuli kobisika kwa Inu.

6Iwo amene amadalira Inu

asanyozedwe chifukwa cha ine,

Inu Ambuye Wamphamvuzonse.

Iwo amene amafunafuna Inu

asachititsidwe manyazi chifukwa cha ine,

Inu Mulungu wa Israeli.

7Pakuti ndimapirira kunyozedwa chifukwa cha Inu,

ndipo manyazi amaphimba nkhope yanga.

8Ndine mlendo kwa abale anga,

munthu wakudza kwa ana aamuna a amayi anga;

9pakuti changu chochitira nyumba yanu chandiphetsa

ndipo chipongwe cha iwo amene amanyoza Inu chandigwera.

10Pamene ndikulira ndi kusala kudya,

ndiyenera kupirira kunyozedwa;

11pomwe ndavala chiguduli,

anthu amandiseweretsa.

12Iwo amene amakhala pa chipata amandinena,

ndipo ine ndine nyimbo ya zidakwa.

13Koma ndikupempha kwa Inu Ambuye,

pa nthawi yanu yondikomera mtima;

mwa chikondi chanu chachikulu

Inu Mulungu, mundiyankhe pondipulumutsa.

14Mundilanditse kuchoka mʼmatope,

musalole kuti ndimire,

pulumutseni ine kwa iwo

amene amadana nane, kuchoka mʼmadzi ozama.

15Musalole kuti chigumula chindimeze,

kuya kusandimeze

ndipo dzenje lisatseke pakamwa pake kundimiza.

16Ndiyankheni Inu Yehova mwa ubwino wanu wa chikondi chanu;

mwa chifundo chanu chachikulu tembenukirani kwa ine.

17Musabisire nkhope yanu mtumiki wanu,

ndiyankheni msanga, pakuti ndili pa mavuto.

18Bwerani pafupi ndi kundilanditsa;

ndiwomboleni chifukwa cha adani anga.

19Inu mukudziwa momwe ndanyozedwera,

kunyozedwa ndi kuchititsidwa manyazi; adani anga onse ali pamaso panu.

20Mnyozo waswa mtima wanga

ndipo wandisiya wopanda thandizo lililonse;

ndinafunafuna ena woti andichitire chisoni,

koma panalibe ndi mmodzi yemwe woti anditonthoze, sindinapeze ndi mmodzi yemwe.

21Iwo anayika ndulu mʼchakudya changa

ndi kundipatsa vinyo wosasa chifukwa cha ludzu.

22Chakudya chomwe chayikidwa patsogolo pawo chikhale msampha;

chikhale chobwezera chilango ndiponso khwekhwe.

23Maso awo adetsedwe kotero kuti asaonenso

ndipo misana yawo ipindike mpaka kalekale.

24Khuthulirani ukali wanu pa iwo;

mkwiyo wanu woyaka moto uwathe mphamvu.

25Malo awo akhale wopanda anthu

pasapezeke ndi mmodzi yemwe wokhala mʼmatenti awo.

26Pakuti iwo amazunza amene inu munamuvulaza

ndi kuyankhula zowawa kwa amene munawapweteka.

27Awonjezereni kulakwa pa kulakwa kwawo,

musalole kuti akhale ndi gawo pa chipulumutso chanu.

28Iwo afufutidwe mʼbuku la amoyo

ndipo asalembedwe pamodzi ndi olungama.

29Ndikumva zowawa ndi kuzunzika;

lolani chipulumutso chanu, Inu Mulungu, chinditeteze.

30Ine ndidzatamanda dzina la Mulungu mʼnyimbo,

ndidzalemekeza Iye ndi chiyamiko.

31Izi zidzakondweretsa Yehova kupambana ngʼombe,

kupambananso ngʼombe yayimuna, pamodzi ndi nyanga ndi ziboda zake.

32Wosauka adzaona ndipo adzasangalala,

Inu amene mumafunafuna Mulungu, mitima yanu ikhale ndi moyo!

33Yehova amamvera anthu osowa

ndipo sanyoza anthu ake omangidwa.

34Kumwamba ndi dziko lapansi zitamanda Iye,

nyanja ndi zonse zomwe zimayenda mʼmenemo,

35pakuti Mulungu adzapulumutsa Ziyoni

ndi kumanganso mizinda ya Yuda,

anthu adzakhala kumeneko ndipo dzikolo lidzakhala lawo;

36ana atumiki ake adzalitenga kukhala cholowa chawo,

ndipo iwo amene amakonda dzina lake adzakhala kumeneko.