Masalimo 45 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 45:1-17

Salimo 45

Kwa mtsogoleri wamayimbidwe. Monga mwa mayimbidwe a “Maluwa a Kakombo.” Salimo la ana a Kora. Nyimbo ya pa ukwati.

1Mtima wanga watakasika ndi nkhani yokoma

pamene ndikulakatula mawu anga kwa mfumu;

lilime langa ndi cholembera cha wolemba waluso.

2Inu ndinu abwino kwambiri kuposa anthu onse

ndipo milomo yanu inadzozedwa ndi chikondi cha Mulungu chosasinthika,

popeza Mulungu wakudalitsani kwamuyaya.

3Mangirirani lupanga lanu mʼchiwuno mwanu, inu munthu wamphamvu;

mudziveke nokha ndi ulemerero ndi ukulu wanu.

4Mu ukulu wanu mupite mutakwera mwachigonjetso

mʼmalo mwa choonadi, kudzichepetsa ndi chilungamo;

dzanja lanu lamanja lionetsere ntchito zanu zoopsa.

5Mivi yanu yakuthwa ilase mitima ya adani a mfumu,

mitundu ya anthu igwe pansi pa mapazi anu.

6Mpando wanu waufumu, Inu Mulungu, udzakhala ku nthawi za nthawi;

ndodo yaufumu yachilungamo idzakhala ndodo yaufumu ya ufumu wanu.

7Inu mumakonda chilungamo ndi kudana ndi zoyipa;

choncho Mulungu, Mulungu wanu, wakukhazikani pamwamba pa anzanu

pokudzozani ndi mafuta a chimwemwe.

8Mikanjo yanu yonse ndi yonunkhira ndi mure ndi aloe ndi kasiya;

kuchokera ku nyumba zaufumu zokongoletsedwa ndi mnyanga wanjovu

nyimbo za zoyimbira zazingwe zimakusangalatsani.

9Ana aakazi a mafumu ali pakati pa akazi anu olemekezeka;

ku dzanja lanu lamanja kuli mkwatibwi waufumu ali mu golide wa ku Ofiri.

10Tamvera, iwe mwana wa mkazi ganizira ndipo tchera khutu;

iwala anthu ako ndi nyumba ya abambo ako.

11Mfumu yathedwa nzeru chifukwa cha kukongola kwako;

mulemekeze pakuti iyeyo ndiye mbuye wako.

12Mwana wa mkazi wa ku Turo adzabwera ndi mphatso,

amuna a chuma adzafunafuna kukoma mtima kwako.

13Wokongola kwambiri ndi mwana wa mfumu ali mʼchipinda mwake,

chovala chake ndi cholukidwa ndi thonje ndi golide.

14Atavala zovala zamaluwamaluwa akupita naye kwa mfumu;

anamwali okhala naye akumutsatira

ndipo abweretsedwa kwa inu.

15Iwo akuwaperekeza ndi chimwemwe ndi chisangalalo;

akulowa mʼnyumba yaufumu.

16Ana ako aamuna adzatenga malo a makolo ako;

udzachititsa kuti akhale ana a mfumu mʼdziko lonse.

17Ndidzabukitsa mbiri yako mʼmibado yonse;

choncho mitundu yonse idzakutamanda ku nthawi za nthawi.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 45:1-17

第 45 篇

婚禮詩歌

可拉後裔作的訓誨詩,也是婚禮上唱的情歌,交給樂長,調用「百合花」。

1我心中湧出美麗的詩章,

我要把它獻給王,

我的舌頭是詩人手上的妙筆。

2你俊美無比,口出恩言,

因此上帝永遠賜福給你。

3偉大的王啊,

佩上你的寶劍,

你是何等尊貴、威嚴!

4你威嚴無比,所向披靡,

捍衛真理和正義,

保護卑微的人。

願你的右手彰顯可畏的作為!

5你的利箭刺穿敵人的心窩,

列國臣服在你腳下。

6上帝啊,你的寶座永遠長存,

你以公義的杖執掌王權。

7你喜愛公義,憎惡邪惡,

因此上帝,你的上帝,

用喜樂之油膏你,

使你超過同伴。

8你的衣袍散發出沒藥、沉香和肉桂的芬芳,

你陶醉在象牙宮的弦樂中。

9眾公主在你的貴客中,

俄斐金飾的王后站在你右邊。

10女子啊,

要側耳傾聽:不要再掛念家鄉的父老,

11王喜歡你的美貌,

你要敬重他,因他是你的主。

12泰爾人必來送禮,

富人必來取悅你。

13公主身穿金線衣,無比華貴。

14她身披錦繡,

由侍女伴隨前來見王,

15她們歡喜快樂地進入王宮。

16你的子孫將來要繼承祖先的王位,

你要立他們在各地做王。

17我要使你的名世代受尊崇,

萬民必永遠稱謝你。