Masalimo 41 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 41:1-13

Salimo 41

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Wodala ndi munthu amene amaganizira anthu osauka;

Yehova amamuwombola pa nthawi yamsautso.

2Yehova adzamuteteza ndi kusunga moyo wake;

Yehova adzamudalitsa iye mʼdziko

ndipo sadzamupereka ku zofuna za adani ake.

3Yehova adzamuthandiza pamene akudwala

ndipo adzamuchiritsa pa bedi lake la matenda.

4Ndinati, “Inu Yehova, mundichitire chifundo;

chiritseni pakuti ndakuchimwirani.”

5Adani anga mwankhwidzi amanena za ine kuti,

“Kodi munthu ameneyu adzafa liti kuti ayiwalike?”

6Pamene wina abwera kudzandiona,

amayankhula mwachinyengo, pomwe mtima wake ukusonkhanitsa zachipongwe;

kenaka iye amatuluka ndi kukalengeza kunja.

7Adani anga onse amanongʼonezana pamodzi kulimbana nane,

iwo amalingalira zoyipa kwambiri za ine, ponena kuti,

8“Matenda owopsa amugwira;

sadzaukapo pamalo pamene wagona.”

9Ngakhale bwenzi langa la pamtima amene ndinamudalira,

iye amene amadya pamodzi ndi ine

watukula chidendene chake kulimbana nane.

10Koma Yehova mundichititre chifundo,

dzutseni kuti ndiwabwezere.

11Ine ndikudziwa kuti mukukondwera nane,

pakuti mdani wanga sandigonjetsa.

12Mu ungwiro wanga Inu mumandisunga

ndi kundiyimika pamaso panu kwamuyaya.

13Atamandike Yehova Mulungu wa Israeli

kuchokera muyaya mpaka muyaya.

Ameni ndi Ameni.