Masalimo 56 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 56:1-13

Salimo 56

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Potsata mayimbidwe a “Njiwa pa Mtengo wa Thundu wa Kutali.” Mikitamu ya Davide, pamene Afilisti anamugwira ku Gati.

1Mundichitire chifundo Inu Mulungu, pakuti anthu akundithamangitsa kwambiri;

tsiku lonse akundithira nkhondo.

2Ondinyoza akundithamangitsa tsiku lonse,

ambiri akumenyana nane monyada.

3Ndikachita mantha

ndimadalira Inu.

4Mwa Mulungu, amene mawu ake ine ndimatamanda,

mwa Mulungu ine ndimadaliramo; sindidzachita mantha.

Kodi munthu amene amafa angandichite chiyani?

5Tsiku lonse amatembenuza mawu anga;

nthawi zonse amakonza zondivulaza.

6Iwo amakambirana, amandibisalira,

amayangʼanitsitsa mayendedwe anga

ndipo amakhala ndi chidwi chofuna kuchotsa moyo wanga.

7Musalole konse kuti athawe;

mu mkwiyo wanu Mulungu mugwetse mitundu ya anthu.

8Mulembe za kulira kwanga,

mulembe chiwerengero cha misozi yanga mʼbuku lanu.

Kodi zimenezi sizinalembedwe mʼbuku lanulo?

9Adani anga adzabwerera mʼmbuyo

pamene ndidzalirira kwa Inu.

Pamenepo ndidzadziwa kuti Mulungu ali ku mbali yanga.

10Mwa Mulungu amene mawu ake ndimawatamanda,

mwa Yehova amene mawu ake ndimawatamanda,

11mwa Mulungu ine ndimadalira ndipo sindidzachita mantha.

Kodi munthu angandichite chiyani?

12Ndiyenera kuchita zomwe ndinalumbira kwa Mulungu;

ndidzapereka nsembe zanga zachiyamiko kwa inu.

13Pakuti mwawombola moyo wanga ku imfa

ndi mapazi anga kuti ndingagwe,

kuti ndiyende pamaso pa Mulungu

mʼkuwala kwa moyo.