Masalimo 59 – CCL & CST

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 59:1-17

Salimo 59

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide. Pamene Sauli anatumiza anthu kuti akalondere nyumba ya Davide ndi cholinga choti amuphe.

1Landitseni kwa adani anga, Inu Mulungu;

munditeteze kwa anthu amene auka kutsutsana nane.

2Landitseni kwa anthu ochita zoyipa

ndipo mundipulumutse kwa anthu okhetsa magazi.

3Onani momwe iwo akundibisalira!

Anthu owopsa agwirizana zolimbana nane;

osati chifukwa cha mlandu kapena tchimo langa, Inu Yehova.

4Ine sindinachite cholakwa, koma iwo ndi okonzeka kundithira nkhondo.

Dzukani kuti mundithandize; penyani mavuto anga!

5Inu Yehova Mulungu Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israeli,

dzidzutseni nokha kuti mulange anthu a mitundu ina yonse;

musaonetse chifundo chanu kwa anthu oyipa achinyengowa.

6Iwo amabweranso madzulo

akuchita phokoso ngati agalu

ndi kumangoyendayenda mu mzinda.

7Onani zomwe amalavula mʼkamwa mwawo;

iwo amalavula malupanga kuchokera pa milomo yawo,

ndipo amanena kuti, “Ndani angatimve?”

8Koma Inu Yehova, mumawaseka,

mumayinyoza mitundu yonseyo.

9Inu mphamvu yanga, ine ndiyangʼana kwa inu;

Inu Mulungu, ndinu linga langa. 10Mulungu wanga wachikondi.

Mulungu adzapita patsogolo panga

ndipo adzandilola kunyada pa iwo amene amandinyoza.

11Koma musawaphe, Inu Ambuye chishango chathu,

kuopa kuti anthu anga angayiwale.

Mwa mphamvu zanu,

lolani kuti azingoyendayenda ndipo muwatsitse.

12Chifukwa cha machimo a pakamwa pawo

chifukwa cha mawu a milomo yawo,

iwo akodwe mʼkunyada kwawo.

Chifukwa cha matemberero ndi mabodza amene ayankhula

13muwawononge mu ukali (wanu)

muwawononge mpaka atheretu.

Pamenepo zidzadziwika ku malekezero a dziko lapansi

kuti Mulungu amalamulira Yakobo.

14Iwo amabweranso madzulo,

akuchita phokoso ngati agalu

ndi kumangoyenda mu mzinda.

15Iwo amayendayenda kufuna chakudya

ndipo amawuwa ngati sanakhute.

16Koma ine ndidzayimba za mphamvu yanu,

mmawa ndidzayimba zachikondi chanu;

pakuti ndinu linga langa,

pothawirapo panga mʼnthawi ya mavuto.

17Inu mphamvu yanga, ndiyimba matamando kwa inu;

Inu Mulungu, ndinu linga langa, Mulungu wanga wachikondi.

Nueva Versión Internacional (Castilian)

Salmo 59:1-17

Salmo 59

Al director musical. Sígase la tonada de «No destruyas». Mictam de David, cuando Saúl había ordenado que vigilaran la casa de David con el propósito de matarlo.

1Líbrame de mis enemigos, oh Dios;

protégeme de los que me atacan.

2Líbrame de los malhechores;

sálvame de los asesinos.

3¡Mira cómo me acechan!

Hombres crueles conspiran contra mí

sin que yo, Señor, haya delinquido ni pecado.

4Presurosos se disponen a atacarme

sin que yo haya cometido mal alguno.

¡Levántate y ven en mi ayuda!

¡Mira mi condición!

5Tú, Señor, eres el Dios Todopoderoso,

¡eres el Dios de Israel!

¡Despiértate y castiga a todas las naciones;

no tengas compasión de esos viles traidores! Selah

6Ellos vuelven por la noche,

gruñendo como perros

y acechando alrededor de la ciudad.

7Echan espuma por la boca,

lanzan espadas por sus fauces,

y dicen: «¿Quién va a oírnos?»

8Pero tú, Señor, te burlas de ellos;

te ríes de todas las naciones.

9A ti, fortaleza mía, vuelvo los ojos,

pues tú, oh Dios, eres mi protector.

10Tú eres el Dios que me ama,

e irás delante de mí

para hacerme ver la derrota de mis enemigos.

11Pero no los mates,

para que mi pueblo no lo olvide.

Zarandéalos con tu poder; ¡humíllalos!

¡Tú, Señor, eres nuestro escudo!

12Por los pecados de su boca,

por las palabras de sus labios,

que caigan en la trampa de su orgullo.

Por las maldiciones y mentiras que profieren,

13consúmelos en tu enojo;

¡consúmelos hasta que dejen de existir!

Así todos sabrán que Dios gobierna en Jacob,

y hasta los confines de la tierra. Selah

14Porque ellos vuelven por la noche,

gruñendo como perros

y acechando alrededor de la ciudad.

15Van de un lado a otro buscando comida,

y aúllan si no quedan satisfechos.

16Pero yo le cantaré a tu poder,

y por la mañana alabaré tu amor;

porque tú eres mi protector,

mi refugio en momentos de angustia.

17A ti, fortaleza mía, te cantaré salmos,

pues tú, oh Dios, eres mi protector.

¡Tú eres el Dios que me ama!