Masalimo 55 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 55:1-23

Salimo 55

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Ndakatulo ya Davide. Pa zoyimbira za zingwe.

1Mvetserani pemphero langa, Inu Mulungu,

musakufulatire kupempha kwanga,

2mverani ndipo mundiyankhe.

Maganizo anga akundisautsa ndipo ndathedwa nzeru

3chifukwa cha mawu a adani anga,

chifukwa cha kupondereza kwa anthu oyipa;

pakuti andidzetsera masautso

ndipo akundizunza mu mkwiyo wawo.

4Mtima wanga ukupweteka mʼkati mwanga;

mantha a imfa andigwera.

5Mantha ndi kunjenjemera zandizinga;

mantha aakulu andithetsa nzeru.

6Ndinati, “Ndithu, ndikanakhala ndi mapiko ankhunda!

Ndikanawulukira kutali ndi kukapuma.

7Ndikanathawira kutali

ndi kukakhala mʼchipululu.

8Ndikanathamangira kumalo anga a chitetezo;

kutali ndi mphepo yaukali ndi yamkuntho.”

9Sokonezani maganizo a oyipa, Inu Ambuye, tsutsani mawu awo;

pakuti ine ndikuona chiwawa ndi mkangano mu mzinda.

10Usana ndi usiku iwo akuzungulirazungulira pa makoma ake;

nkhwidzi ndi kuzunza kuli mʼkati mwake.

11Mphamvu zowononga zili pa ntchito mu mzinda;

kuopseza ndi mabodza sizichoka mʼmisewu yake.

12Akanakhala mdani akundinyoza, ine

ndikanapirira;

akanakhala mdani akudzikweza yekha kutsutsana nane,

ndikanakabisala.

13Koma iweyo mnzanga, mnzanga woyenda naye,

bwenzi langa la pondaapanʼpondepo, ndi amene ukuchita zimenezi.

14Mnzanga amene nthawi ina tinkasangalala

pa chiyanjano chokoma ku nyumba ya Mulungu.

15Mulole imfa itenge adani anga mwadzidzidzi;

alowe mʼmanda ali amoyo

pakuti choyipa chili pakati pawo.

16Koma ine ndinafuwulira kwa Mulungu,

ndipo Yehova anandipulumutsa.

17Madzulo, mmawa ndi masana

ndimalira mowawidwa mtima,

ndipo Iye amamva mawu anga.

18Iye amandiwombola ine osavulazidwa

pa nkhondo imene yafika kulimbana nane,

ngakhale kuti ndi ambiri amene akunditsutsa.

19Mulungu amene ali pa mpando wake kwamuyaya,

adzandimenyera nkhondo; adzawatsitsa adani anga,

chifukwa safuna kusintha njira zawo zoyipa

ndipo saopa Mulungu.

20Mnzanga woyenda naye wathira nkhondo abwenzi ake;

iye akuphwanya pangano ake.

21Mawu ake ndi osalala kuposa batala

komabe nkhondo ili mu mtima mwake;

mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta,

komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.

22Tulani nkhawa zanu kwa Yehova

ndipo Iye adzakulimbitsani;

Iye sadzalola kuti wolungama agwe.

23Koma Inu Mulungu mudzawatsitsa anthu oyipa

kulowa mʼdzenje lachiwonongeko;

anthu okhetsa magazi ndi anthu achinyengo

sadzakhala moyo theka la masiku awo,

koma ine ndimadalira Inu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 55:1-23

第 55 篇

被朋友出賣者的禱告

大衛作的訓誨詩,交給樂長,用弦樂器。

1上帝啊,

求你垂聽我的禱告,

不要對我的呼求置之不理。

2求你垂聽、應允我的呼求。

我思緒煩亂,坐立不安。

3仇敵向我咆哮,

惡人迫害我。

他們帶給我苦難,

怒氣沖沖地辱罵我。

4我內心悲痛,

被死亡的恐怖籠罩。

5我渾身顫慄,驚恐不已。

6啊,但願我能像鴿子展翅飛去,

得享安息。

7我要飛到遠方,住在曠野。(細拉)

8我要趕快躲進避難所,

避過暴雨狂風。

9主啊,

我在城中看見暴力和爭鬥,

求你使他們言語混亂。

10他們晝夜在城牆上出沒,

城內充滿了邪惡和壓迫,

11毀壞的勢力到處肆虐,

恐嚇與欺詐遍佈大街小巷。

12倘若是仇敵辱罵我,

我還能忍受;

倘若是恨我的人欺凌我,

我還可以躲開。

13可是,竟然是你——我志同道合的夥伴,我的摯友!

14從前我們情誼深厚,

與眾人同去上帝的殿。

15願死亡突然抓住我的仇敵,

願他們活活地下陰間,

因為他們的內心和家中罪惡充斥。

16但我要呼求耶和華上帝,

祂必拯救我。

17晚上、早晨和中午,

我發出痛苦的呼求,

祂必垂聽。

18雖然許多人攻擊我,

祂必救我平安脫離險境。

19永掌王權的上帝必鑒察並懲罰他們,

因為他們頑梗悖逆、不敬畏上帝。

20我的同伴違背盟約,攻擊朋友。

21他口蜜腹劍,笑裡藏刀。

22把你的重擔卸給耶和華,

祂必扶持你。

祂必不讓義人跌倒。

23上帝啊,

你必把惡人送進滅亡的坑裡。

嗜血成性的騙子必早早夭亡。

但我要信靠你。