Masalimo 66 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 66:1-20

Salimo 66

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo.

1Fuwulani kwa Mulungu ndi chimwemwe, dziko lonse lapansi!

2Imbani ulemerero wa dzina lake;

kumutamanda kwake kukhale kwaulemerero.

3Nenani kwa Mulungu, “Ntchito zanu ndi zoopsa ndithu!

Mphamvu yanu ndi yayikulu kwambiri

kotero kuti adani anu amawerama pamaso panu.

4Dziko lonse lapansi limaweramira inu;

limayimba matamando kwa Inu;

limayimba matamando pa dzina lanu.”

Sela.

5Bwerani mudzaone zimene Mulungu wachita,

ntchito zanu ndi zoopsa ndithu pakati pa anthu.

6Iye anasandutsa nyanja kukhala malo owuma,

iwo anawoloka pa madzi ndi mapazi.

Bwerani, tiyeni tikondwere mwa Iye.

7Iye amalamulira ndi mphamvu zake mpaka muyaya,

maso ake amayangʼanira anthu a mitundu ina.

Anthu owukira asadzitukumule.

8Tamandani Mulungu wathu, inu mitundu ya anthu,

mulole kuti mawu a matamando ake amveke;

9Iye watchinjiriza miyoyo yathu

ndi kusunga mapazi athu kuti angaterereke.

10Pakuti Inu Mulungu munatiyesa;

munatiyenga ngati siliva.

11Inu mwatilowetsa mʼndende

ndi kutisenzetsa zolemera pa misana yathu.

12Inu munalola kuti anthu akwere pa mitu yathu;

ife tinadutsa mʼmoto ndi mʼmadzi,

koma Inu munatibweretsa ku malo a zinthu zochuluka.

13Ine ndidzabwera ku Nyumba yanu ndi nsembe zopsereza

ndi kukwaniritsa malumbiro anga.

14Malumbiro amene milomo yanga inalonjeza

ndi pakamwa panga panayankhula pamene ndinali pa mavuto.

15Ndidzapereka nsembe nyama zonenepa kwa Inu

ndi chopereka cha nkhosa zazimuna;

ndidzapereka ngʼombe zamphongo ndi mbuzi.

Sela

16Bwerani ndipo mudzamve inu nonse amene mumaopa Mulungu.

Ndidzakuwuzani zimene Iyeyo wandichitira.

17Ndinafuwula kwa Iye ndi pakamwa panga,

matamando ake anali pa lilime panga.

18Ndikanasekerera tchimo mu mtima mwanga

Ambuye sakanamvera;

19koma ndithu Mulungu wamvetsera

ndipo watchera khutu ku mawu a kupempha kwanga.

20Matamando akhale kwa Mulungu

amene sanakane pemphero langa

kapena kuletsa chikondi chake pa ine!