Masalimo 34 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 34:1-22

Salimo 34

Salimo la Davide. Pamene iye ananyengezera misala pamaso pa Abimeleki, amene anamupirikitsa, iyeyo nʼkuchoka.

1Ndidzayamika Yehova nthawi zonse;

matamando ake adzakhala pa milomo yanga nthawi zonse.

2Moyo wanga udzanyadira Yehova;

anthu osautsidwa amve ndi kukondwera.

3Lemekezani Yehova pamodzi ndi ine;

tiyeni pamodzi tikuze dzina lake.

4Ine ndinafunafuna Yehova ndipo Iye anandiyankha;

anandilanditsa ku mantha anga onse.

5Iwo amene amayangʼana kwa Iye, nkhope zawo zimanyezimira;

nkhope zawo sizikhala zophimbidwa ndi manyazi.

6Munthu wosauka uno anayitana, ndipo Yehova anamumva;

Yehova anamupulumutsa ku mavuto ake onse.

7Mngelo wa Yehova amatchinjiriza amene amakonda Iye

ndi kuwalanditsa.

8Lawani ndipo onani kuti Yehova ndi wabwino;

wodala munthu amene amathawira kwa Iye.

9Wopani Yehova inu oyera mtima ake,

pakuti iwo amene amaopa Iye sasowa kanthu.

10Mikango itha kulefuka ndi kumva njala

koma iwo amene amafunafuna Yehova sasowa kanthu kalikonse kabwino.

11Bwerani ana anga, mundimvere;

ndidzakuphunzitsani kuopa Yehova.

12Aliyense wa inu amene amakonda moyo wake

ndi kukhumba kuti aone masiku abwino ambiri,

13asunge lilime lake ku zoyipa

ndi milomo yake kuti isayankhule zonama.

14Tembenuka kuchoka ku zoyipa ndipo chita zabwino;

funafuna mtendere ndi kuwulondola.

15Maso a Yehova ali pa olungama

ndipo makutu ake ali tcheru kumva kulira kwawo;

16nkhope ya Yehova ikutsutsana ndi amene amachita zoyipa,

kuwachotsa kuti asawakumbukirenso pa dziko lapansi.

17Olungama amafuwula, ndipo Yehova amawamva;

Iye amawalanditsa ku mavuto awo onse.

18Yehova ali pafupi kwa osweka mtima

ndipo amapulumutsa iwo amene asweka mu mzimu.

19Munthu wolungama atha kukhala ndi mavuto ambiri,

Koma Yehova amamulanditsa ku mavuto onsewo,

20Iye amateteza mafupa ake onse,

palibe limodzi la mafupawo limene lidzathyoledwa.

21Choyipa chidzapha anthu oyipa;

adani a olungama adzapezeka olakwa.

22Yehova amawombola atumiki ake;

aliyense amene amathawira kwa Iye sadzapezeka wolakwa.