Masalimo 68 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 68:1-35

Salimo 68

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Adzuke Mulungu, adani ake amwazikane;

adani ake athawe pamaso pake.

2Monga momwe mphepo imachotsera utsi; Inu muwawulutsire kutali.

Monga phula limasungunukira pa moto,

oyipa awonongeke pamaso pa Mulungu.

3Koma olungama asangalale

ndi kukondwera pamaso pa Mulungu;

iwo akondwere ndi kusangalala.

4Imbirani Mulungu imbirani dzina lake matamando,

mukwezeni Iye amene amakwera pa mitambo;

dzina lake ndi Yehova ndipo sangalalani pamaso pake.

5Atate wa ana amasiye, mtetezi wa akazi amasiye,

ndiye Mulungu amene amakhala mʼmalo oyera.

6Mulungu amakhazikitsa mtima pansi osungulumwa mʼmabanja,

amatsogolera amʼndende ndi kuyimba;

koma anthu osamvera amakhala ku malo owuma a dziko lapansi.

7Pamene munatuluka kutsogolera anthu anu, Inu Mulungu,

pamene munayenda kudutsa chipululu,

8dziko lapansi linagwedezeka, miyamba inakhuthula pansi mvula,

pamaso pa Mulungu, Mmodzi uja wa ku Sinai.

Pamaso pa Mulungu, Mulungu wa Israeli.

9Munapereka mivumbi yochuluka, Inu Mulungu;

munatsitsimutsa cholowa chanu cholefuka.

10Anthu anu anakhala mʼmenemo

ndipo munapatsa anthu osauka zimene zinkawasowa chifukwa cha ubwino wanu Mulungu.

11Ambuye analengeza mawu,

ndipo gulu linali lalikulu la iwo amene anapita kukawafalitsa;

12“Mafumu ndi ankhondo anathawa mwaliwiro;

mʼmisasa anthu anagawana zolanda pa nkhondo.

13Ngakhale mukugona pakati pa makola a ziweto,

mapiko a nkhunda akutidwa ndi siliva,

nthenga zake ndi golide wonyezimira.”

14Pamene Wamphamvuzonse anabalalitsa mafumu mʼdziko,

zinali ngati matalala akugwa pa Zalimoni.

15Mapiri a Basani ndi mapiri aulemerero;

mapiri a Basani, ndi mapiri a msonga zambiri.

16Muyangʼaniranji mwansanje inu mapiri a msonga zambiri,

pa phiri limene Mulungu analisankha kuti azilamulira,

kumene Yehova mwini adzakhalako kwamuyaya?

17Magaleta a Mulungu ndi osawerengeka,

ndi miyandamiyanda;

Ambuye wabwera kuchokera ku Sinai, walowa mʼmalo ake opatulika.

18Pamene Inu munakwera mmwamba,

munatsogolera a mʼndende ambiri;

munalandira mphatso kuchokera kwa anthu,

ngakhale kuchokera kwa owukira,

kuti Inu Mulungu, mukhale kumeneko.

19Matamando akhale kwa Ambuye, kwa Mulungu Mpulumutsi wathu

amene tsiku ndi tsiku amasenza zolemetsa zathu.

20Mulungu wathu ndi Mulungu amene amapulumutsa;

Ambuye Wamphamvuzonse ndiye amene amatipulumutsa ku imfa.

21Ndithu Mulungu adzaphwanya mitu ya adani ake,

zipewa za ubweya za iwo amene amapitiriza kuchita machimo awo.

22Ambuye akunena kuti, “Ndidzawabweretsa kuchokera ku Basani;

ndidzawabweretsa kuchokera ku nyanja zozama.

23Kuti muviyike mapazi anu mʼmagazi a adani anu,

pamene malilime a agalu anu akudyapo gawo lawo.”

24Mayendedwe aulemu a anthu anu aonekera poyera, Inu Mulungu;

mayendedwe olemekeza Mulungu wanga ndi Mfumu yanga yokalowa mʼmalo opatulika.

25Patsogolo pali oyimba nyimbo pakamwa, pambuyo pawo oyimba nyimbo ndi zipangizo;

pamodzi ndi iwo pali atsikana akuyimba matambolini.

26Tamandani Mulungu mu msonkhano waukulu;

tamandani Yehova mu msonkhano wa Israeli.

27Pali fuko lalingʼono la Benjamini, kuwatsogolera,

pali gulu lalikulu la ana a mafumu a Yuda,

ndiponso pali ana a mafumu a Zebuloni ndi Nafutali.

28Kungani mphamvu zanu Mulungu;

tionetseni nyonga zanu, Inu Mulungu, monga munachitira poyamba.

29Chifukwa cha Nyumba yanu ku Yerusalemu,

mafumu adzabweretsa kwa Inu mphatso.

30Dzudzulani chirombo pakati pa mabango,

gulu la ngʼombe zazimuna pakati pa ana angʼombe a mitundu ya anthu.

Mochititsidwa manyazi, abweretse mitanda ya siliva.

Balalitsani anthu a mitundu ina amene amasangalatsidwa ndi nkhondo.

31Nthumwi zidzachokera ku Igupto;

Kusi adzadzipereka yekha kwa Mulungu.

32Imbirani Mulungu Inu mafumu a dziko lapansi

imbirani Ambuye matamando.

Sela

33Kwa Iye amene amakwera pa mitambo yakalekale ya mmwamba

amene amabangula ndi mawu amphamvu.

34Lengezani za mphamvu za Mulungu,

amene ulemerero wake uli pa Israeli

amene mphamvu zake zili mʼmitambo.

35Ndinu woopsa, Inu Mulungu mʼmalo anu opatulika;

Mulungu wa Israeli amapereka mphamvu ndi nyonga kwa anthu ake.

Matamando akhale kwa Mulungu!