Masalimo 57 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 57:1-11

Salimo 57

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Musawononge.” Ndakatulo ya Davide, pamene anathawa Sauli kupita ku phanga.

1Mundichitire chifundo, Inu Mulungu mundichitire chifundo,

pakuti mwa Inu moyo wanga umathawiramo.

Ndidzathawira mu mthunzi wa mapiko anu

mpaka chiwonongeko chitapita.

2Ine ndikufuwulira kwa Mulungu Wammwambamwamba,

kwa Mulungu amene amakwaniritsa cholinga chake pa ine.

3Mulungu amanditumizira kuchokera kumwamba ndi kundipulumutsa,

kudzudzula iwo amene akundithamangitsa kwambiri.

Mulungu amatumiza chikondi chake ndi kukhulupirika kwake.

4Ine ndili pakati pa mikango,

ndagona pakati pa zirombo zolusa;

anthu amene mano awo ndi milomo yawo ndi mivi,

malilime awo ndi malupanga akuthwa.

5Mukwezekedwe Inu Mulungu, kuposa mayiko onse akumwamba;

mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.

6Iwo anatchera mapazi anga ukonde

ndipo ndinawerama pansi mosautsidwa.

Anakumba dzenje mʼnjira yanga

koma agweramo okha mʼmenemo.

7Mtima wanga ndi wokhazikika, Inu Mulungu

mtima wanga ndi wokhazikika.

Ndidzayimba nyimbo, nyimbo yake yamatamando.

8Dzuka moyo wanga!

Dzukani zeze ndi pangwe!

Ndidzadzuka mʼbandakucha.

9Ndidzakutamandani Ambuye, pakati pa mitundu ya anthu,

ndidzayimba za Inu pakati pa mayiko.

10Pakuti chikondi chanu nʼchachikulu, kufikira ku mayiko akumwamba;

kukhulupirika kwanu kwafika ku mitambo.

11Mukwezekedwe Inu Mulungu kuposa mayiko akumwamba,

mulole kuti ulemerero wanu ukhale pa dziko lonse lapansi.