Masalimo 35 – CCL & KJV

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 35:1-28

Salimo 35

Salimo la Davide.

1Inu Yehova, mulimbane nawo amene akulimbana nane;

mumenyane nawo amene akumenyana nane.

2Tengani chishango ndi lihawo;

dzukani ndipo bwerani mundithandize.

3Tengani mkondo ndi nthungo,

kulimbana ndi iwo amene akundithamangitsa.

Uzani moyo wanga kuti,

“Ine ndine chipulumutso chako.”

4Iwo amene akufunafuna moyo wanga

anyozedwe ndi kuchita manyazi;

iwo amene akukonza kuti moyo wanga uwonongeke

abwerere mʼmbuyo mochititsa mantha.

5Akhale ngati mankhusu owuluka ndi mphepo

pamene mngelo wa Yehova akuwapirikitsa.

6Njira yawo ikhale ya mdima ndi yoterera

pamene mngelo wa Yehova akuwathamangitsa.

7Popeza ananditchera ukonde popanda chifukwa

ndipo popanda chifukwa andikumbira dzenje,

8chiwonongeko chiwapeza modzidzimutsa

ukonde umene iwo abisa uwakole,

agwere mʼdzenje kuti awonongedwe.

9Pamenepo moyo wanga udzakondwera mwa Yehova

ndi kusangalala ndi chipulumutso chake.

10Thupi langa lidzafuwula mokondwera,

“Ndani angafanane nanu Yehova?

Mumalanditsa osauka kwa amene ali ndi mphamvu zambiri,

osauka ndi osowa kwa iwo amene amawalanda.”

11Mboni zopanda chisoni zinayimirira,

zinandifunsa zinthu zimene sindikuzidziwa.

12Iwo anandibwezera zoyipa pa zabwino

ndipo anasiya moyo wanga pa chisoni.

13Koma pamene iwo ankadwala, ine ndinavala chiguduli

ndi kudzichepetsa ndekha posala zakudya.

Pamene mapemphero anga anabwerera kwa ine osayankhidwa,

14ndinayendayenda ndi kulira maliro,

kumulira ngati bwenzi langa kapena mʼbale wanga.

Ndinaweramitsa mutu wanga mosweka mtima

kukhala ngati ndikulira amayi anga.

15Koma pamene ndinaphunthwa, iwo anasonkhana mosangalala;

ondithira nkhondo anasonkhana kutsutsana nane, ineyo osadziwa.

Iwo sanasiye kundiyankhulira mawu onyoza.

16Monga anthu osapembedza, iwo anandinyoza mwachipongwe;

anandikukutira mano awo.

17Ambuye, mpaka liti mudzakhala mukungoyangʼana?

Landitsani moyo wanga ku chiwonongeko chawo,

moyo wanga wopambana ku mikango.

18Ndidzakuyamikani mu msonkhano waukulu;

pakati pa gulu lalikulu la anthu ndidzakutamandani.

19Musalole adani anga onyenga

akondwere chifukwa cha masautso anga;

musalole kuti amene amadana nane popanda chifukwa

andiyangʼane chamʼmbali mondinyoza.

20Iwowo sayankhula mwamtendere,

koma amaganizira zonamizira

iwo amene amakhala mwabata mʼdziko.

21Iwo amandiseka mofuwula ndipo amati, “Haa! Haa!

Ndipo ndi maso athuwa ife taziona.”

22Yehova mwaona zimenezi; musakhale chete.

Ambuye musakhale kutali ndi ine.

23Dzukani, ndipo nyamukani kunditeteza!

Mulimbane nawo chifukwa cha ine, Mulungu wanga ndi Ambuye anga.

24Onetsani kusalakwa kwanga mwa chilungamo chanu, Inu Yehova Mulungu wanga.

Musalole kuti akondwere chifukwa cha mavuto anga.

25Musalole kuti aganize kuti, “Amati atani, zachitika monga momwe timafunira!”

Kapena kunena kuti, “Tamutha ameneyu basi.”

26Onse amene amakondwera ndi masautso anga

achite manyazi ndi kusokonezeka.

Onse amene amadzikweza kufuna kundipambana,

avekedwe manyazi ndi mnyozo ngati zovala.

27Koma amene amakondwera chifukwa chakuti ndine wosalakwa,

afuwule mwachimwemwe ndi chisangalalo.

Nthawi zonse azinena kuti, “Yehova akwezeke,

Iye amene amakondwera ndi kupeza bwino kwa mtumiki wake.”

28Pakamwa panga padzayankhula za chilungamo chanu

ndi za matamando anu tsiku lonse.

King James Version

Psalms 35:1-28

A Psalm of David.

1Plead my cause, O LORD, with them that strive with me: fight against them that fight against me.

2Take hold of shield and buckler, and stand up for mine help.

3Draw out also the spear, and stop the way against them that persecute me: say unto my soul, I am thy salvation.

4Let them be confounded and put to shame that seek after my soul: let them be turned back and brought to confusion that devise my hurt.

5Let them be as chaff before the wind: and let the angel of the LORD chase them.

6Let their way be dark and slippery: and let the angel of the LORD persecute them.35.6 dark…: Heb. darkness and slipperiness

7For without cause have they hid for me their net in a pit, which without cause they have digged for my soul.

8Let destruction come upon him at unawares; and let his net that he hath hid catch himself: into that very destruction let him fall.35.8 at…: Heb. which he knoweth not of

9And my soul shall be joyful in the LORD: it shall rejoice in his salvation.

10All my bones shall say, LORD, who is like unto thee, which deliverest the poor from him that is too strong for him, yea, the poor and the needy from him that spoileth him?

11False witnesses did rise up; they laid to my charge things that I knew not.35.11 False…: Heb. Witnesses of wrong35.11 they…: Heb. they asked me

12They rewarded me evil for good to the spoiling of my soul.35.12 spoiling: Heb. depriving

13But as for me, when they were sick, my clothing was sackcloth: I humbled my soul with fasting; and my prayer returned into mine own bosom.35.13 humbled: or, afflicted

14I behaved myself as though he had been my friend or brother: I bowed down heavily, as one that mourneth for his mother.35.14 behaved myself: Heb. walked35.14 as though…: Heb. as a friend, as a brother to me

15But in mine adversity they rejoiced, and gathered themselves together: yea, the abjects gathered themselves together against me, and I knew it not; they did tear me, and ceased not:35.15 adversity: Heb. halting

16With hypocritical mockers in feasts, they gnashed upon me with their teeth.

17Lord, how long wilt thou look on? rescue my soul from their destructions, my darling from the lions.35.17 darling: Heb. only one

18I will give thee thanks in the great congregation: I will praise thee among much people.35.18 much: Heb. strong

19Let not them that are mine enemies wrongfully rejoice over me: neither let them wink with the eye that hate me without a cause.35.19 wrongfully: Heb. falsely

20For they speak not peace: but they devise deceitful matters against them that are quiet in the land.

21Yea, they opened their mouth wide against me, and said, Aha, aha, our eye hath seen it.

22This thou hast seen, O LORD: keep not silence: O Lord, be not far from me.

23Stir up thyself, and awake to my judgment, even unto my cause, my God and my Lord.

24Judge me, O LORD my God, according to thy righteousness; and let them not rejoice over me.

25Let them not say in their hearts, Ah, so would we have it: let them not say, We have swallowed him up.35.25 Ah…: Heb. Ah, ah, our soul

26Let them be ashamed and brought to confusion together that rejoice at mine hurt: let them be clothed with shame and dishonour that magnify themselves against me.

27Let them shout for joy, and be glad, that favour my righteous cause: yea, let them say continually, Let the LORD be magnified, which hath pleasure in the prosperity of his servant.35.27 righteous…: Heb. righteousness

28And my tongue shall speak of thy righteousness and of thy praise all the day long.