Masalimo 25 – CCL & NRT

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Masalimo 25:1-22

Salimo 25

Salimo la Davide.

1Kwa Inu Yehova, ndipereka moyo wanga.

2Ndimadalira Inu Mulungu wanga.

Musalole kuti ndichite manyazi

kapena kuti adani anga andipambane.

3Aliyense amene amayembekezera kwa Ambuye

sadzachititsidwa manyazi

koma achinyengo ndiwo adzachititsidwe manyazi

ndipo sadzakhala ndi chodzitetezera.

4Ndidziwitseni njira zanu Inu Yehova,

phunzitseni mayendedwe anu;

5tsogolereni mʼchoonadi chanu ndi kundiphunzitsa,

pakuti Inu ndinu Mulungu mpulumutsi wanga,

ndipo chiyembekezo changa chili mwa Inu tsiku lonse.

6Kumbukirani Inu Yehova chifundo ndi chikondi chanu chachikulu,

pakuti ndi zakalekale.

7Musakumbukire machimo a ubwana wanga

ndi makhalidwe anga owukira;

molingana ndi chikondi chanu ndikumbukireni ine,

pakuti Inu Yehova ndinu wabwino.

8Yehova ndi wabwino ndi wolungama;

choncho Iye akulangiza ochimwa mʼnjira yake.

9Amatsogolera odzichepetsa kuti achite zolungama

ndipo amawaphunzitsa njira zake.

10Njira zonse za Yehova ndi zachikondi ndi zokhulupirika

kwa iwo amene amasunga zofuna za pangano lake.

11Chifukwa cha dzina lanu, Inu Yehova,

khululukireni mphulupulu zanga, ngakhale kuti ndi zochuluka.

12Tsono ndani munthu amene amaopa Yehova?

Yehova adzamulangiza njira yoti ayitsate.

13Iye adzakhala pa ulemerero masiku ake onse,

ndipo zidzukulu zake zidzalandira dziko ngati cholowa chawo.

14Yehova amawulula chinsinsi chake kwa iwo amene amamuopa;

amawulula pangano lake kwa iwowo.

15Maso anga ali pa Yehova nthawi zonse,

pakuti ndi Iye yekha amene adzawonjola mapazi anga mu msampha.

16Tembenukirani kwa ine ndipo mundikomere mtima,

pakuti ndili ndekhandekha ndipo ndikuzunzika.

17Masautso a mu mtima mwanga achulukirachulukira;

masuleni ku zowawa zanga.

18Penyani mazunzo anga ndi zovuta zanga

ndipo mufafanize machimo anga onse.

19Onani mmene adani anga achulukira

ndi momwe chidani chawo ndi ine chakulira.

20Tetezani moyo wanga ndi kundilanditsa;

musalole kuti ndichite manyazi,

pakuti ndimathawira kwa Inu.

21Kukhulupirika ndi kulungama kwanga kunditeteze,

chifukwa chiyembekezo changa chili mwa Inu.

22Wombolani Israeli Inu Mulungu,

ku mavuto ake onse!

New Russian Translation

Псалтирь 25:1-12

Псалом 25

1Псалом Давида.

Господи, оправдай меня,

ведь я жил непорочной жизнью.

Я уповал на Господа,

не колеблясь.

2Проверь меня, Господи,

испытай меня,

исследуй сердце мое и разум.

3Ведь Твоя милость пред очами моими;

я всегда хожу в Твоей истине.

4Я не сижу с людьми лживыми

и с коварными не пойду.

5Я ненавижу сборище грешников

и с нечестивыми не сажусь.

6Буду омывать свои руки в невинности

и кругом обходить Твой жертвенник, Господи,

7воспевая Тебе хвалу

и говоря о всех чудесах Твоих.

8Господи, я люблю дом, в котором Ты обитаешь,

место, где слава Твоя живет.

9Не погуби души моей с грешными,

жизни моей с кровожадными,

10у которых в руках злой умысел,

чьи правые руки взяток полны.

11А я живу беспорочно.

Избавь меня и помилуй!

12Ноги мои стоят на ровной земле;

в большом собрании восхвалю я Господа.