Masalimo 36 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 36:1-12

Salimo 36

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide, mtumiki wa Yehova.

1Uthenga uli mu mtima mwanga

wonena za kuchimwa kwa munthu woyipa:

Mu mtima mwake

mulibe kuopa Mulungu.

2Pakuti iye mʼkuona kwake amadzinyenga yekha kwambiri,

sazindikira kapena kudana ndi tchimo lake.

3Mawu a pakamwa pake ndi oyipa ndi achinyengo;

iyeyo waleka kukhala wanzeru ndi kuchita zabwino.

4Ngakhale ali pa bedi pake amakonzekera zoyipa;

iye amadzipereka yekha ku njira ya uchimo

ndipo sakana cholakwa chilichonse.

5Chikondi chanu Yehova, chimafika ku mayiko a kumwamba,

kukhulupirika kwanu mpaka ku mitambo.

6Chilungamo chanu Mulungu chili ngati mapiri aakulu,

chiweruzo chanu chili ngati kuzama kwakukulu.

Yehova mumasunga munthu pamodzi ndi chinyama.

7Chikondi chanu chosatha ndi chamtengowapatali!

Otchuka pamodzi ndi anthu wamba pakati pa anthu

amapeza pothawirapo mu mthunzi wa mapiko anu.

8Iwo amadyerera zinthu zambiri za mʼnyumba yanu;

Inu mumawapatsa chakumwa kuchokera mu mtsinje wanu wachikondwerero.

9Pakuti kwa Inu kuli kasupe wamoyo;

mʼkuwala kwanu ifenso timaona kuwala.

10Pitirizani chikondi chanu pa iwo amene amakudziwani,

chilungamo chanu kwa olungama mtima.

11Musalole kuti phazi la wodzikuza libwere kulimbana nane,

kapena dzanja la oyipa kundithamangitsa.

12Onani momwe ochita zoyipa agonera atagwa,

aponyeni pansi, kuti asathe kudzukanso!