Masalimo 31 – Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero CCL

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 31:1-24

Salimo 31

Kwa mtsogoleri wa mayimbidwe. Salimo la Davide.

1Mwa Inu Yehova, ine ndimathawiramo;

musalole nʼkomwe kuti ndichititsidwe manyazi;

mundipulumutse chifukwa cha chilungamo chanu.

2Tcherani khutu lanu kwa ine,

bwerani msanga kudzandilanditsa;

mukhale thanthwe langa lothawirapo,

linga lolimba kundipulumutsa ine.

3Popeza Inu ndinu thanthwe langa ndi linga langa,

chifukwa cha dzina lanu tsogolereni ndi kundiwongolera.

4Ndimasuleni mu msampha umene anditchera

pakuti ndinu pothawirapo panga.

5Mʼmanja mwanu ndipereka mzimu wanga;

womboleni Yehova Mulungu wachoonadi.

6Koma ine ndimadana nawo amene amamamatira mafano achabechabe;

ine ndimadalira Yehova.

7Ndidzakondwa ndi kusangalala mʼchikondi chanu

popeza Inu munaona masautso anga

ndipo mumadziwa kuwawa kwa moyo wanga.

8Inu simunandipereke kwa mdani

koma mwayika mapazi anga pa malo otakasuka.

9Mundichitire chifundo Inu Yehova pakuti ndili pa mavuto;

maso anga akulefuka ndi chisoni,

mʼmoyo mwanga ndi mʼthupi mwanga momwe mukupweteka.

10Moyo wanga ukunyeka chifukwa cha kuwawidwa mtima

ndi zaka zanga chifukwa cha kubuwula;

mphamvu zanga zatha chifuwa cha masautso,

ndipo mafupa anga akulefuka.

11Chifukwa cha adani anga onse,

ndine wonyozeka kwambiri ndi anansi anga;

ndine chochititsa manyazi kwa abwenzi anga.

Iwo amene amandiona mu msewu amandithawa.

12Ine ndinayiwalika kwa iwo ngati kuti ndinamwalira;

ndakhala ngati mʼphika wosweka.

13Pakuti ine ndamva zonena zoyipa za anthu ambiri;

zoopsa zandizungulira mbali zonse;

iwo akukonza chiwembu kuti alimbane nane,

kuti atenge moyo wanga.

14Koma ndikudalira Inu Yehova;

ndikunena kuti, “Ndinu Mulungu wanga.”

15Masiku anga ali mʼmanja mwanu;

ndipulumutseni kwa adani anga

ndi kwa iwo amene akundithamangitsa.

16Walitsani nkhope yanu pa mtumiki wanu;

pulumutseni mwa chikondi chanu chosatha.

17Yehova musalole kuti ndichite manyazi,

pakuti ndalirira kwa Inu;

koma oyipa achititsidwe manyazi

ndipo agone chete mʼmanda.

18Milomo yawo yabodzayo ikhale chete,

pakuti chifukwa cha kunyada

ayankhula modzikuza kutsutsana ndi wolungama.

19Ndi waukulu ubwino wanu

umene mwawasungira amene amakuopani,

umene mumapereka anthu akuona

kwa iwo amene amathawira kwa Inu.

20Mu mthunzi wa pamalo popezeka panu muwabisa,

kuwateteza ku ziwembu za anthu;

mʼmalo anu okhalamo mumawateteza

kwa anthu owatsutsa.

21Matamando akhale kwa Yehova,

pakuti anaonetsa chikondi chake chodabwitsa kwa ine

pamene ndinali mu mzinda wozingidwa.

22Ndili mʼnkhawa zanga ndinati,

“Ine ndachotsedwa pamaso panu!”

Komabe Inu munamva kupempha chifundo kwanga

pamene ndinapempha thandizo kwa Inu.

23Kondani Yehova oyera mtima ake onse!

Yehova amasunga wokhulupirika

koma amalanga kwathunthu anthu odzikuza.

24Khalani ndi nyonga ndipo limbani mtima,

inu nonse amene mumayembekezera Yehova.