Masalimo 33 – CCL & CCBT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 33:1-22

Salimo 33

1Imbirani Yehova mokondwera Inu olungama,

nʼkoyenera kuti owongoka mtima azitamanda Iyeyo.

2Mutamandeni Yehova ndi pangwe;

muyimbireni Iye nyimbo pa zeze wa zingwe khumi.

3Muyimbireni nyimbo yatsopano;

imbani mwaluso, ndipo fuwulani mwachimwemwe.

4Pakuti mawu a Yehova ndi olungama ndi owona;

Iye ndi wokhulupirika pa zonse zimene amachita.

5Yehova amakonda chilungamo ndipo amaweruza molungama;

dziko lapansi ladzaza ndi chikondi chake chosatha.

6Ndi mawu a Yehova mayiko akumwamba anapangidwa,

zolengedwa zake ndi mpweya wa mʼkamwa mwake.

7Iye amasonkhanitsa pamodzi madzi a mʼnyanja mʼmitsuko;

amayika zozama mʼnyumba zosungiramo.

8Dziko lonse lapansi liope Yehova;

anthu onse amulemekeze Iye.

9Pakuti Iye anayankhula ndipo zinakhalapo;

Iye analamulira ndipo zinakhazikika.

10Yehova amalepheretsa chikonzero cha anthu a mitundu ina;

Iye amaphwanya zolinga za anthu ambiri.

11Koma chikonzero cha Yehova chimakhala mpaka muyaya,

zolinga za mu mtima mwake pa mibado yonse.

12Wodala mtundu wa anthu umene Mulungu wake ndi Yehova,

anthu amene Iye anawasankha kukhala cholowa chake.

13Kuchokera kumwamba Yehova amayangʼana pansi

ndi kuona anthu onse;

14kuchokera ku malo ake okhalako Iye amayangʼanira

onse amene amakhala pa dziko lapansi.

15Iye amene amapanga mitima ya onse,

amaona zonse zimene akuchita.

16Palibe mfumu imene imapulumutsidwa chifukwa cha kukula kwa gulu lake lankhondo;

palibe msilikali amene amathawa ndi mphamvu zake zazikulu.

17Kavalo ndi chiyembekezo cha chabechabe cha chipulumutso,

ngakhale ali ndi mphamvu yayikulu sangathe kupulumutsa.

18Koma maso a Yehova ali pa iwo amene amaopa Iye;

amene chiyembekezo chawo chili mʼchikondi chake chosatha,

19kuwawombola iwo ku imfa

ndi kuwasunga ndi moyo nthawi ya njala.

20Ife timadikira kwa Yehova mwachiyembekezo;

Iye ndiye thandizo lathu ndi chishango chathu.

21Mwa Iye mitima yathu imakondwera,

pakuti ife timadalira dzina lake loyera.

22Chikondi chanu chosatha

chikhale pa ife Inu Yehova, pamene tikuyembekeza kwa Inu.

Chinese Contemporary Bible (Traditional)

詩篇 33:1-22

第 33 篇

頌讚之歌

1義人啊,

你們要歡然歌頌耶和華,

正直的人理應讚美祂。

2你們要彈琴讚美耶和華,

彈奏十弦琴讚美祂。

3要為祂唱新歌,

琴聲要美妙,歌聲要嘹亮。

4因為耶和華的話是真理,

祂的作為信實可靠。

5祂喜愛公平正義,

大地充滿祂的慈愛。

6諸天靠祂的話而造,

群星靠祂口中的氣而成。

7祂將海水聚在一處,把汪洋收進倉庫。

8願普世都敬畏耶和華!

願世人都尊崇祂!

9因為祂一發話,就創造了天地;

祂一命令,就立定了萬物。

10祂挫敗列國的謀算,

攔阻列邦的計劃。

11祂的計劃永不落空,

祂的旨意萬代長存。

12尊祂為上帝的邦國有福了!

蒙揀選做祂子民的人有福了!

13祂從天上俯視人間,

14從祂的居所察看世上萬民。

15祂塑造人心,

洞察人的一切行為。

16君王不能靠兵多取勝,

勇士不能憑力大獲救。

17靠戰馬取勝實屬妄想,

馬雖力大也不能救人。

18但耶和華看顧敬畏祂、仰望祂慈愛的人。

19祂救他們脫離死亡,

保護他們度過饑荒。

20我們仰望耶和華,

祂是我們的幫助,

是我們的盾牌。

21我們信靠祂的聖名,

我們的心因祂而充滿喜樂。

22耶和華啊,我們仰望你,求你向我們施慈愛。