Masalimo 38 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 38:1-22

Salimo 38

Salimo la Davide. Kupempha.

1Yehova musandidzudzule mutapsa mtima

kapena kundilanga muli ndi ukali.

2Pakuti mivi yanu yandilasa,

ndipo dzanja lanu latsika ndipo landifikira.

3Chifukwa cha ukali wanu mulibe thanzi mʼthupi langa;

mafupa anga alibe mphamvu chifukwa cha tchimo langa.

4Kulakwa kwanga kwandipsinja

ngati katundu wolemera kwambiri kuposa mphamvu zanga.

5Mabala anga akuwola ndipo akununkha

chifukwa cha uchitsiru wa moyo wanga wauchimo.

6Ine ndapindika msana ndipo ndawerama kwambiri;

tsiku lonse ndimangolira.

7Msana wanga wagwidwa ndi ululu wosasimbika,

mulibe thanzi mʼthupi langa.

8Ndilibe mphamvu ndipo ndakunthidwa kwathunthu;

ndikubuwula ndi ululu wa mumtima.

9Zokhumba zanga zonse zili poonekera pamaso panu Ambuye,

kusisima kwanga sikunabisike kwa Inu.

10Mtima wanga ukugunda, mphamvu zanga zikutha;

ngakhale kuwala kwachoka mʼmaso mwanga.

11Abwenzi anga ndi anzanga akundipewa chifukwa cha mabala anga;

anansi anga akhala kutali nane.

12Iwo amene akufunafuna moyo wanga atchera misampha yawo,

oti andipwetekewo amayankhula za kuwonongeka kwanga;

tsiku lonse amakonza zachinyengo.

13Ine ndili ngati munthu wosamva amene sangamve,

monga wosayankhula, amene sangathe kutsekula pakamwa pake;

14Ndakhala ngati munthu amene samva,

amene pakamwa pake sipangathe kuyankha.

15Ndikudikira Inu Yehova;

mudzayankha, Inu Ambuye Mulungu wanga.

16Pakuti Ine ndinati, “Musawalole kuti akondwere

kapena kudzikweza okha pa ine pamene phazi langa laterereka.”

17Pakuti ndili pafupi kugwa,

ndipo ndikumva kuwawa nthawi zonse.

18Ndikuvomereza mphulupulu zanga;

ndipo ndavutika ndi tchimo langa.

19Ambiri ndi adani anga amphamvu;

amene amandida popanda chifukwa alipo ochuluka kwambiri.

20Iwo amene amandibwezera zoyipa mʼmalo mwa zabwino

amandinyoza pamene nditsatira zabwino.

21Inu Yehova, musanditaye;

musakhale kutali ndi ine Mulungu wanga.

22Bwerani msanga kudzandithandiza,

Inu Ambuye Mpulumutsi wanga.